Print Page Options
Previous Prev Day Next DayNext

Revised Common Lectionary (Semicontinuous)

Daily Bible readings that follow the church liturgical year, with sequential stories told across multiple weeks.
Duration: 1245 days
Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero (CCL)
Version
Yesaya 6:1-8

Masomphenya a Yesaya

Chaka chimene mfumu Uziya anamwalira, ndinaona Ambuye atakhala pa mpando waufumu, wautali ndi wokwezedwa, ndipo mkanjo wawo unali wautali; kotero kuti unadzaza mʼNyumba ya Yehova. Pamwamba pawo panayimirira Aserafi, aliyense anali ndi mapiko asanu ndi limodzi: awiri anaphimba nkhope zawo, awiri anaphimba mapazi awo, ndipo awiri ankawulukira. Ndipo Aserafiwo amafuwulirana kuti

“Woyera, woyera, woyera Yehova Wamphamvuzonse.
    Dziko lonse lapansi ladzaza ndi ulemerero wake.”

Chifukwa cha kufuwulako maziko a zitseko ndi ziwundo anagwedezeka ndipo mʼNyumba ya Yehova munadzaza utsi.

Tsono ine ndinafuwula kuti, “Tsoka langa ine! Ndatayika! Pakuti ndine munthu wapakamwa poyipa, ndipo ndimakhala pakati pa anthu a pakamwa poyipa, ndipo ndi maso anga ndaona mfumu Yehova Wamphamvuzonse.”

Pomwepo mmodzi mwa Aserafi aja anawulukira kwa ine ali ndi khala lamoto mʼdzanja lake, khala limene analichotsa ndi mbaniro pa guwa lansembe. Ndipo anandikhudza pakamwa panga ndi khala lamotolo nati, “Taona ndakhudza pa milomo yako ndi khalali; kulakwa kwako kwachotsedwa, machimo ako akhululukidwa.”

Kenaka ndinamva mawu a Ambuye akuti, “Kodi ndidzatuma yani? Ndipo ndani adzapite mʼmalo mwathu?”

Ndipo ine ndinati, “Ndilipo. Tumeni!”

Yesaya 6:9-13

Yehova anati, “Pita ndipo ukawawuze anthu awa:

“ ‘Kumva muzimva, koma osamvetsetsa;
    kupenya muzipenya koma osaona kanthu.’
10 Tsono anthu amenewa uwaphe mtima;
    uwagonthetse makutu,
    ndipo uwatseke mʼmaso.
Mwina angaone ndi maso awo,
    angamve ndi makutu awo,
    angamvetse ndi mitima yawo,
kenaka ndi kutembenuka mtima ndi kuchiritsidwa.”

11 Pamenepo ine ndinati, “Zimenezo ndi mpaka liti Inu Ambuye?”

Ndipo Iyeyo anandiyankha kuti,

“Mpaka mizinda itasanduka mabwinja
    nʼkusowa wokhalamo,
mpaka nyumba zitasowa anthu okhalamo,
    mpaka dziko litasanduka chipululu ndithu,
12 mpaka Yehova atasamutsira aliyense kutali,
    dziko nʼkusiyidwa kwathunthu.
13 Ndipo ngakhale chigawo chakhumi cha anthu chitatsala mʼdziko,
    nachonso chidzawonongedwa.
Koma monga momwe mitengo ya muwanga ndi thundu
    imasiyira chitsa pamene ayidula,
    chonchonso mbewu yoyera idzatsalira ngati chitsa chotsala mʼdziko.”

Masalimo 138

Salimo la Davide.

138 Ndidzakuyamikani Yehova ndi mtima wanga wonse;
    ndidzayimba nyimbo zokutamandani pamaso pa “milungu.”
Ndidzagwada kuyangʼana ku Nyumba yanu yoyera
    ndipo ndidzayamika dzina lanu
    chifukwa cha chikondi chanu ndi kukhulupirika kwanu,
pakuti Inu mwakuza dzina lanu ndi mawu anu
    kupambana zinthu zonse.
Pamene ndinayitana, munandiyankha;
    munandisandutsa wamphamvu ndi wolimba mtima.

Mafumu onse a dziko lapansi akuyamikeni Yehova,
    pamene amva mawu a pakamwa panu.
Iwo ayimbe za njira za Yehova,
    pakuti ulemerero wa Yehova ndi waukulu.

