Revised Common Lectionary (Semicontinuous)
Salimo la Davide. Kupempha.
38 Yehova musandidzudzule mutapsa mtima
kapena kundilanga muli ndi ukali.
2 Pakuti mivi yanu yandilasa,
ndipo dzanja lanu latsika ndipo landifikira.
3 Chifukwa cha ukali wanu mulibe thanzi mʼthupi langa;
mafupa anga alibe mphamvu chifukwa cha tchimo langa.
4 Kulakwa kwanga kwandipsinja
ngati katundu wolemera kwambiri kuposa mphamvu zanga.
5 Mabala anga akuwola ndipo akununkha
chifukwa cha uchitsiru wa moyo wanga wauchimo.
6 Ine ndapindika msana ndipo ndawerama kwambiri;
tsiku lonse ndimangolira.
7 Msana wanga wagwidwa ndi ululu wosasimbika,
mulibe thanzi mʼthupi langa.
8 Ndilibe mphamvu ndipo ndakunthidwa kwathunthu;
ndikubuwula ndi ululu wa mumtima.
9 Zokhumba zanga zonse zili poonekera pamaso panu Ambuye,
kusisima kwanga sikunabisike kwa Inu.
10 Mtima wanga ukugunda, mphamvu zanga zikutha;
ngakhale kuwala kwachoka mʼmaso mwanga.
11 Abwenzi anga ndi anzanga akundipewa chifukwa cha mabala anga;
anansi anga akhala kutali nane.
12 Iwo amene akufunafuna moyo wanga atchera misampha yawo,
oti andipwetekewo amayankhula za kuwonongeka kwanga;
tsiku lonse amakonza zachinyengo.
13 Ine ndili ngati munthu wosamva amene sangamve,
monga wosayankhula, amene sangathe kutsekula pakamwa pake;
14 Ndakhala ngati munthu amene samva,
amene pakamwa pake sipangathe kuyankha.
15 Ndikudikira Inu Yehova;
mudzayankha, Inu Ambuye Mulungu wanga.
16 Pakuti Ine ndinati, “Musawalole kuti akondwere
kapena kudzikweza okha pa ine pamene phazi langa laterereka.”
17 Pakuti ndili pafupi kugwa,
ndipo ndikumva kuwawa nthawi zonse.
18 Ndikuvomereza mphulupulu zanga;
ndipo ndavutika ndi tchimo langa.
19 Ambiri ndi adani anga amphamvu;
amene amandida popanda chifukwa alipo ochuluka kwambiri.
20 Iwo amene amandibwezera zoyipa mʼmalo mwa zabwino
amandinyoza pamene nditsatira zabwino.
21 Inu Yehova, musanditaye;
musakhale kutali ndi ine Mulungu wanga.
22 Bwerani msanga kudzandithandiza,
Inu Ambuye Mpulumutsi wanga.
Davide Amusiya Sauli Wosamupha
24 Sauli atabwera kuchokera kumene amathamangitsa Afilisti anamva kuti, “Davide ali mʼchipululu cha Eni Gedi.” 2 Tsono Sauli anatenga asilikali 3,000 odziwa kumenya bwino nkhondo kuchokera pakati pa Aisraeli onse ndipo anapita kukafunafuna Davide ndi anthu ake ku Matanthwe a Mbalale.
3 Iye anafika ku makola a nkhosa amene anali mʼmbali mwa njira. Kumeneko kunali phanga, ndipo Sauli analowa mʼphangamo kuti akadzithandize. Davide ndi anthu ake ankabisala mʼkati mwenimweni mwa phangalo. 4 Tsono anthu a Davide anamuwuza kuti, “Tsiku lija lafika limene Yehova anakuwuzani kuti, ‘Ndidzapereka mdani wanu mʼmanja mwanu, ndi kumuchita chimene chidzakukomereni.’ ” Koma Davide anapita mwakachetechete ndi kukadula msonga ya mkanjo wa Sauli.
5 Atachita izi, Davide anatsutsika mu mtima chifukwa anadula msonga ya mkanjo wa Sauli. 6 Tsono anawuza anthu ake kuti, “Yehova asalole kuti ndimuchite choyipa mbuye wanga, wodzozedwa wa Yehova. Ndisamupweteke pakuti ndi wodzozedwa wa Yehova.” 7 Choncho Davide anabweza mitima ya anthu ake ndi mawu amenewa, ndipo sanawalole kuti aphe Sauli. Pambuyo pake Sauli anatuluka mʼphangamo ndipo anachoka.
