Revised Common Lectionary (Semicontinuous)
Salimo la Davide.
29 Perekani kwa Yehova, inu anthu amphamvu,
perekani kwa Yehova ulemerero ndi mphamvu.
2 Perekani kwa Yehova ulemerero woyenera dzina lake,
pembedzani Yehova mwa kukongola kwa chiyero chake.
3 Liwu la Yehova lili pamwamba pa madzi;
Mulungu waulemerero abangula,
Yehova abangula pamwamba pa madzi amphamvu.
4 Liwu la Yehova ndi lamphamvu;
liwu la Yehova ndi laulemerero.
5 Liwu la Yehova limathyola mikungudza;
Yehova amathyolathyola mikungudza ya ku Lebanoni.
6 Iye amachititsa Lebanoni kulumphalumpha ngati mwana wangʼombe,
Siriyoni ngati mwana wa njati:
7 Liwu la Yehova limakantha
ngati kungʼanima kwa mphenzi.
8 Liwu la Yehova limagwedeza chipululu;
Yehova amagwedeza chipululu cha Kadesi.
9 Liwu la Yehova limapindapinda mibawa
ndi kuyeretsa nkhalango.
Ndipo mʼNyumba mwake onse amafuwula kuti, “Ulemerero!”
10 Yehova amakhala pamwamba pa madzi osefukira,
Yehova ndiye mfumu kwamuyaya.
11 Yehova amapereka mphamvu kwa anthu ake;
Yehova amadalitsa anthu ake ndi mtendere.
Chilichonse Chili ndi Nthawi
3 Chinthu chilichonse chili ndi nthawi yake,
ndi nyengo yake yomwe anayika Mulungu:
2 Nthawi yobadwa ndi nthawi yomwalira,
nthawi yodzala ndi nthawi yokolola.
3 Nthawi yakupha ndi nthawi yochiritsa,
nthawi yogwetsa ndi nthawi yomanga.
4 Nthawi yomva chisoni ndi nthawi yosangalala,
nthawi yolira maliro ndi nthawi yovina.
5 Nthawi yotaya miyala ndi nthawi yokundika miyala,
nthawi yokumbatirana ndi nthawi yoleka kukumbatirana.
6 Nthawi yofunafuna ndi nthawi yoleka kufunafuna,
nthawi yosunga ndi nthawi yotaya.
7 Nthawi yongʼamba ndi nthawi yosoka,
nthawi yokhala chete ndi nthawi yoyankhula.
8 Nthawi yokondana ndi nthawi yodana,
nthawi ya nkhondo ndi nthawi ya mtendere.
9 Kodi wantchito amapeza phindu lanji pa ntchito yake yolemetsa? 10 Ine ndinaona chipsinjo chimene Mulungu anayika pa anthu. 11 Iye anapanga chinthu chilichonse kuti chikhale chabwino pa nthawi yake. Anayika nzeru zamuyaya mʼmitima ya anthu; komabe anthuwo sangathe kuzindikira zomwe Mulungu wachita kuyambira pa chiyambi mpaka chimaliziro. 12 Ine ndikudziwa kuti palibenso kanthu kabwino kwa anthu kopambana kusangalala ndi kuchita zabwino pamene ali ndi moyo. 13 Ndi mphatso ya Mulungu kwa munthu kuti azidya, azimwa ndi kumakondwera ndi ntchito zake zolemetsa. 14 Ndikudziwa kuti chilichonse chimene Mulungu amachita chidzakhala mpaka muyaya; palibe zimene zingawonjezedwe kapena kuchotsedwa. Mulungu amazichita kuti anthu azimuopa.
15 Chilichonse chimene chilipo chinalipo kale,
ndipo chimene chidzakhalapo chinalipo poyamba;
Mulungu amabwezanso zakale zimene zinapita kuti zichitikenso.
11 Kodi ndani mwa anthu angadziwe maganizo a munthu wina, kupatula mzimu wa munthuyo wokhala mʼkati mwake? Chimodzimodzinso palibe amene adziwa maganizo a Mulungu kupatula Mzimu wa Mulunguyo. 12 Mzimu amene tinalandira ife si wa dziko lapansi koma Mzimu wochokera kwa Mulungu wotipatsa ife mwaulere. 13 Izi ndi zimene timayankhula osati mʼmawu wophunzitsidwa ndi nzeru za munthu koma mʼmawu wophunzitsidwa ndi Mzimu, kufotokozera zoonadi zauzimu mʼmawu auzimu. 14 Munthu wopanda Mzimu savomereza zinthu zimene zichokera kwa Mzimu wa Mulungu, popeza ndi zopusa kwa iyeyo, ndipo sangazimvetsetse chifukwa zimazindikirika mwa Mzimu. 15 Munthu wauzimu amaweruza pa zinthu zonse, koma iye mwini saweruzidwa ndi munthu aliyense. 16 Pakuti
“Ndani anadziwa malingaliro a Ambuye,
kuti akhoza kumulangiza Iye.”
Koma tili nawo mtima wa Khristu.
The Word of God in Contemporary Chichewa Copyright © 2002, 2016 by Biblica, Inc.® Used by permission of Biblica, Inc.® All rights reserved worldwide. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Mwini © 2002, 2016 ndi Biblica, Inc.® Kugwiritsa ntchito mwachilolezo. Umwini ndi otetezedwa pa dziko lonse.