Print Page Options
Previous Prev Day Next DayNext

Revised Common Lectionary (Semicontinuous)

Daily Bible readings that follow the church liturgical year, with sequential stories told across multiple weeks.
Duration: 1245 days
Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero (CCL)
Version
Masalimo 119:89-96

Lamedi

89 Mawu anu Yehova ndi amuyaya;
    akhazikika kumwambako.
90 Kukhulupirika kwanu kumakhala mpaka ku mibado yonse;
    Inu munakhazikitsa dziko lapansi ndipo lilipobe.
91 Malamulo anu alipobe mpaka lero lino,
    pakuti zinthu zonse zimatumikira Inu.
92 Malamulo anu akanapanda kukhala chikondwerero changa,
    ndikanawonongeka mʼmasautso anga.
93 Ine sindidzayiwala konse malangizo anu,
    pakuti ndi malangizo anuwo munasunga moyo wanga.
94 Ndine wanu, ndipulumutseni;
    pakuti ndasamala malangizo anu.
95 Anthu oyipa akudikira kuti andiwononge,
    koma ndidzalingalira umboni wanu.
96 Ndadziwa kuti zinthu zonse zili ndi malire,
    koma malamulo anu alibe malire konse.

Yeremiya 36:27-32

27 Mfumu itatentha buku limene linali ndi mawu amene Yeremiya anamulembetsa Baruki, Yehova anayankhula ndi Yeremiya kuti, 28 “Tenganso buku lina ndipo ulembe mawu onse amene anali mʼbuku loyamba lija, limene Yehoyakimu analitentha. 29 Ndiponso akamuwuze Yehoyakimu mfumu ya Yuda kuti, ‘Yehova akuti: Iwe unatentha buku lija ndipo unati: Nʼchifukwa chiyani unalemba kuti mfumu ya ku Babuloni idzabwera ndithu kudzawononga dziko lino ndi kupha anthu pamodzi ndi nyama zomwe?’ 30 Nʼchifukwa chake kunena za Yehoyakimu mfumu ya Yuda Yehova akuti sipadzaoneka munthu wina wolowa mʼmalo mwake pa mpando wa Davide. Akadzafa mtembo wake udzaponyedwa kunja ndipo udzakhala pa dzuwa masana, ndi pachisanu chowundana usiku. 31 Ndidzamulanga pamodzi ndi ana ake ndiponso omutumikira ake chifukwa cha zoyipa zawo; ndidzagwetsa pa iwo ndi pa onse amene akukhala mu Yerusalemu ndiponso pa anthu a ku Yuda masautso onse amene ndinawanena, chifukwa sanamvere.”

32 Choncho Yeremiya anatenga buku lina napatsa mlembi Baruki mwana wa Neriya, ndipo Yeremiya anamulembetsa mawu onse amene anali mʼbuku limene Yehoyakimu mfumu ya Yuda anatentha. Ndipo anawonjezerapo mawu ambiri monga omwewo.

Luka 4:38-44

Yesu Achiritsa Anthu Ambiri

38 Yesu anatuluka mʼsunagoge ndipo anapita kwa Simoni. Tsopano mpongozi wake wa Simoni amadwala malungo akulu, ndipo anamupempha Yesu kuti amuthandize. 39 Ndipo anawerama nadzudzula malungowo ndipo anamusiya. Anadzuka nthawi yomweyo nayamba kuwatumikira.

40 Pamene dzuwa linkalowa, anthu anabweretsa kwa Yesu onse amene anali ndi matenda osiyanasiyana, ndipo atasanjika manja ake pa aliyense, anachiritsidwa. 41 Komanso ziwanda zinkatuluka mwa anthu ambiri, zikufuwula kuti, “Inu ndinu Mwana wa Mulungu!” Koma Iye anazidzudzula ndipo sanazilole kuyankhula chifukwa zimadziwa kuti Iye ndi Khristu.

42 Kutacha, Yesu anapita ku malo a yekha. Anthu ankamufunafuna Iye ndipo pamene anafika kumene anali, anthuwo anayesetsa kumuletsa kuti asawachokere. 43 Koma Iye anati, “Ine ndikuyenera kulalikira Uthenga Wabwino wa ufumu wa Mulungu ku mizinda inanso chifukwa ichi ndi chimene ananditumira.” 44 Ndipo Iye anapitirirabe kulalikira mʼmasunagoge a ku Yudeya.

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero (CCL)

The Word of God in Contemporary Chichewa Copyright © 2002, 2016 by Biblica, Inc.® Used by permission of Biblica, Inc.® All rights reserved worldwide. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Mwini © 2002, 2016 ndi Biblica, Inc.® Kugwiritsa ntchito mwachilolezo. Umwini ndi otetezedwa pa dziko lonse.