Revised Common Lectionary (Semicontinuous)
Yehova Yekha Mpulumutsi wa Israeli
43 Koma tsopano, Yehova
amene anakulenga, iwe Yakobo,
amene anakuwumba, iwe Israeli akuti,
“Usaope, pakuti ndakuwombola;
Ndinakuyitanitsa mokutchula dzina lako, ndiwe wanga.
2 Pamene ukuwoloka nyanja,
ndidzakhala nawe;
ndipo pamene ukuwoloka mitsinje,
sidzakukokolola.
Pamene ukudutsa pa moto,
sudzapsa;
lawi la moto silidzakutentha.
3 Chifukwa Ine Yehova, Mulungu wako,
Woyera wa Israeli, ndine Mpulumutsi wako.
Ndinapereka Igupto pofuna kuti ndiwombole iwe,
ndinapereka Kusi ndi Seba mʼmalo mwa iwe.
4 Popeza kuti ndiwe wamtengowapatali wolemekezeka ndi wapamtima panga,
ndipo chifukwa ndimakukonda,
ndidzapereka anthu mʼmalo mwa iwe,
ndidzapereka mitundu ya anthu pofuna kuwombola moyo wako.
5 Usachite mantha, pakuti Ine ndili nawe;
ndidzabweretsa ana ako kuchokera kummawa,
ndipo ndidzakusonkhanitsani kuchokera kumadzulo.
6 Ndidzawuza a kumpoto kuti, ‘Amasuleni,’
ndidzawuza akummwera kuti, ‘Musawagwire.’
Bweretsani ana anga aamuna kuchokera ku mayiko akutali,
ana anga a akazi kuchokera kumalekezero a dziko lapansi;
7 onsewo amadziwika ndi dzina langa;
ndinawalenga chifukwa cha ulemerero wanga,
ndinawawumba, inde ndinawapanga.”
Salimo la Davide.
29 Perekani kwa Yehova, inu anthu amphamvu,
perekani kwa Yehova ulemerero ndi mphamvu.
2 Perekani kwa Yehova ulemerero woyenera dzina lake,
pembedzani Yehova mwa kukongola kwa chiyero chake.
3 Liwu la Yehova lili pamwamba pa madzi;
Mulungu waulemerero abangula,
Yehova abangula pamwamba pa madzi amphamvu.
4 Liwu la Yehova ndi lamphamvu;
liwu la Yehova ndi laulemerero.
5 Liwu la Yehova limathyola mikungudza;
Yehova amathyolathyola mikungudza ya ku Lebanoni.
6 Iye amachititsa Lebanoni kulumphalumpha ngati mwana wangʼombe,
Siriyoni ngati mwana wa njati:
7 Liwu la Yehova limakantha
ngati kungʼanima kwa mphenzi.
8 Liwu la Yehova limagwedeza chipululu;
Yehova amagwedeza chipululu cha Kadesi.
9 Liwu la Yehova limapindapinda mibawa
ndi kuyeretsa nkhalango.
Ndipo mʼNyumba mwake onse amafuwula kuti, “Ulemerero!”
10 Yehova amakhala pamwamba pa madzi osefukira,
Yehova ndiye mfumu kwamuyaya.
11 Yehova amapereka mphamvu kwa anthu ake;
Yehova amadalitsa anthu ake ndi mtendere.
14 Atumwi a ku Yerusalemu atamva kuti anthu a ku Samariya analandira Mawu a Mulungu, anatumiza Petro ndi Yohane. 15 Atafika anawapempherera kuti alandire Mzimu Woyera, 16 chifukwa Mzimu Woyera anali asanafike pa wina aliyense wa iwo; anali atangobatizidwa mʼdzina la Ambuye Yesu. 17 Ndipo Petro ndi Yohane anasanjika manja awo pa iwo, ndipo analandira Mzimu Woyera.
15 Anthu ankadikira ndi chiyembekezo ndipo ankasinkhasinkha mʼmitima mwawo kuti mwina Yohane nʼkukhala Khristu. 16 Yohane anayankha onse kuti, “Ine ndikubatizani ndi madzi. Koma wina wondiposa ine mphamvu adzabwera amene sindili woyenera kumasula lamba wa nsapato zake. Iyeyu adzakubatizani inu ndi Mzimu Woyera ndi moto. 17 Mʼdzanja lake muli chopetera kuti ayeretse powomberapo tirigu ndi kusonkhanitsa tirigu ndipo adzatentha zotsalira zonse ndi moto wosazimitsika.”
Ubatizo wa Yesu
21 Pamene anthu onse ankabatizidwa, Yesu anabatizidwanso. Ndipo akupemphera, kumwamba kunatsekuka. 22 Mzimu Woyera anatsika pa Iye mumaonekedwe a nkhunda ndipo mawu anamveka kuchokera kumwamba: “Iwe ndiwe Mwana wanga wokondedwa; ndimakondwera nawe.”
The Word of God in Contemporary Chichewa Copyright © 2002, 2016 by Biblica, Inc.® Used by permission of Biblica, Inc.® All rights reserved worldwide. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Mwini © 2002, 2016 ndi Biblica, Inc.® Kugwiritsa ntchito mwachilolezo. Umwini ndi otetezedwa pa dziko lonse.