Revised Common Lectionary (Semicontinuous)
71 Mwa Inu Yehova ine ndathawiramo;
musalole kuti ndichititsidwe manyazi.
2 Mundilanditse ndi kundipulumutsa mwa chilungamo chanu,
mutchere khutu lanu ndi kundipulumutsa.
3 Mukhale thanthwe langa lothawirapo,
kumene ine nditha kupita nthawi zonse;
lamulani kuti ndipulumuke,
pakuti Inu ndinu thanthwe langa ndi linga langa.
4 Landitseni Inu Mulungu wanga, kuchoka mʼdzanja la oyipa,
kuchoka mʼdzanja la oyipa ndi anthu ankhanza.
5 Pakuti Inu mwakhala chiyembekezo changa, Inu Ambuye Wamphamvuzonse,
chilimbikitso changa kuyambira ndili mwana.
6 Kuyambira pamene ndinabadwa, ndakhala ndikudalira Inu;
Inu munanditulutsa mʼmimba mwa amayi anga,
ndipo ndidzakupembedzani nthawi zonse.
Yosiya Akonzanso Chipembedzo
34 Yosiya anali wa zaka zisanu ndi zitatu pamene anakhala mfumu, ndipo analamulira mu Yerusalemu kwa zaka 31. 2 Iye anachita zolungama pamaso pa Yehova ndi kutsata makhalidwe a Davide abambo ake, osatembenukira kumanja kapena kumanzere.
3 Mʼchaka chachisanu ndi chitatu cha ulamuliro wake, iye akanalibe wamngʼono, anayamba kufunafuna Mulungu wa Davide abambo ake. Mʼchaka cha khumi ndi chiwiri iye anayamba kuyeretsa Yuda ndi Yerusalemu kuchotsa malo azipembedzo, mafano a Asera, milungu yosema ndi mafano owumbidwa. 4 Maguwa ansembe a Baala anagwetsedwa iye atalamulira. Anadula zidutswazidutswa maguwa ofukizira lubani amene anali pamwamba pake, ndipo anaphwanya mafano a Asera, milungu ndi zifaniziro zake. Anaziperapera ndipo anaziwaza pamwamba pa manda a amene ankapereka nsembe kwa mafanowo. 5 Iye anatentha mafupa a ansembe pa maguwa awo, kotero iye anayeretsa Yuda ndi Yerusalemu. 6 Ku mizinda ya Manase, Efereimu ndi Simeoni mpaka kufika ku Nafutali, ndiponso malo a mabanja owazungulira, 7 iye anagwetsa maguwa ansembe ndi mafano a Asera ndi kuphwanyaphwanya milungu yawo kukhala fumbi ndi kuduladula maguwa ofukizapo lubani mʼdziko lonse la Israeli. Atatero, anabwerera ku Yerusalemu.
44 Petro akuyankhulabe mawu amenewa, Mzimu Woyera unatsikira pa onse amene amamva uthengawo. 45 Abale a mdulidwe omwe anabwera ndi Petro anadabwa kuona kuti mphatso ya Mzimu Woyera yapatsidwanso kwa anthu a mitundu ina. 46 Pakuti anamva iwo akuyankhula mʼmalilime ndi kuyamika Mulungu. Ndipo Petro anati, 47 “Kodi alipo amene angawaletse anthu awa kubatizidwa mʼmadzi? Iwotu alandira Mzimu Woyera monga ifenso.” 48 Tsono iye analamula kuti abatizidwe mʼdzina la Yesu Khristu. Ndipo anthu aja anamupempha Petro kuti akhale nawo masiku angapo.
The Word of God in Contemporary Chichewa Copyright © 2002, 2016 by Biblica, Inc.® Used by permission of Biblica, Inc.® All rights reserved worldwide. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Mwini © 2002, 2016 ndi Biblica, Inc.® Kugwiritsa ntchito mwachilolezo. Umwini ndi otetezedwa pa dziko lonse.