Revised Common Lectionary (Semicontinuous)
115 Kwa ife ayi Yehova, kwa ife ayi
koma ulemerero ukhale pa dzina lanu,
chifukwa cha chikondi chanu chosasinthika ndiponso chifukwa cha kukhulupirika kwanu.
2 Chifukwa chiyani anthu a mitundu ina akunena kuti,
“Mulungu wawo ali kuti?”
3 Mulungu wathu ali kumwamba;
Iye amachita chilichonse chimene chimamukondweretsa.
4 Koma mafano awo ndi siliva ndi golide,
opangidwa ndi manja a anthu.
5 Pakamwa ali napo koma sayankhula,
maso ali nawo koma sapenya;
6 makutu ali nawo koma samva,
mphuno ali nazo koma sanunkhiza;
7 manja ali nawo koma akakhudza samva kanthu;
mapazi ali nawo koma sayenda;
kapena pakhosi pawo kutulutsa mawu.
8 Anthu amene amapanga mafanowo adzafanana nawo,
chimodzimodzinso onse amene amadalira mafanowo.
9 Inu Aisraeli, dalirani Yehova;
Iye ndiye thandizo lanu ndi chishango chanu.
10 Iwe nyumba ya Aaroni, dalira Yehova;
Iye ndiye thandizo lako ndi chishango chako.
11 Inu amene mumaopa Iye, dalirani Yehova;
Iye ndiye thandizo lanu ndi chishango chanu.
12 Yehova watikumbukira ndipo adzatidalitsa:
adzadalitsa nyumba ya Israeli,
adzadalitsa nyumba ya Aaroni,
13 adzadalitsa iwo amene amaopa Yehova;
aangʼono ndi aakulu omwe.
14 Yehova akuwonjezereni madalitso;
inuyo pamodzi ndi ana anu.
15 Mudalitsidwe ndi Yehova,
Wolenga kumwamba ndi dziko lapansi.
16 Kumwamba ndi kwa Yehova,
koma dziko lapansi Iye walipereka kwa anthu.
17 Si anthu akufa amene amatamanda Yehova,
amene amatsikira kuli chete;
18 ndi ife amene timatamanda Yehova,
kuyambira tsopano mpaka muyaya.
Tamandani Yehova.
5 Ndipo pa nthawi ya nsembe ya madzulo, ndinadzidzimuka mu mtima wanga wokhumudwa nʼkuyimirira, zovala zanga ndi mwinjiro wanga zikanali zongʼambika ndipo ndinagwada ndi kukweza manja anga kwa Yehova Mulungu wanga 6 ndipo ndinapemphera kuti,
“Inu Mulungu wanga, ndine wamanyazi ndi wachisoni moti sindingathe kukweza nkhope yanga kwa Inu Mulungu wanga, chifukwa machimo athu akwera kupambana mitu yathu, ndipo kulakwa kwathu kwafika ku thambo. 7 Ndipo chifukwa cha machimo athu, ifeyo, mafumu athu, ndi ansembe athu takhala akutipereka mʼmanja mwa mafumu a mitundu ina ya anthu kuti atiphe pa nkhondo, atitenge ku ukapolo, atilande zinthu zathu ndi kutichititsa manyazi monga zilili leromu.
8 “Koma tsopano, pa kanthawi kochepa, Inu Yehova Mulungu wathu mwaonetsa kukoma mtima. Inu mwalola kuti ena mwa ife tipulumuke ku ukapolo ndi kutipatsa cholowa mʼmalo anu oyera. Mwatipulumutsa ku ukapolo ndi kutipatsa mpumulo pangʼono mu ukapolo wathu. 9 Ndifedi akapolo. Koma Inu Yehova simunatileke mu ukapolo wathu. Mwationetsa chikondi chanu chosasinthika pamaso pa mafumu a ku Perisiya. Mwatitsitsimutsa kuti timange Nyumba yanu pokonzanso mabwinja ake. Mwatitchinjiriza mʼdziko la Yuda ndi Yerusalemu.
