Print Page Options
Previous Prev Day Next DayNext

Revised Common Lectionary (Semicontinuous)

Daily Bible readings that follow the church liturgical year, with sequential stories told across multiple weeks.
Duration: 1245 days
Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero (CCL)
Version
Masalimo 37:1-17

Salimo la Davide.

37 Usamavutike chifukwa cha anthu oyipa
    kapena kuchitira nsanje amene akuchita cholakwa;
pakuti monga udzu iwo adzafota msanga,
    ngati mbewu zobiriwira adzanyala msanga.

Khulupirira Yehova ndipo uzichita zabwino;
    khazikika mʼdziko ndi kutsata zokhulupirika.
Udzikondweretse wekha mwa Yehova
    ndipo Iye adzakupatsa zokhumba za mtima wako.

Pereka njira yako kwa Yehova;
    dalira Iye ndipo Iyeyo adzachita izi:
Iye adzachititsa chilungamo chako kuwala ngati mʼbandakucha,
    chiweruzo chako ngati dzuwa la masana.

Khala chete pamaso pa Yehova ndipo umudikire mofatsa;
    usavutike pamene anthu apambana mʼnjira zawo,
    pamene iwo achita zinthu zawo zoyipa.

Pewa kupsa mtima ndipo tembenuka kuchoka ku ukali,
    usavutike chifukwa zimenezi zimatsogolera ku zoyipa.
Pakuti anthu oyipa adzachotsedwa,
    koma iwo amene amayembekeza mwa Yehova adzalandira dziko.

10 Kwa kanthawi oyipa sadzapezekanso;
    ngakhale muwafunefune, sadzapezekanso.
11 Koma ofatsa adzalandira dziko
    ndipo adzasangalala ndi mtendere waukulu.

12 Oyipa amakonza chiwembu kutsutsana ndi olungama
    ndipo amawakukutira mano;
13 koma Ambuye amaseka oyipa
    pakuti Iye amadziwa kuti tsiku lawo likubwera.

14 Oyipa amasolola lupanga
    ndi kupinda uta
kugwetsa osauka ndi osowa,
    kupha iwo amene njira zawo ndi zolungama.
15 Koma malupanga awo analasa mitima yawo yomwe,
    ndipo mauta awo anathyoka.

16 Zabwino zochepa zimene olungama ali nazo
    ziposa chuma cha anthu oyipa ambiri;
17 pakuti mphamvu ya oyipa idzasweka,
    koma Yehova amasunga olungama.

Rute 2:1-16

Rute Akumana ndi Bowazi

Naomi anali ndi mʼbale wake wolemera kwambiri wochokera ku banja la mwamuna wake Elimeleki, dzina lake Bowazi.

Tsiku lina Rute, Mmowabu uja anati kwa Naomi, “Mundilole kuti ndikakunkhe barele ku munda wa munthu aliyense amene akandikomere mtima.” Naomi anati kwa iye, “Pita mwana wanga.”

Choncho Rute ananyamuka kupita kukakunkha ku minda yokololedwa kale. Tsono zinangochitika kuti Rute anafika mʼmunda wa Bowazi, yemwe anali wochokera ku banja la Elimeleki.

Posakhalitsa Bowazi anafika kuchokera ku Betelehemu ndipo analonjera okolola aja kuti, “Yehova akhale nanu!”

Iwo anayankha kuti, “Yehova akudalitseni.”

Bowazi anafunsa kapitawo wake amene ankayangʼanira okolola aja kuti, “Mayi uyo ndi ndani?”

Kapitawo uja anayankha kuti, “Mayiyu ndi Mmowabu amene anabwera ndi Naomi kuchokera ku dziko la Mowabu. Iye anandipempha kuti, ‘Chonde mundilole kuti ndikunkhe barele mʼminda moti akololamo kale.’ Iye wakhala akukunkha kuyambira mmawa mpaka tsopano lino osapuma nʼpangʼono pomwe.”

Choncho Bowazi anati kwa Rute, “Tamvera mwana wanga, usapite kukakunkha mʼmunda wina, ndipo usachoke mʼmunda uno. Koma uzitsata adzakazi angawa. Uziyangʼana munda akukolola anyamatawo akamakolola mʼmundamu, ndipo iwe uzitsata pambuyo pawo. Ndawawuza anyamatawo kuti asakuvutitse. Ndipo ukamva ludzu, uzipita ku mitsuko ndi kukamwa madzi amene anyamatawa atunga.”

10 Atamva zimenezi Rute anawerama nazolikitsa nkhope yake pansi. Kenaka anafunsa kuti, “Mwandikomera mtima chotere mlendo ngati ine chifukwa chiyani?”

11 Bowazi anayankha kuti, “Ine ndawuzidwa zonse zimene wakhala ukuchitira apongozi ako chimwalirire mwamuna wako. Ndamvanso kuti unasiya abambo ndi amayi ako komanso dziko la kwanu ndi kubwera kudzakhala ndi anthu amene sumawadziwa ndi kale lonse. 12 Yehova akubwezere pa zimene wachitazi. Yehova Mulungu wa Israeli, amene wabwera pansi pa mapiko ake kuti akuteteze, akupatse mphotho yayikulu.”

13 Rute anati, “Mwandikomera mtima, mbuye wanga. Ndipo mwandisangalatsa ndi kundiyankhula mwa chifundo ngakhale sindili mmodzi mwa adzakazi anu.”

14 Nthawi ya chakudya cha masana Bowazi anati kwa iye, “Bwera kuno, utenge buledi ndi kusunsa nthongo mu vinyo.” Choncho anakhala pansi pafupi ndi okololawo, ndipo Bowazi anamupatsa chakudya ndi nyama yowotcha. Anadya chilichonse amafuna ndipo chakudya china chinatsalako.

15 Atanyamuka kuti azikakunkha, Bowazi analangiza anyamata ake kuti, “Ngakhale mayiyu azikunkha pakati pa mitolo musamuletse ndi kumuchititsa manyazi. 16 Koma muzimusololerako ngala zina za mʼmitolo ndi kumusiyira kuti azikunkha ndipo musamukalipire.”

Yakobo 5:1-6

Chenjezo kwa Achuma Opondereza Anzawo

Tsono tamverani, inu anthu achuma, lirani ndi kufuwula chifukwa cha zovuta zimene zidzakugwereni. Chuma chanu chawola ndipo njenjete zadya zovala zanu. Golide ndi siliva wanu zachita dzimbiri. Dzimbirilo lidzakhala umboni wokutsutsani ndi kuwononga mnofu wanu ngati moto. Mwadziwunjikira chuma pa masiku ano otsiriza. Taonani, ndalama za malipiro zimene munakanika kulipira aganyu aja ankasenga mʼmunda mwanu zikulira mokutsutsani. Kulira kwa okololawo kwamveka mʼmakutu mwa Ambuye Wamphamvuzonse. Mwakhala pa dziko lapansi pano moyo ofewa ndipo mwalidyera dziko lapansi. Mwadzinenepetsa pa tsiku lokaphedwa. Mwaweruza kuti ndi wolakwa ndipo mwapha munthu wosalakwa, amene sakutsutsana nanu.

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero (CCL)

The Word of God in Contemporary Chichewa Copyright © 2002, 2016 by Biblica, Inc.® Used by permission of Biblica, Inc.® All rights reserved worldwide. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Mwini © 2002, 2016 ndi Biblica, Inc.® Kugwiritsa ntchito mwachilolezo. Umwini ndi otetezedwa pa dziko lonse.