Revised Common Lectionary (Semicontinuous)
93 Yehova akulamulira, wavala ulemerero;
Yehova wavala ulemerero ndipo wadzimangirira mphamvu,
dziko lonse lakhazikika kolimba; silingasunthidwe.
2 Mpando wanu waufumu unakhazikika kalekale;
Inu ndinu wamuyaya.
3 Nyanja zakweza Inu Yehova,
nyanja zakweza mawu ake;
nyanja zakweza mafunde ake ochita mkokomo.
4 Yehova ndi wamphamvu kupambana mkokomo wa madzi ambiri,
ndi wamphamvu kupambana mafunde a nyanja,
Yehova mmwamba ndi wamphamvu.
5 Malamulo anu Yehova ndi osasinthika;
chiyero chimakongoletsa nyumba yanu
mpaka muyaya.
18 Sungani mawu amenewa mu mtima mwanu ndi mʼmaganizo mwanu, muwamangirire pa mikono yanu ndipo muwayike pamphumi panu. 19 Mawuwa muziphunzitsa ana anu, muzikamba za iwo pamene mukhala pansi mʼnyumba zanu, pamene mukuyenda mʼnjira, pamene mugona ndi pamene mukudzuka. 20 Muwalembe pa mphuthu za nyumba zanu ndi pa zipata zanu, 21 kuti inu ndi ana anu mukhale mʼdziko limene Yehova analumbira kupatsa makolo anu mpaka kalekale monga umakhalira mlengalenga pamwamba pa dziko.
Yesu Apita Kumwamba
19 Ambuye Yesu atatha kuyankhulana nawo, anatengedwa kupita kumwamba ndipo anakhala kudzanja lamanja la Mulungu. 20 Pamenepo ophunzira aja anapita ndi kukalalikira ponseponse, ndipo Ambuye anagwira nawo ntchito pamodzi, ndipo anatsimikizira mawuwo ndi zizindikiro zimene ankachita.
The Word of God in Contemporary Chichewa Copyright © 2002, 2016 by Biblica, Inc.® Used by permission of Biblica, Inc.® All rights reserved worldwide. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Mwini © 2002, 2016 ndi Biblica, Inc.® Kugwiritsa ntchito mwachilolezo. Umwini ndi otetezedwa pa dziko lonse.