Revised Common Lectionary (Semicontinuous)
Nyimbo yoyimba pokwera ku Yerusalemu.
120 Ndimafuwulira kwa Yehova mʼmasautso anga,
ndipo Iye amandiyankha.
2 Pulumutseni Yehova ku milomo yabodza,
ndi kwa anthu achinyengo.
3 Kodi adzakuchitani chiyani,
ndipo adzawonjezerapo zotani, inu anthu achinyengo?
4 Adzakulangani ndi mivi yakuthwa ya munthu wankhondo,
ndi makala oyaka a mtengo wa tsanya.
5 Tsoka ine kuti ndimakhala ku Mesaki,
kuti ndimakhala pakati pa matenti a ku Kedara!
6 Kwa nthawi yayitali ndakhala pakati
pa iwo amene amadana ndi mtendere.
7 Ine ndine munthu wamtendere;
koma ndikamayankhula, iwo amafuna nkhondo.
Koresi Athandiza Ayuda Kubwerera Kwawo
1 Mʼchaka choyamba cha ufumu wa Koresi mfumu ya Perisiya, pofuna kukwaniritsa zimene anayankhula kudzera mwa Yeremiya, Yehova anayika maganizo mu mtima mwa Koresi mfumu ya Perisiya kuti alengeze mʼdziko lake lonse ndi mawu apakamwa ngakhalenso ochita kulemba.
2 Iye anati, “Koresi mfumu ya Perisiya ikunena kuti,
“ ‘Yehova, Mulungu wakumwamba wandipatsa maufumu onse a dziko lapansi, ndipo wandipatsa udindo woti ndimumangire Nyumba ku Yerusalemu mʼdziko la Yuda. 3 Aliyense wa inu amene ali wa Yehova, Mulungu wakeyo akhale naye. Tsono aliyense wa inu apite ku Yerusalemu, mʼdziko la Yuda kuti akamange Nyumba ya Yehova, Mulungu wa Israeli. Iyeyu ndi Mulungu amene ali mu Yerusalemu. 4 Ndipo kumalo kulikonse kumene otsalawo akukhala, athandizidwe ndi eni dzikolo powapatsa siliva, golide, katundu ndi ziweto ndi zopereka za ufulu zoti akapereke ku Nyumba ya Yehova imene ili ku Yerusalemu.’ ”
5 Choncho atsogoleri a mabanja afuko la Yuda ndi la Benjamini komanso ansembe ndi Alevi, aliyense amene Mulungu anawutsa mtima wake, anayamba kukonzeka kupita kukamanga Nyumba ya Yehova imene ili ku Yerusalemu. 6 Onse oyandikana nawo anawathandiza powapatsa ziwiya za siliva ndi zagolide, kuphatikizaponso katundu ndi ziweto, ndiponso mphatso zamtengo wapatali, kuwonjezera pa zopereka zaufulu zija. 7 Nayenso mfumu Koresi anatulutsa ziwiya za mʼNyumba ya Yehova zimene Nebukadinezara anazitenga kuzichotsa ku Yerusalemu ndi kuziyika mʼnyumba ya milungu yake. 8 Koresi, mfumu ya ku Perisiya inatulutsa ziwiyazi ndi kuzipereka kwa Miteridati, msungichuma amene anaziwerenga pamaso pa Sesibazara nduna yayikulu ya dziko la Yuda.
9 Chiwerengerochi chinali motere:
Mabeseni agolide | 30 |
mabeseni asiliva | 1,000 |
a zopereka | 29 |
10 timiphika tagolide | 230 |
timiphika tasiliva | 410 |
ziwiya zina | 1,000. |
11 Ziwiya zonse zagolide ndi siliva pamodzi zinalipo 5,400. Zonsezi ndi zimene Sezi-Bazara anabwera nazo pamene otengedwa ukapolo aja ankabwerera ku Yerusalemu kuchokera ku Babuloni.
Paulo Afotokoza za Kusintha kwa Ulendo Wake
12 Tsono chonyadira chathu nʼchakuti, chikumbumtima chathu chimatitsimikizira kuti timakhala bwino mʼdziko lapansi, makamaka pa ubale wathu ndi inu. Takhala moona mtima ndi oyera mtima. Sitinachite chomwechi mwa nzeru ya dziko lapansi koma monga mwa chisomo cha Mulungu. 13 Pakuti sitikukulemberani zoti simungawerenge kapena kumvetsetsa. 14 Monga mwamva pangʼono chabe, ndikuyembekeza kuti mudzamvetsa kwenikweni, kuti mutha kutinyadira monga ife tidzakunyadirani, pa tsiku la Ambuye Yesu.
15 Popeza ndinatsimikiza mtima za ichi, nʼchifukwa chake ndinafuna kuti poyamba, ndidzakuchezereni kuti mupindule pawiri. 16 Ndinafuna kuti ndidzakuchezereni pa ulendo wanga wopita ku Makedoniya ndi kudzakuonaninso pochokera ku Makedoniyako kuti inu mudzandithandize pa ulendo wanga wopita ku Yudeya. 17 Kodi pamene ndinkakonzekera zimenezi, mukuganiza kuti ndinkachita mwachibwana? Kapena kuti ndinkaganiza ngati mwa dziko lapansi; kuti ndikhoza kumanena kuti, “Inde, Inde,” nthawi yomweyo nʼkumatinso “Ayi, Ayi?”
18 Koma zoona monga Mulungu ali wokhulupirika, uthenga wathu kwa inu siwakuti, “Inde” nʼkutinso “Ayi.” 19 Pakuti Yesu Khristu mwana wa Mulungu amene ine, Silivano ndi Timoteyo tinamulalikira pakati panu sali “Inde” yemweyonso “Ayi.” Koma nthawi zonse mwa Iye muli “Inde.”
The Word of God in Contemporary Chichewa Copyright © 2002, 2016 by Biblica, Inc.® Used by permission of Biblica, Inc.® All rights reserved worldwide. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Mwini © 2002, 2016 ndi Biblica, Inc.® Kugwiritsa ntchito mwachilolezo. Umwini ndi otetezedwa pa dziko lonse.