10 “Koma tsopano, Inu Mulungu wathu, kodi tinganene chiyani titachita zoyipa zonsezi? Ife taphwanya malamulo anu 11 amene munawapereka kudzera mwa atumiki anu aneneri. Inu munati, ‘Dziko limene mukulowamolo kuti likhale cholowa chanu, ndi dziko lodetsedwa ndi zonyansa za mitundu ya mʼmayikomo. Ndipo adzaza dzikolo ndi zochita zawo zonyansa. 12 Nʼchifukwa chake, musapereke ana anu aakazi kuti akwatiwe ndi ana awo aamuna kapena kulola kuti ana awo aakazi akwatiwe ndi ana anu aamuna. Musagwirizane nawo, kapena kuchita nawo malonda kuti mukhale amphamvu ndi kudya zokoma za mʼdzikomo ndi kusiyira ana anu dzikoli ngati cholowa chawo mpaka kalekale.’
13 “Tsono pambuyo pa zonse zimene zatigwera chifukwa cha ntchito zathu zoyipa ndi uchimo wathu waukulu, komanso pambuyo poona kuti Inu Mulungu wathu simunangotilanga kokha pangʼono kuyerekeza ndi kuchimwa kwathu komanso mwalola kuti ena mwa ife tipulumuke, 14 kodi ife nʼkuphwanyanso malamulo anu ndi kukwatirana ndi anthu amitundu ina amene amachita zonyansa zimenezi? Kodi simudzatikwiyira ndi kutiwononga kwathunthu popanda wina wotsala kapena wopulumuka? 15 Inu Yehova, Mulungu wa Israeli, ndinu wachifundo, pakuti ndife otsala amene tapulumuka monga mmene zilili lero lino. Ife tayima pamaso panu ngakhale tikudziwa kuchimwa kwathu pakuti palibe munthu amene angathe kuyima pamaso panu chifukwa cha machimo ake.”
Chisoni cha Ophunzira Chisandulika Chimwemwe
16 Yesu anapitiriza kuyankhula kuti, “Mwa kanthawi kochepa, simudzandionanso, ndipo patatha nthawi pangʼono mudzandionanso.”
17 Ena a ophunzira ake anati kwa wina ndi mnzake, “Kodi Iye akutanthauza chiyani ponena kuti, ‘Mwa kanthawi kochepa, simudzandionanso,’ ndi ‘ndipo patatha nthawi pangʼono mudzandionanso,’ ndiponso ‘chifukwa ndikupita kwa Atate?’ ” 18 Iwo anapitiriza kufunsana kuti, “Kodi akutanthauza chiyani, ‘kanthawi kochepa?’ Ife sitikumvetsetsa chimene Iye akuyankhula.”
19 Yesu anadziwa kuti ankafuna kuti amufunse za zimenezi, choncho anawafunsa kuti, “Kodi mukufunsana wina ndi mnzake chimene Ine ndimatanthauza pamene ndinati, ‘Mwa kanthawi kochepa simudzandionanso,’ ndi ‘patatha nthawi pangʼono mudzandionanso?’ 20 Zoonadi, Ine ndikukuwuzani kuti inu mudzalira ndi kubuma pomwe dziko lapansi lidzakhale likukondwera. Inu mudzamva chisoni, koma chisoni chanu chidzasandulika chimwemwe. 21 Mayi akamabereka mwana amamva ululu chifukwa nthawi yake yafika; koma mwana wake akabadwa amayiwala ululu wake chifukwa cha chimwemwe chake chakuti mwana wabadwa mʼdziko lapansi. 22 Chimodzimodzinso ndi inu. Tsopano ino ndi nthawi yanu yomva chisoni, koma Ine ndidzakuonaninso ndipo inu mudzasangalala, ndipo palibe amene adzachotsa chimwemwe chanu. 23 Tsiku limenelo inu simudzandipemphanso kalikonse. Ine ndikukuwuzani zoona kuti Atate anga adzakupatsani chilichonse chimene mudzapempha mʼdzina langa. 24 Mpaka tsopano simunapemphe kalikonse mʼdzina langa. Pemphani ndipo mudzalandira, ndipo chimwemwe chanu chidzakhala chathunthu.
The Word of God in Contemporary Chichewa Copyright © 2002, 2016 by Biblica, Inc.® Used by permission of Biblica, Inc.® All rights reserved worldwide. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Mwini © 2002, 2016 ndi Biblica, Inc.® Kugwiritsa ntchito mwachilolezo. Umwini ndi otetezedwa pa dziko lonse.