Print Page Options
Previous Prev Day Next DayNext

Revised Common Lectionary (Semicontinuous)

Daily Bible readings that follow the church liturgical year, with sequential stories told across multiple weeks.
Duration: 1245 days
Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero (CCL)
Version
Masalimo 29

Salimo la Davide.

29 Perekani kwa Yehova, inu anthu amphamvu,
    perekani kwa Yehova ulemerero ndi mphamvu.
Perekani kwa Yehova ulemerero woyenera dzina lake,
    pembedzani Yehova mwa kukongola kwa chiyero chake.

Liwu la Yehova lili pamwamba pa madzi;
    Mulungu waulemerero abangula,
    Yehova abangula pamwamba pa madzi amphamvu.
Liwu la Yehova ndi lamphamvu;
    liwu la Yehova ndi laulemerero.
Liwu la Yehova limathyola mikungudza;
    Yehova amathyolathyola mikungudza ya ku Lebanoni.
Iye amachititsa Lebanoni kulumphalumpha ngati mwana wangʼombe,
    Siriyoni ngati mwana wa njati:
Liwu la Yehova limakantha
    ngati kungʼanima kwa mphenzi.
Liwu la Yehova limagwedeza chipululu;
    Yehova amagwedeza chipululu cha Kadesi.
Liwu la Yehova limapindapinda mibawa
    ndi kuyeretsa nkhalango.
Ndipo mʼNyumba mwake onse amafuwula kuti, “Ulemerero!”

10 Yehova amakhala pamwamba pa madzi osefukira,
    Yehova ndiye mfumu kwamuyaya.
11 Yehova amapereka mphamvu kwa anthu ake;
    Yehova amadalitsa anthu ake ndi mtendere.

Yesaya 2:1-5

Phiri la Yehova

Nazi zinthu zokhudza Yuda ndi Yerusalemu, zimene Yesaya mwana wa Amozi anaziona mʼmasomphenya:

Mʼmasiku otsiriza,

phiri la Nyumba ya Yehova adzalikhazikitsa
    kukhala lalitali kuposa mapiri ena onse,
lidzaonekera pamwamba pa mapiri ena onse,
    ndipo mayiko onse adzathamangira kumeneko.

Anthu ambiri adzabwera ndikunena kuti,

“Tiyeni tikwere ku phiri la Yehova,
    ku nyumba ya Mulungu wa Yakobo.
Iye adzatiphunzitsa njira zake,
    ndipo tidzayenda mʼnjira zakezo.”
Malangizo adzachokera ku Ziyoni,
    mawu a Yehova adzachokera ku Yerusalemu.
Iye adzaweruza pakati pa mayiko,
    ndipo adzathetsa kusamvana pakati pa anthu ambiri.
Anthuwo adzasandutsa malupanga awo kukhala makasu
    ndiponso mikondo yawo kukhala zomwetera.
Mtundu wina sudzatenganso lupanga kumenyana ndi mtundu wina,
    kapena kuphunziranso za nkhondo.

Inu nyumba ya Yakobo, bwerani,
    tiyeni tiyende mʼkuwala kwa Yehova.

Aroma 8:9-11

Koma inu simulamulidwanso ndi khalidwe lanu lauchimo koma ndi Mzimu ngati Mzimu wa Mulungu akhaladi mwa inu. Koma ngati munthu aliyense alibe Mzimu wa Khristu, iyeyu si wa Khristu. 10 Ndipo ngati Khristu ali mwa inu, thupi lanu ndi lakufa chifukwa cha uchimo, koma mzimu wanu ndi wamoyo chifukwa cha chilungamo. 11 Ndipo ngati Mzimu wa Mulungu amene anaukitsa Yesu kwa akufa akhala mwa inu, Iyeyo amene anaukitsa Khristu kwa akufa adzapatsanso moyo matupi anu amene amafa kudzera mwa Mzimu wake amene amakhala mwa inu.

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero (CCL)

The Word of God in Contemporary Chichewa Copyright © 2002, 2016 by Biblica, Inc.® Used by permission of Biblica, Inc.® All rights reserved worldwide. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Mwini © 2002, 2016 ndi Biblica, Inc.® Kugwiritsa ntchito mwachilolezo. Umwini ndi otetezedwa pa dziko lonse.