Revised Common Lectionary (Semicontinuous)
Salimo la Davide.
37 Usamavutike chifukwa cha anthu oyipa
kapena kuchitira nsanje amene akuchita cholakwa;
2 pakuti monga udzu iwo adzafota msanga,
ngati mbewu zobiriwira adzanyala msanga.
3 Khulupirira Yehova ndipo uzichita zabwino;
khazikika mʼdziko ndi kutsata zokhulupirika.
4 Udzikondweretse wekha mwa Yehova
ndipo Iye adzakupatsa zokhumba za mtima wako.
5 Pereka njira yako kwa Yehova;
dalira Iye ndipo Iyeyo adzachita izi:
6 Iye adzachititsa chilungamo chako kuwala ngati mʼbandakucha,
chiweruzo chako ngati dzuwa la masana.
7 Khala chete pamaso pa Yehova ndipo umudikire mofatsa;
usavutike pamene anthu apambana mʼnjira zawo,
pamene iwo achita zinthu zawo zoyipa.
8 Pewa kupsa mtima ndipo tembenuka kuchoka ku ukali,
usavutike chifukwa zimenezi zimatsogolera ku zoyipa.
9 Pakuti anthu oyipa adzachotsedwa,
koma iwo amene amayembekeza mwa Yehova adzalandira dziko.
10 Kwa kanthawi oyipa sadzapezekanso;
ngakhale muwafunefune, sadzapezekanso.
11 Koma ofatsa adzalandira dziko
ndipo adzasangalala ndi mtendere waukulu.
39 Chipulumutso cha olungama chimachokera kwa Yehova;
Iye ndiye linga lawo pa nthawi ya masautso.
40 Yehova amawathandiza ndi kuwalanditsa;
Iye amawalanditsa kwa oyipa ndi kuwapulumutsa,
pakuti amathawira kwa Iye.
Chikho Chasiliva Mʼthumba la Benjamini
44 Pambuyo pake Yosefe analamulira wantchito wa mʼnyumba mwake kuti, “Adzazire chakudya anthuwa mʼmatumba mwawo monga mmene anganyamulire, ndipo uwayikire ndalama zawo pakamwa pa matumba awowo. 2 Tsono uyike chikho changa cha siliva chija, pakamwa pa thumba la wamngʼono kwambiriyu pamodzi ndi ndalama zake za chakudya” Ndipo iye anachita monga Yosefe ananenera.
3 Mmawa kutacha anthu aja analoledwa kuti apite ndi abulu awo. 4 Atangotuluka mu mzinda muja, koma asanapite patali, Yosefe anati kwa wantchito wake, “Nyamuka atsatire anthu aja msanga. Ndipo ukawapeza, uwafunse kuti, ‘Bwanji mwabwezera zoyipa ndi zabwino? 5 Mwaberanji chikho chimene mbuye wanga amamweramo ndi kugwiritsa ntchito akafuna kuwombeza? Chimene mwachitachi ndi chinthu choyipa.’ ”
6 Wantchito uja atawapeza ananena mawu anawuzidwa aja. 7 Koma iwo anati kwa iye, “Kodi mbuye wanga mukuneneranji zimenezi? Sizingatheke ndi pangʼono pomwe kuti antchito anufe nʼkuchita zoterozo ayi! 8 Paja ife pobwera kuchokera ku Kanaani tinatenga ndalama kubwezera zimene tinazipeza mʼmatumba mwathu. Ndiye pali chifukwa chanji kuti tikabe siliva kapena golide mʼnyumba mwa mbuye wanu? 9 Ngati wantchito wanu wina pano atapezeka nacho chikhocho, ameneyo aphedwe ndipo ena tonsefe tidzakhala akapolo anu, mbuye wathu.”
10 Iye anati, “Chabwino, tsono zikhale monga mwaneneramu. Komatu aliyense amene angapezeke nacho chikhocho adzakhala kapolo wanga, ndipo ena nonsenu muzipita mwaufulu.”
11 Tsono onse anafulumira kutsitsa pansi aliyense thumba lake ndi kulitsekula. 12 Kenaka anayamba kufufuza, kuyambira pa wamkulu mpaka pa wamngʼono. Ndipo chikhocho chinapezeka mʼthumba mwa Benjamini. 13 Apo onse anangʼamba zovala zawo ndi chisoni. Ndipo anasenzetsa abulu katundu wawo nabwerera ku mzinda konkuja.
14 Pamene Yuda ndi abale ake ankafika ku nyumba kwa Yosefe nʼkuti Yosefe akanali komweko. Ndipo anadzigwetsa pansi pamaso pake. 15 Yosefe anafunsa kuti, “Nʼchiyani mwachitachi? Kodi simudziwa kuti munthu ngati ine ndikhoza kuona zinthu mwakuwombeza?”
16 Yuda anayankha, “Kodi tinganenenji kwa mbuye wanga? Tinena chiyani? Tingadzilungamitse bwanji? Mulungu waulula kulakwa kwa antchito anu. Ndipo tsopano ndife akapolo a mbuye wanga, ife tonse pamodzi ndi amene wapezeka ndi chikhocho.”
17 Koma Yosefe anati, “Sindingachite choncho ayi! Yekhayo amene wapezeka ndi chikhocho ndi amene akhale kapolo wanga. Ena nonsenu, bwererani kwa abambo anu mu mtendere.”
12 Inu ana okondedwa, ndikukulemberani
popeza kuti machimo anu akhululukidwa chifukwa cha dzina la Yesu.
13 Inu abambo, ndikukulemberani
popeza kuti munamudziwa Iye amene analipo kuyambira pachiyambi.
Inu anyamata, ndikukulemberani
popeza kuti munagonjetsa woyipayo.
14 Ana okondedwa, ndikukulemberani
chifukwa mumawadziwa Atate.
Abambo, ndikukulemberani
chifukwa munamudziwa Iye amene analipo kuyambira pachiyambi.
Inu anyamata, ndikukulemberani
chifukwa ndinu amphamvu.
Mawu a Mulungu amakhala mwa inu
ndipo mumamugonjetsa woyipayo.
Musakonde Dziko Lapansi
15 Musamakonde dziko lapansi kapena chilichonse cha dziko lapansi. Ngati munthu wina aliyense akonda dziko lapansi, mwa iyeyo mulibe chikondi chokonda Atate. 16 Pakuti zonse za mʼdziko lapansi, zilakolako za thupi, zinthu zimene maso amakhumbira ndiponso kuyandikira zinthu za moyo uno, zonsezi sizichokera kwa Atate, koma ku dziko lapansi. 17 Dziko lapansi likupita pamodzi ndi zilakolako zake, koma amene amachita chifuniro cha Mulungu amakhalapo mpaka muyaya.
The Word of God in Contemporary Chichewa Copyright © 2002, 2016 by Biblica, Inc.® Used by permission of Biblica, Inc.® All rights reserved worldwide. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Mwini © 2002, 2016 ndi Biblica, Inc.® Kugwiritsa ntchito mwachilolezo. Umwini ndi otetezedwa pa dziko lonse.