Revised Common Lectionary (Semicontinuous)
Kwa mtsogoleri wa mayimbidwe. Salimo la Davide.
20 Yehova akuyankhe pamene uli pa msautso;
dzina la Mulungu wa Yakobo likuteteze.
2 Iye atumize thandizo kuchokera ku malo ake opatulika;
akugwirizize kuchokera ku Ziyoni.
3 Iye akumbukire nsembe zako zonse
ndipo alandire nsembe zako zopsereza.
Sela
4 Akupatse chokhumba cha mtima wako
ndipo akuthandize kuti zonse wakonza zichitike.
5 Ife tidzafuwula ndi chimwemwe pamene iwe wapambana
ndipo tidzanyamula mbendera zathu mʼdzina la Mulungu wathu,
Yehova ayankhe zopempha zako zonse.
6 Tsopano ndadziwa kuti Yehova amapulumutsa wodzozedwa wake;
Iye amamuyankha kuchokera kumwamba ku malo ake opatulika
ndi mphamvu yopulumutsa ya dzanja lake lamanja.
7 Ena amadalira magaleta ndipo ena akavalo
koma ife tidzadalira dzina la Yehova Mulungu wathu.
8 Iwo amagonjetsedwa ndi kugwa,
koma ife timadzuka ndi kuyima chilili.
9 Inu Yehova, pulumutsani mfumu!
Tiyankheni pamene tikuyitanani!
Zopereka Zomangira Chihema
25 Yehova ananena kwa Mose kuti, 2 “Uza Aisraeli kuti abweretse chopereka kwa Ine. Iwe ulandire choperekacho mʼmalo mwanga kuchokera kwa munthu amene akupereka mwakufuna kwake. 3 Zopereka zimene ulandire kwa anthuwo ndi izi: Golide, siliva ndi mkuwa. 4 Nsalu zobiriwira, zapepo, zofiira, nsalu zofewa, ubweya wambuzi; 5 zikopa za nkhosa zazimuna za utoto wofiira ndi zikopa za akatumbu; matabwa amtengo wa mkesha; 6 mafuta anyale a olivi, zonunkhiritsa mafuta odzozera ndi zopangira lubani wonunkhira; 7 miyala yokongola ya mtundu wa onikisi ndi ina yabwino yoyika pa efodi ndi pa chovala cha pachifuwa.
8 “Iwo andipangire malo wopatulika, ndipo Ine ndidzakhala pakati pawo. 9 Umange chihema ndiponso ziwiya zamʼkatimo monga momwe Ine ndidzakuonetsere.
Bokosi la Chipangano
10 “Tsono apange bokosi lamatabwa amtengo wa mkesha, ndipo kutalika kwake kukhale masentimita 114, mulifupi mwake masentimita 69, msinkhu wake masentimita 69. 11 Bokosilo ulikute ndi golide wabwino kwambiri, mʼkati mwake ndi kunja komwe, ndipo upange mkombero wagolide kuzungulira bokosilo. 12 Upange mphete zinayi zagolide ndipo uzimangirire ku miyendo yake inayi ya bokosilo, mbali ina ziwiri ndi mbali inanso ziwiri. 13 Kenaka upange mizati yamtengo wa mkesha ndi kuzikuta ndi golide. 14 Ndipo ulowetse nsichizo mʼmphete zija za mbali zonse ziwiri za bokosilo kuti azinyamulira. 15 Nsichizo zizikhala mʼmphete za bokosilo nthawi zonse, zisamachotsedwe. 16 Ndipo udzayike mʼbokosilo miyala iwiri yolembedwapo malamulo imene Ine ndidzakupatse.
17 “Upange chivundikiro cha bokosilo cha golide wabwino kwambiri, kutalika kwake masentimita 114, mulifupi mwake masentimita 69. 18 Ndipo upange Akerubi awiri agolide osula ndi nyundo, uwayike mbali ziwiri za chivundikirocho, 19 kerubi mmodzi mbali ina ndi wina mbali inayo. Akerubiwa uwapangire limodzi ndi chivundikirocho mʼmapeto mwa mbali ziwirizo. 20 Mapiko a Akerubiwo adzatambasukire pamwamba pa chivundikiro cha bokosilo kuti achiphimbe. Akerubiwo adzakhale choyangʼanana, aliyense kuyangʼana chivundikirocho. 21 Uyike chivundikirocho pamwamba pa bokosi ndipo mʼbokosilo uyikemo miyala ya malamulo, imene ndidzakupatse. 22 Ndizidzakumana nawe pamenepo, pamwamba pa chivundikiro cha bokosilo, pakati pa Akerubi awiriwo, ndikumadzakupatsa malamulo onse okhudzana ndi Aisraeli.
2 Pamene ndinabwera kwa inu, abale, sindinabwere ndi luntha lodziwa kuyankhula kapena nzeru zapamwamba pamene ndinachitira umboni chinsinsi cha Mulungu. 2 Pakuti ndinatsimikiza pamene ndinali ndi inu kuti ndisadziwe kanthu kena kupatula Yesu Khristu wopachikidwayo. 3 Ndinabwera kwa inu wofowoka ndi wamantha, ndiponso wonjenjemera kwambiri. 4 Uthenga ndi ulaliki wanga sunali wa mawu anzeru ndi onyengerera koma woonetsa mphamvu za Mzimu, 5 kuti chikhulupiriro chanu chisatsamire pa nzeru ya anthu koma pa mphamvu za Mulungu.
Nzeru Yochokera kwa Mzimu
6 Komabe ife timayankhula uthenga wa nzeru kwa okhwima, koma osati ndi nzeru ya mʼbado uno kapena ya olamula a mʼbado uno, amene mphamvu yawo ikutha. 7 Ayi, ife timayankhula za nzeru yobisika ya Mulungu, nzeru imene inabisidwa ndipo imene Mulungu anatikonzera mu ulemerero wathu isanayambe nthawi. 8 Palibe olamulira aliyense wa mʼbado uno amene anamumvetsetsa popeza anakamumvetsetsa sakanamupachika Ambuye wa ulemerero. 9 Komabe monga zalembedwa kuti,
“Palibe diso linaona,
palibe khutu linamva,
palibe amene anaganizira,
zimene Mulungu anakonzera amene amukonda”
10 koma Mulungu waululira ife mwa Mzimu wake.
Mzimu amafufuza zinthu zonse, ndi zozama za Mulungu zomwe.
The Word of God in Contemporary Chichewa Copyright © 2002, 2016 by Biblica, Inc.® Used by permission of Biblica, Inc.® All rights reserved worldwide. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Mwini © 2002, 2016 ndi Biblica, Inc.® Kugwiritsa ntchito mwachilolezo. Umwini ndi otetezedwa pa dziko lonse.