8 Kenaka Davide anatuluka mʼphanga muja ndipo anayitana Sauli, “Mbuye wanga!” Sauli atayangʼana mʼmbuyo, Davide anawerama ndi kugunditsa nkhope yake pansi. 9 Anafunsa Sauli kuti, “Nʼchifukwa chiyani mumamvera mawu a anthu kuti, ‘Davide wakukonzerani chiwembu?’ 10 Lero lino inu mwadzionera nokha kuti Yehova anakuperekani mʼmanja mwanga mʼphanga muja. Ena anandiwuza kuti ndikupheni, koma ndakusiyani. Ndinati, ‘Sindidzapha mbuye wanga pakuti ndiye wodzozedwa wa Yehova.’ 11 Tsono abambo anga, onanitu kansalu ka mkanjo wanu kali mʼdzanja langali! Popeza kuti ndinatha kudula msonga ya mkanjo wanu koma osakuphani, pamenepo mudziwe kuti ine ndilibe maganizo woti ndikuchiteni choyipa kapena kukuwukirani. Sindinakulakwireni ngakhale kuti inu mukufuna moyo wanga kuti mundiphe. 12 Yehova aweruze pakati pa inu ndi ine, akulangeni chifukwa cha zoyipa zimene mukundichitazi, koma dzanja langa silidzakukhudzani. 13 Paja anthu akale anati, ‘Munthu woyipa, ntchito zakenso ndi zoyipa.’ Kotero dzanja langa silidzakukhudzani.
14 “Kodi mfumu ya Israeli yadzalondola yani. Inu mukuthamangitsa yani? Galu wakufa kodi? Nsabwe kodi? 15 Nʼchifukwa chake Yehova agamule, inde aweruze pakati pa inu ndi ine ndi kupeza wolakwa. Yehova anditeteze ndi kundipulumutsa mʼdzanja lanu.”
16 Davide atatsiriza kuyankhula mawu awa, Sauli anafunsa kuti, “Kodi mawu amenewa ndi akodi mwana wanga Davide?” Sauli anayamba kulira mokweza. 17 Anawuza Davide kuti, “Ndiwe wolungama kuposa ine. Iwe wandikomera mtima pamene ine ndakuchitira zoyipa. 18 Iweyo lero lino wandifotokozera zabwino zimene wandichitira. Yehova anandipereka mʼdzanja lako koma iwe sunandiphe. 19 Kodi munthu atapeza mdani wake angamulole kuti apite wosamuvulaza? Motero Yehova akuchitire iwe zabwino chifukwa cha zimene wandichitira lerozi. 20 Ona tsono, Ine ndikudziwa kuti udzakhala mfumu ndithu ndipo ufumu wa Israeli udzakhazikika mʼmanja mwako. 21 Tsopano undilonjeze molumbira lero mʼdzina la Yehova kuti sudzapha zidzukulu zanga ine nditamwalira kapena kufuta dzina langa pa banja la makolo anga.”
22 Choncho Davide analumbira pamaso pa Sauli. Pambuyo pake Sauli anabwerera kwawo, koma Davide ndi anthu ake anapitanso ku phanga kuja.
Mgonero wa Ambuye
17 Koma popereka malangizo awa sindikufuna kukuyamikirani popeza mʼmisonkhano yanu mumachita zoyipa kuposa zabwino. 18 Choyamba, ndikumva kuti mukasonkhana mu mpingo mumasankhana ndipo ndikukhulupirira kuti zimenezi kwinaku nʼzoona. 19 Nʼzosakayikitsa kuti pali kugawikana pakati panu kuti adziwike amene ndi ovomerezeka ndi Mulungu. 20 Tsono, mukasonkhana pamodzi, chimene mumadya si Mgonero wa Ambuye. 21 Pakuti mukamadya, aliyense amangodzidyera zomwe anakonza. Wina amakhala ndi njala pamene wina amaledzera. 22 Kodi mulibe nyumba zanu kumene mungamadyere ndi kumwa? Kapena mumapeputsa mpingo wa Mulungu ndi kuchititsa manyazi amene alibe kalikonse? Ndikunena chiyani kwa inu? Moti ndikuyamikireni pa zimenezi? Ayi, pa zinthu izi sindingakuyamikireni.
27 Chifukwa chake, aliyense amene adya buledi kapena kumwa chikho cha Ambuye mʼnjira yosayenera adzachimwira thupi ndi magazi a Ambuye. 28 Munthu adzisanthule yekha asanadye buledi kapena kumwa chikhochi. 29 Popeza aliyense amene adya kapena kumwa mosazindikira thupi la Ambuye, amadya ndi kumwa chiweruzo chake chomwe. 30 Nʼchifukwa chake pakati panu ambiri mwa inu ndi ofowoka ndi odwala, ndipo ambirinso agona tulo. 31 Koma tikanadziyesa tokha sitikaweruzidwanso. 32 Pamene tiweruzidwa ndi Ambuye, ndiye kuti akukonza khalidwe lathu kupewa kuti tingatsutsidwe pamodzi ndi anthu osakhulupirira.
33 Ndiye tsono abale anga, pamene musonkhana pa chakudya, mudikirirane.
The Word of God in Contemporary Chichewa Copyright © 2002, 2016 by Biblica, Inc.® Used by permission of Biblica, Inc.® All rights reserved worldwide. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Mwini © 2002, 2016 ndi Biblica, Inc.® Kugwiritsa ntchito mwachilolezo. Umwini ndi otetezedwa pa dziko lonse.