Print Page Options
Previous Prev Day Next DayNext

Revised Common Lectionary (Semicontinuous)

Daily Bible readings that follow the church liturgical year, with sequential stories told across multiple weeks.
Duration: 1245 days
Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero (CCL)
Version
Masalimo 147:12-20

12 Lemekeza Yehova, iwe Yerusalemu;
    tamanda Mulungu wako, iwe Ziyoni,
13 pakuti Iye amalimbitsa mipiringidzo ya zipata zako
    ndi kudalitsa anthu ako mwa iwe.
14 Iye amabweretsa mtendere mʼmalire mwako
    ndi kukukhutitsa ndi ufa wa tirigu wosalala.

15 Iyeyo amapereka lamulo pa dziko lapansi;
    mawu ake amayenda mwaliwiro.
16 Amagwetsa chisanu ngati ubweya
    ndi kumwaza chipale ngati phulusa.
17 Amagwetsa matalala ngati miyala.
    Kodi ndani angathe kupirira kuzizira kwake?
18 Amatumiza mawu ake ndipo chisanucho chimasungunuka;
    amawombetsa mphepo ndipo madzi amayenda.

19 Iye anawulula mawu ake kwa Yakobo,
    malamulo ake ndi zophunzitsa zake kwa Israeli.
20 Sanachitepo zimenezi kwa mtundu wina uliwonse wa anthu;
    anthu enawo sadziwa malamulo ake.

Tamandani Yehova.

Miyambo 1:1-7

Mawu Oyamba: Cholinga ndi Mutu

Iyi ndi miyambi ya Solomoni mwana wa Davide, mfumu ya Israeli:

Ndi yothandiza kuti munthu adziwe nzeru ndi malangizo;
    kuti amvetse mawu a matanthauzo ozama;
kuti alandire malangizo othandiza kuti achite zinthu mwanzeru,
    akhale wangwiro, wachilungamo ndiponso wosakondera.
Ndi yothandiza munthu wamba kuti aphunzire nzeru za kuchenjera,
    achinyamata kudziwa zinthu bwino ndi kulingalira.
Munthu wanzeru amvetse bwino miyamboyi kuti awonjezere kuphunzira kwake,
    ndi munthu womvetsa zinthu bwino apatepo luso,
kuti azimvetsa miyambi ndi mafanizo,
    mawu a anthu anzeru ndi mikuluwiko.

Kuopa Yehova ndiye chiyambi cha nzeru.
    Zitsiru zimanyoza nzeru ndi malangizo.

Yakobo 3:13-18

Mitundu Iwiri ya Nzeru

13 Ndani mwa inu amene ndi wanzeru ndi womvetsa zinthu? Mulekeni aonetse ndi makhalidwe ake abwino kuti nzeru ndiye zikutsogolera kudzichepetsa kwake ndi zochita zake 14 Koma ngati muli ndi mtima wakaduka ndi odzikonda, musadzitamandire kapena kukana choonadi. 15 “Nzeru” zotere sizochokera kumwamba koma ndi za mʼdziko lapansi, si zauzimu koma ndi za ziwanda. 16 Pakuti pamene pali kaduka ndi kudzikonda pomweponso pamakhala chisokonezo ndi zochitika zoyipa zonse.

17 Koma nzeru imene imachoka kumwamba, poyamba ndi yangwiro, ndi yokonda mtendere, yoganizira za ena, yogonjera, yodzaza ndi chifundo ndi chipatso chabwino, yosakondera ndi yoona mtima. 18 Anthu amtendere amene amadzala mtendere amakolola chilungamo.

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero (CCL)

The Word of God in Contemporary Chichewa Copyright © 2002, 2016 by Biblica, Inc.® Used by permission of Biblica, Inc.® All rights reserved worldwide. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Mwini © 2002, 2016 ndi Biblica, Inc.® Kugwiritsa ntchito mwachilolezo. Umwini ndi otetezedwa pa dziko lonse.