Revised Common Lectionary (Semicontinuous)
115 Kwa ife ayi Yehova, kwa ife ayi
koma ulemerero ukhale pa dzina lanu,
chifukwa cha chikondi chanu chosasinthika ndiponso chifukwa cha kukhulupirika kwanu.
2 Chifukwa chiyani anthu a mitundu ina akunena kuti,
“Mulungu wawo ali kuti?”
3 Mulungu wathu ali kumwamba;
Iye amachita chilichonse chimene chimamukondweretsa.
4 Koma mafano awo ndi siliva ndi golide,
opangidwa ndi manja a anthu.
5 Pakamwa ali napo koma sayankhula,
maso ali nawo koma sapenya;
6 makutu ali nawo koma samva,
mphuno ali nazo koma sanunkhiza;
7 manja ali nawo koma akakhudza samva kanthu;
mapazi ali nawo koma sayenda;
kapena pakhosi pawo kutulutsa mawu.
8 Anthu amene amapanga mafanowo adzafanana nawo,
chimodzimodzinso onse amene amadalira mafanowo.
9 Inu Aisraeli, dalirani Yehova;
Iye ndiye thandizo lanu ndi chishango chanu.
10 Iwe nyumba ya Aaroni, dalira Yehova;
Iye ndiye thandizo lako ndi chishango chako.
11 Inu amene mumaopa Iye, dalirani Yehova;
Iye ndiye thandizo lanu ndi chishango chanu.
12 Yehova watikumbukira ndipo adzatidalitsa:
adzadalitsa nyumba ya Israeli,
adzadalitsa nyumba ya Aaroni,
13 adzadalitsa iwo amene amaopa Yehova;
aangʼono ndi aakulu omwe.
14 Yehova akuwonjezereni madalitso;
inuyo pamodzi ndi ana anu.
15 Mudalitsidwe ndi Yehova,
Wolenga kumwamba ndi dziko lapansi.
16 Kumwamba ndi kwa Yehova,
koma dziko lapansi Iye walipereka kwa anthu.
17 Si anthu akufa amene amatamanda Yehova,
amene amatsikira kuli chete;
18 ndi ife amene timatamanda Yehova,
kuyambira tsopano mpaka muyaya.
Tamandani Yehova.
Za Kupatulidwa kwa Alevi
5 Yehova anawuza Mose kuti, 6 “Tenga Alevi pakati pa Aisraeli ndipo uwayeretse. 7 Powayeretsa uchite izi: uwawaze madzi oyeretsa ndipo amete thupi lawo lonse ndi kuchapa zovala zawo kuti adziyeretse. 8 Atenge ngʼombe yayimuna yayingʼono ndi chopereka cha chakudya cha ufa wosalala wosakaniza ndi mafuta. Atengenso ngʼombe ina yayimuna, yayingʼono, ya chopereka chopepesera machimo. 9 Ubwere nawo Aleviwo kutsogolo kwa tenti ya msonkhano ndipo usonkhanitse gulu la Aisraeli. 10 Ubwere nawo pamaso pa Yehova, ndipo Aisraeli asanjike manja awo pa iwo. 11 Aaroni apereke Alevi aja pamaso pa Yehova ngati chopereka choweyula kuchokera kwa Aisraeli kuti akhale okonzeka kugwira ntchito ya Yehova.
12 “Alevi akatsiriza kusanjika manja awo pa mitu ya ngʼombe zazimuna, imodzi ikhale ya nsembe yopepesera machimo ndipo inayo ikhale ya nsembe yopsereza ya kwa Yehova, kupepesera machimo a Alevi. 13 Uyimiritse Aleviwo pamaso pa Aaroni ndi ana ake aamuna ndipo uwapereke ngati nsembe yoweyula kwa Yehova. 14 Pochita zimenezi mudzapatula Alevi pakati pa Aisraeli ndipo Aleviwo adzakhala anga.
