Revised Common Lectionary (Semicontinuous)
Kwa mtsogoleri wa mayimbidwe. Salimo la ana a Kora.
47 Ombani mʼmanja, inu anthu onse;
fuwulani kwa Mulungu ndi mawu achimwemwe.
2 Ndi woopsadi Yehova Wammwambamwamba;
Mfumu yayikulu ya dziko lonse lapansi!
3 Iye anatigonjetsera mitundu yambirimbiri ya anthu;
anayika anthu pansi pa mapazi athu.
4 Iye anatisankhira cholowa chathu,
chonyaditsa cha Yakobo, amene anamukonda.
Sela
5 Mulungu wakwera, anthu akumufuwulira mwachimwemwe,
Yehova wakwera, akumuyimbira malipenga.
6 Imbani matamando kwa Mulungu, imbani matamando;
imbani matamando kwa mfumu yathu, imbani matamando.
7 Pakuti Mulungu ndi mfumu ya dziko lonse lapansi;
imbirani Iye salimo la matamando.
8 Mulungu akulamulira mitundu ya anthu;
Mulungu wakhala pa mpando wake waufumu woyera.
9 Anthu otchuka mwa anthu a mitundu ina asonkhana
monga anthu a Mulungu wa Abrahamu,
pakuti mafumu a dziko lapansi ndi ake a Mulungu;
Iye wakwezedwa kwakukulu.
15 Mose atakwera ku phiri kuja mtambo unaphimba phirilo. 16 Ulemerero wa Yehova unakhala pa phiri la Sinai, ndipo mtambo unaphimba phirilo kwa masiku asanu ndi limodzi. Pa tsiku lachisanu ndi chiwiri Yehova anayitana Mose kuchokera mu mtambowo. 17 Ulemerero wa Yehova uja unkaoneka ngati malawi a moto pamwamba pa phirilo. 18 Ndipo Mose analowa mʼmitambo nakwera phiri. Iye anakhala ku phiriko 40 usana ndi usiku.
Wina Wokhala ngati Mwana wa Munthu
9 Ine Yohane mʼbale wanu ndi mnzanu mʼmasautso ndi mu ufumu ndi mukupirira kwambiri, zomwe ndi zathu mwa Yesu, ndinali pa chilumba cha Patimo chifukwa cha Mawu a Mulungu ndi umboni wa Yesu. 10 Pa tsiku la Ambuye ndinanyamulidwa ndi Mzimu ndipo ndinamva kumbuyo kwanga mawu ofuwula ngati lipenga, 11 amene anati, “Lemba mʼbuku zimene ukuziona ndipo uzitumize ku mipingo isanu ndi iwiri ya ku Efeso, Simurna, Pergamo, Tiyatira, Sarde, Filadefiya ndi ku Laodikaya.”
12 Nditatembenuka kuti ndione amene amandiyankhulayo, ndinaona zoyikapo nyale zisanu ndi ziwiri zagolide. 13 Pakati pa zoyikapo nyalezo ndinaona wina wooneka ngati Mwana wa Munthu atavala mkanjo wofika kumapazi ake ndipo anamangirira lamba wagolide pa chifuwa pake. 14 Tsitsi lake linali loyera ngati thonje, kuyera ngati matalala, ndipo maso ake amawala ngati malawi amoto. 15 Mapazi ake anali ngati chitsulo choti chili mʼngʼanjo yamoto, ndipo mawu ake anali ngati mkokomo wamadzi othamanga. 16 Mʼdzanja lake lamanja ananyamula nyenyezi zisanu ndi ziwiri, ndipo mʼkamwa mwake munali lupanga lakuthwa konsekonse. Nkhope yake imawala ngati dzuwa lowala kwambiri.
17 Nditamuona ndinagwa pa mapazi ake ngati wakufa. Kenaka Iye anasanjika dzanja lake lamanja pa ine nati, “Usachite mantha. Ndine Woyamba ndi Wotsiriza. 18 Ine ndine Wamoyo; ndinali wakufa ndipo taona ndine wamoyo mpaka muyaya! Ndipo ndili ndi makiyi a imfa ndi Hade.
The Word of God in Contemporary Chichewa Copyright © 2002, 2016 by Biblica, Inc.® Used by permission of Biblica, Inc.® All rights reserved worldwide. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Mwini © 2002, 2016 ndi Biblica, Inc.® Kugwiritsa ntchito mwachilolezo. Umwini ndi otetezedwa pa dziko lonse.