Revised Common Lectionary (Semicontinuous)
15 Pa nthawi imeneyo Petro anayimirira pakati pa okhulupirira (gulu la anthu pafupifupi 120). 16 Iye anati, “Abale anga, Malemba anayenera kukwaniritsidwa omwe Mzimu Woyera anayankhula kalekale kudzera mwa Davide za Yudasi, amene anatsogolera amene anamugwira Yesu. 17 Iye anali mmodzi wa gulu lathu ndipo anatumikira pamodzi ndi ife.”
21 Chifukwa chake ndi kofunika kusankha mmodzi wa anthu amene akhala nafe nthawi yonse imene Ambuye Yesu ankayenda nafe, 22 kuyambira pa nthawi ya ubatizo wa Yohane mpaka nthawi imene Yesu anatengedwa pakati pathu. Pakuti mmodzi wa anthu awa ayenera kukhala mboni pamodzi ndi ife zakuuka kwake.”
23 Pamenepo anasankha anthu awiri, Yosefe wotchedwa Barsaba (wodziwikanso kuti Yusto) ndi Matiyasi. 24 Kenaka iwo anapemphera nati, “Ambuye mukudziwa mtima wa aliyense. Tionetseni amene mwamusankha mwa awiri awa 25 kuti atenge ntchito iyi ya utumwi, imene Yudasi anasiya napita kumalo womuyenera.” 26 Tsono anachita maere, ndipo maerewo anagwera Matiyasi. Tsono iye anawonjezedwa pa gulu la atumwi khumi ndi mmodziwo.
BUKU LOYAMBA
Masalimo 1–41
1 Wodala munthu
amene satsatira uphungu wa anthu ochimwa,
kapena kuyima mʼnjira ya anthu oyipa,
kapena kukhala mʼmagulu a anthu onyoza.
2 Koma chikondwerero chake chili mʼmalamulo a Yehova
ndipo mʼmalamulo akewo amalingaliramo usana ndi usiku.
3 Iye ali ngati mtengo wodzalidwa mʼmbali mwa mitsinje ya madzi,
umene umabereka zipatso zake pa nyengo yake
ndipo masamba ake safota.
Chilichonse chimene amachita amapindula nacho.
4 Sizitero ndi anthu oyipa!
Iwo ali ngati mungu
umene umawuluzidwa ndi mphepo.
5 Kotero anthu oyipa sadzatha kuyima pa chiweruzo,
kapena anthu ochimwa mu msonkhano wa anthu olungama.
6 Pakuti Yehova amayangʼanira mayendedwe a anthu olungama,
koma mayendedwe a anthu oyipa adzawonongeka.
9 Timalandira umboni wa anthu, koma umboni wa Mulungu ndi wopambana. Umboniwo ndi umene anachitira Mwana wake. 10 Aliyense amene amakhulupirira Mwana wa Mulungu ali nawo umboniwu mu mtima mwake, koma aliyense amene sanakhulupirire Mulungu amayesa kuti Mulunguyo ndi wonama, chifukwa sanakhulupirire umboni umene Mulungu anachitira wa Mwana wake. 11 Ndipo umboniwo ndi uwu: Mulungu anatipatsa moyo wosatha, ndipo moyowu uli mwa Mwana wake. 12 Iye amene ali ndi Mwana ali ndi moyo, amene alibe Mwana wa Mulungu alibe moyo.
Mawu Otsiriza
13 Ine ndikulemba zimenezi kwa inu, amene mwakhulupirira dzina la Mwana wa Mulungu kuti mudziwe kuti muli ndi moyo wosatha.
Yesu Apempherera Ophunzira Ake
6 “Ine ndawadziwitsa za Inu anthu amene munandipatsa mʼdziko lapansi. Iwo anali anu. Inu munawapereka kwa Ine ndipo amvera mawu anu. 7 Tsopano akudziwa kuti zonse zimene munandipatsa nʼzochokera kwa Inu. 8 Pakuti Ine ndiwapatsa mawu amene Inu munandipatsa ndipo awalandira. Iwo akudziwa ndithu kuti Ine ndinachokera kwa Inu, ndipo akukhulupirira kuti Inu ndiye amene munandituma Ine. 9 Ine ndikuwapempherera. Ine sindikupempherera dziko lapansi, koma anthu amene Inu mwandipatsa, pakuti ndi anu. 10 Zonse zimene Ine ndili nazo ndi zanu, ndipo zonse zimene Inu muli nazo ndi zanga. Choncho Ine ndalemekezedwa mwa iwowo. 11 Ine sindikukhalanso mʼdziko lapansi nthawi yayitali, koma iwo akanali mʼdziko lapansi. Ine ndikubwera kwa Inu. Atate Woyera, atetezeni ndi mphamvu za dzina lanu. Dzina limene munandipatsa Ine, kuti iwo akhale amodzi monga Ife tili amodzi. 12 Pamene ndinali nawo, ndinawateteza ndi kuwasunga mosamala mʼdzina limene munandipatsa. Palibe ndi mmodzi yemwe amene anatayika kupatula yekhayo amene anayenera kuwonongeka kuti malemba akwaniritsidwe.
13 “Tsopano ndikubwera kwa Inu. Ndikunena izi ndikanali mʼdziko lapansi, kuti iwo akhale ndi muyeso wodzaza wachimwemwe changa mʼkati mwawo. 14 Ine ndawapatsa mawu anu ndipo dziko lapansi likudana nawo, pakuti sali a dziko lapansi monga Ine sindilinso wa dziko lapansi. 15 Sindikupempha kuti muwachotse mʼdziko lapansi koma kuti muwateteze kwa woyipayo. 16 Iwo si a dziko lapansi, monga Ine sindilinso wa dziko lapansi. 17 Ayeretseni ndi choonadi chanu. Mawu anu ndiye choonadi. 18 Monga Inu munandituma Ine mʼdziko lapansi, Inenso ndikuwatuma mʼdziko lapansi. 19 Chifukwa cha iwowa Ine ndikudziyeretsa, kuti iwo ayeretsedwenso kwenikweni.
The Word of God in Contemporary Chichewa Copyright © 2002, 2016 by Biblica, Inc.® Used by permission of Biblica, Inc.® All rights reserved worldwide. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Mwini © 2002, 2016 ndi Biblica, Inc.® Kugwiritsa ntchito mwachilolezo. Umwini ndi otetezedwa pa dziko lonse.