15 “Utatha kuyeretsa ndi kupereka Aleviwo monga nsembe yoweyula, apite kukagwira ntchito yawo ku tenti ya msonkhano. 16 Iwo ndiwo Aisraeli amene aperekedwa kwathunthu kwa Ine. Ndawatenga kuti akhale anga mʼmalo mwa mwana wamwamuna aliyense woyamba kubadwa wa Mwisraeli aliyense wamkazi. 17 Mwana aliyense wamwamuna woyamba kubadwa mu Israeli, kaya wa munthu kapena wa ziweto, ndi wanga. Pamene ndinakantha ana oyamba kubadwa ku Igupto, ndinawapatulira kwa Ine mwini. 18 Ndipo ndatenga Alevi mʼmalo mwa ana aamuna onse oyamba kubadwa mu Israeli. 19 Mwa Aisraeli onse, ndapereka Alevi kuti akhale mphatso kwa Aaroni ndi ana ake aamuna kugwira ntchito ya ku tenti ya msonkhano mʼmalo mwa Aisraeli onse kuti azikapereka nsembe yopepesera machimo, kuti mliri usadzaphe Aisraeli pamene ayandikira ku malo wopatulika.”
20 Mose, Aaroni pamodzi ndi gulu lonse la Israeli anachita kwa Alevi monga momwe Yehova analamulira Mose. 21 Alevi anadziyeretsa ndi kuchapa zovala zawo. Kenaka Aaroni anawapereka ngati nsembe yoweyula pamaso pa Yehova ndi kuchita nsembe yopepesera machimo yowayeretsa. 22 Zitatha zimenezi, Alevi anapita kukagwira ntchito yawo ku tenti ya msonkhano motsogozedwa ndi Aaroni ndi ana ake aamuna. Anachita kwa Alevi monga momwe Yehova analamulira Mose.
1 Ndine Paulo, mtumiki wa Mulungu, ndi mtumwi wa Yesu Khristu. Ndinatumidwa kuti nditsogolere amene Mulungu anawasankha ku chikhulupiriro ndi ku chidziwitso cha choonadi chimene chimawafikitsa ku moyo wolemekeza Mulungu 2 ndi kuwapatsa chiyembekezo cha moyo wosatha, umene Mulungu amene sanama, analonjeza nthawi isanayambe. 3 Pa nthawi yake Mulungu, Mpulumutsi wathu anawulula poyera mawu ake ndipo analamula kuti ndipatsidwe udindo wolalikira uthengawu.
4 Kwa Tito, mwana wanga weniweni mʼchikhulupiriro cha ife tonse:
Chisomo ndi mtendere zochokera kwa Mulungu Atate ndi Khristu Yesu Mpulumutsi wathu.
Ntchito ya Tito ku Krete
5 Ndinakusiya ku Krete kuti ulongosole zonse zimene ndinazisiya zisanathe ndiponso usankhe akulu ampingo mʼmizinda yonse, monga momwe ndinakulamulira. 6 Mkulu wampingo akhale munthu wopanda cholakwa, akhale wa mkazi mmodzi yekha, munthu amene ana ake ndi okhulupirira, osati amakhalidwe oyipa ndi osamvera. 7 Popeza mkulu wa mpingo amayendetsa ntchito za banja la Mulungu, ayenera kukhala wopanda cholakwa, asakhale womva zayekha, kapena wopsa mtima msanga, kapena womwa zoledzeretsa, kapena wandewu, kapena wopeza phindu mwachinyengo. 8 Koma akhale wosamala bwino alendo, wokonda zabwino, wodziretsa, wolungama, woyera mtima ndi wosunga mwambo. 9 Iye ayenera kugwiritsa mawu okhulupirika monga tinaphunzitsira, kuti athe kulimbikitsa ena ndi chiphunzitso choona ndiponso kugonjetsa amene atsutsana nacho.
The Word of God in Contemporary Chichewa Copyright © 2002, 2016 by Biblica, Inc.® Used by permission of Biblica, Inc.® All rights reserved worldwide. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Mwini © 2002, 2016 ndi Biblica, Inc.® Kugwiritsa ntchito mwachilolezo. Umwini ndi otetezedwa pa dziko lonse.