Revised Common Lectionary (Semicontinuous)
Kwa mtsogoleri wa mayimbidwe. Salimo la ana a Kora.
47 Ombani mʼmanja, inu anthu onse;
fuwulani kwa Mulungu ndi mawu achimwemwe.
2 Ndi woopsadi Yehova Wammwambamwamba;
Mfumu yayikulu ya dziko lonse lapansi!
3 Iye anatigonjetsera mitundu yambirimbiri ya anthu;
anayika anthu pansi pa mapazi athu.
4 Iye anatisankhira cholowa chathu,
chonyaditsa cha Yakobo, amene anamukonda.
Sela
5 Mulungu wakwera, anthu akumufuwulira mwachimwemwe,
Yehova wakwera, akumuyimbira malipenga.
6 Imbani matamando kwa Mulungu, imbani matamando;
imbani matamando kwa mfumu yathu, imbani matamando.
7 Pakuti Mulungu ndi mfumu ya dziko lonse lapansi;
imbirani Iye salimo la matamando.
8 Mulungu akulamulira mitundu ya anthu;
Mulungu wakhala pa mpando wake waufumu woyera.
9 Anthu otchuka mwa anthu a mitundu ina asonkhana
monga anthu a Mulungu wa Abrahamu,
pakuti mafumu a dziko lapansi ndi ake a Mulungu;
Iye wakwezedwa kwakukulu.
Mose Amwalira
34 Ndipo Mose anakwera Phiri la Nebo kuchokera ku chigwa cha Mowabu ndi kukafika pamwamba pa Phiri la Pisiga, kummawa kwa Yeriko. Kumeneko Yehova anamuonetsa dziko lonse; kuchokera ku Giliyadi mpaka ku Dani. 2 Dera lonse la Nafutali, dziko lonse la Efereimu ndi Manase, dziko lonse la Yuda mpaka kukafika kumadzulo kwa nyanja, 3 Negevi ndi chigawo chonse kuchokera ku Chigwa cha Yeriko, Mzinda wa mitengo ya migwalangwa, mpaka ku Zowari. 4 Kenaka Yehova anawuza Mose kuti, “Limenelo ndi dziko limene ndinalonjeza mwa lumbiro kwa Abrahamu, Isake ndi Yakobo pamene ndinanena kuti, ‘Ndidzalipereka kwa zidzukulu zanu.’ Ndakulola kuti ulione, koma sudzawoloka kuti ukalowemo.”
5 Choncho Mose mtumiki wa Yehova anamwalira kumeneko ku Mowabu, monga momwe ananenera Yehova. 6 Yehova anamuyika mʼmanda ku Mowabu, mʼchigwa choyangʼanana ndi Beti-Peori, koma mpaka lero palibe amene amadziwa pamene pali manda ake. 7 Mose anamwalira ali ndi zaka 120, koma maso ake ankaonabe ndipo anali amphamvu.
4 Ine ndakuwuzani izi kuti nthawi ikadzafika mudzakumbukire kuti Ine ndinakuchenjezani kale. Ine sindinakuwuzeni izi poyamba paja chifukwa ndinali nanu.”
Ntchito ya Mzimu Woyera
5 “Tsopano Ine ndikupita kwa Iye amene anandituma koma palibe wina mwa inu akundifunsa kuti, ‘Kodi mukupita kuti?’ 6 Muli ndi chisoni kwambiri chifukwa ndakuwuzani zimene. 7 Komatu ndakuwuzani zoona. Ine ndikuti kuli bwino kwa inu kuti ndichoke. Ngati sindichoka, Nkhosweyo sidzabwera kwa inu, koma ngati Ine ndipita, ndidzamutumiza kwa inu. 8 Iye akabwera, adzatsutsa dziko lapansi za uchimo, zachilungamo ndi zachiweruzo. 9 Za uchimo, chifukwa anthu sakhulupirira Ine. 10 Za chilungamo, chifukwa Ine ndi kupita kwa Atate, kumene simudzandionanso. 11 Za chiweruzo, chifukwa wolamulira dziko lino lapansi waweruzidwa tsopano.
The Word of God in Contemporary Chichewa Copyright © 2002, 2016 by Biblica, Inc.® Used by permission of Biblica, Inc.® All rights reserved worldwide. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Mwini © 2002, 2016 ndi Biblica, Inc.® Kugwiritsa ntchito mwachilolezo. Umwini ndi otetezedwa pa dziko lonse.