Ngakhale kuti Yehova ngokwezeka, amasamalira odzichepetsa,
    koma anthu onyada amawadziwira chapatali.
Ngakhale ndiyende pakati pa masautso,
    mumasunga moyo wanga;
mumatambasula dzanja lanu kutsutsana ndi mkwiyo wa adani anga,
    mumandipulumutsa ndi dzanja lanu lamanja.
Yehova adzakwaniritsa cholinga chake pa ine;
    chikondi chanu chosasinthika Yehova, ndi chosatha
    musasiye ntchito ya manja anu.

1 Akorinto 15:1-11

Za Kuuka kwa Khristu

15 Tsono abale, ndikufuna ndikukumbutseni za Uthenga Wabwino umene ndinakulalikirani. Munawulandira ndipo munawukhulupirira kolimba. Inu munapulumutsidwa ndi Uthenga Wabwinowu, ngati mwasunga mawu amene ndinakulalikirani. Kupanda kutero, mwangokhulupirira pachabe.

Pakuti chimene ndinalandira ndinapereka kwa inu monga chofunika kuposa zonse, kuti Khristu anafera zoyipa zathu monga mwa Malemba, kuti anayikidwa mʼmanda, kuti anaukitsidwa tsiku lachitatu monga mwa Malemba; ndipo kuti anaonekera kwa Petro, ndipo kenaka kwa Atumwi khumi ndi awiriwo. Pambuyo pake, Iye anaonekera kwa anthu oposa 500 mwa abale pa nthawi imodzi, ndipo ambiri mwa iwo akanali ndi moyo ngakhale kuti ena anagona tulo. Kenaka anaonekeranso kwa Yakobo, kenaka kwa atumwi onse. Potsiriza pa onse anaonekeranso kwa ine, monga mwana wobadwa nthawi isanakwane.

Pakuti ine ndine wamngʼono kwa atumwi ndipo sindiyenera nʼkomwe kutchedwa mtumwi chifukwa ndinazunza mpingo wa Mulungu. 10 Koma mwachisomo cha Mulungu, ndili mmene ndililimu, ndipo chisomo chake kwa ine sichinali chopanda ntchito. Ndinagwira ntchito kuposa ena onse a iwo. Choncho sindine koma chisomo cha Mulungu chimene chinali ndi ine. 11 Tsono kaya ndi ineyo kapena iwowo, izi ndi zomwe timalalikira, ndipo izi ndi zimene munakhulupirira.

Luka 5:1-11

Yesu Ayitana Ophunzira Oyamba

Tsiku lina Yesu anayima mʼmbali mwa nyanja ya Genesareti, gulu la anthu litamuzungulira likumvetsera mawu a Mulungu. Iye anaona mabwato awiri ali mʼmphepete mwa nyanja, asodzi amene ankachapa makhoka awo atawasiya pamenepo. Iye analowa mʼbwato limodzi limene linali la Simoni, ndi kumupempha kuti alikankhire mʼkati mwa nyanja pangʼono. Kenaka Iye anakhala pansi nayamba kuphunzitsa anthu ali mʼbwatomo.

Atatha kuyankhula anati kwa Simoni, “Kankhirani kwa kuya ndipo muponye makhoka kuti mugwire nsomba.”

Simoni anayankha kuti, “Ambuye, tagwira ntchito molimbika usiku wonse, koma sitinagwire kanthu. Koma pakuti mwatero, ndiponya makhoka.”

Atachita izi, anagwira nsomba zambiri kotero kuti makhoka awo anayamba kungʼambika. Choncho anakodola anzawo a bwato linalo kuti abwere ndi kuwathandiza, ndipo anabwera nadzaza mabwato onse awiri mpaka kuyamba kumira.

Simoni Petro ataona izi, anagwa pa mawondo a Yesu nati, “Chokani kwa ine Ambuye: Ine ndine munthu wochimwa!” Iye ndi anzake onse anadabwa ndi nsomba zimene anagwira, 10 chimodzimodzinso Yakobo ndi Yohane, ana a Zebedayo, anzake a Simoniyo.

Kenaka Yesu anati kwa Simoni, “Musachite mantha; kuyambira tsopano ndidzakusandutsani asodzi a anthu.” 11 Kenaka anakokera mabwato awo ku mtunda, nasiya zonse namutsata Iye.

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero (CCL)

The Word of God in Contemporary Chichewa Copyright © 2002, 2016 by Biblica, Inc.® Used by permission of Biblica, Inc.® All rights reserved worldwide. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Mwini © 2002, 2016 ndi Biblica, Inc.® Kugwiritsa ntchito mwachilolezo. Umwini ndi otetezedwa pa dziko lonse.