Print Page Options
Previous Prev Day Next DayNext

Revised Common Lectionary (Semicontinuous)

Daily Bible readings that follow the church liturgical year, with sequential stories told across multiple weeks.
Duration: 1245 days
Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero (CCL)
Version
Yesaya 62:1-5

Dzina Latsopano la Ziyoni

62 Chifukwa chokonda Ziyoni sindidzakhala chete,
    chifukwa chokonda Yerusalemu sindidzakhala chete,
mpaka chilungamo chake chitaoneka poyera ngati kuwala,
    ndi chipulumutso chake chitaoneka ngati sakali yoyaka.
Mitundu ya anthu idzaona iwe utapambana pa nkhondo
    ndipo mafumu onse adzaona ulemerero wako.
Adzakuyitanira dzina latsopano
    limene adzakupatse ndi Yehova.
Udzakhala ngati chipewa chaulemerero mʼdzanja la Yehova,
    ndi ngati nduwira yaufumu mʼdzanja la Mulungu wako.
Sadzakutchanso “Wosiyidwa,”
    ndipo dziko lako silidzatchedwanso “Chipululu.”
Koma dzina lako latsopano lidzakhala “Ndakondwera naye.”
    Ndipo dziko lako lidzatchedwa “Wokwatiwa.”
Chifukwa Yehova akukondwera nawe,
    ndipo adzakhala ngati mwamuna wa dziko lako.
Monga mnyamata amakwatira namwali,
    momwenso mmisiri wodzakumanga adzakukwatira;
monga mkwati amakondwera ndi mkwatibwi,
    chonchonso Mulungu adzakondwera nawe.

Masalimo 36:5-10

Chikondi chanu Yehova, chimafika ku mayiko a kumwamba,
    kukhulupirika kwanu mpaka ku mitambo.
Chilungamo chanu Mulungu chili ngati mapiri aakulu,
    chiweruzo chanu chili ngati kuzama kwakukulu.
Yehova mumasunga munthu pamodzi ndi chinyama.
    Chikondi chanu chosatha ndi chamtengowapatali!
Otchuka pamodzi ndi anthu wamba pakati pa anthu
    amapeza pothawirapo mu mthunzi wa mapiko anu.
Iwo amadyerera zinthu zambiri za mʼnyumba yanu;
    Inu mumawapatsa chakumwa kuchokera mu mtsinje wanu wachikondwerero.
Pakuti kwa Inu kuli kasupe wamoyo;
    mʼkuwala kwanu ifenso timaona kuwala.

10 Pitirizani chikondi chanu pa iwo amene amakudziwani,
    chilungamo chanu kwa olungama mtima.

1 Akorinto 12:1-11

Mphatso za Mzimu Woyera

12 Tsopano abale anga okondedwa, sindikufuna mukhale osadziwa za mphatso za Mzimu. Inu mukudziwa kuti pamene munali akunja, ankakusocheretsani mʼnjira zosiyanasiyana ndi kukukokerani ku mafano osayankhula. Nʼchifukwa chake ndikuwuzani kuti palibe munthu amene ali ndi Mzimu wa Mulungu angayankhule kuti, “Yesu atembereredwe,” ndiponso palibe munthu anganene kuti “Yesu ndi Ambuye,” popanda kutsogozedwa ndi Mzimu Woyera.

Pali mphatso zosiyanasiyana, koma Mzimu yemweyo. Pali mautumiki osiyanasiyana koma Ambuye yemweyo. Pali magwiridwe antchito osiyanasiyana, koma Mulungu yemweyo amagwira ntchito monsemo mwa anthu onse.

Tsono Mzimu amapereka mphatso kwa aliyense kuti ipindulire onse. Mzimu amapereka kwa munthu wina mawu anzeru, Mzimu yemweyonso amapereka kwa wina mawu achidziwitso. Kwa wina, Mzimu yemweyo amapereka chikhulupiriro, kwa wina mphatso zamachiritso, Mzimu yemweyo. 10 Kwa wina mphamvu zochita zodabwitsa, kwa wina mawu a uneneri, kwa wina mphatso yozindikira mizimu, kwa wina malilime osiyanasiyana, ndiponso kwa wina kutanthauzira malilimewo. 11 Zonsezi ndi ntchito za Mzimu mmodzi yemweyo, ndipo amapereka kwa munthu aliyense monga momwe Mzimuyo wafunira.

Yohane 2:1-11

Yesu Asandutsa Madzi Kukhala Vinyo

Pa tsiku lachitatu munali ukwati mu Kana wa ku Galileya. Amayi ake a Yesu anali komweko, ndipo Yesu ndi ophunzira ake anayitanidwanso ku ukwatiwo. Vinyo atatha, amayi a Yesu anati kwa Iye, “Wawathera vinyo.”

Yesu anayankha kuti, “Amayi, chifukwa chiyani mukundiwuza Ine? Nthawi yanga sinakwane.”

Amayi ake anati kwa antchito, “Inu muchite chilichonse chimene akuwuzeni.”

Pamenepo panali mitsuko yamiyala yothiramo madzi isanu ndi umodzi, imene Ayuda amagwiritsa ntchito pa mwambo wodziyeretsa. Uliwonse unali ndi malita 100 kapena kupitirirapo.

Yesu anati kwa antchitowo, “Dzazani madzi mʼmitsukoyi,” ndipo iwo anadzaza ndendende.

Ndipo Iye anatinso kwa iwo, “Tsopano tungani ndipo kaperekeni kwa mkulu waphwando.”

Iwo anachita momwemo. Mkulu waphwando analawa madziwo amene anasandulika vinyo, ndipo sanazindikire kumene vinyoyo anachokera, ngakhale kuti antchito amene anatunga madziwo amadziwa. Kenaka anayitanira mkwati pambali 10 ndipo anati, “Aliyense amatulutsa vinyo wokoma kwambiri poyambirira ndipo kenaka vinyo wosakoma pamene oyitanidwa atamwa kale wambiri; koma iwe wasunga wokoma mpaka tsopano.”

11 Ichi chinali chizindikiro chodabwitsa choyamba chimene Yesu anachita ku Kana wa ku Galileya. Potero Iye anawulula ulemerero wake, ndipo ophunzira ake anamukhulupirira Iye.

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero (CCL)

The Word of God in Contemporary Chichewa Copyright © 2002, 2016 by Biblica, Inc.® Used by permission of Biblica, Inc.® All rights reserved worldwide. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Mwini © 2002, 2016 ndi Biblica, Inc.® Kugwiritsa ntchito mwachilolezo. Umwini ndi otetezedwa pa dziko lonse.