Print Page Options
Previous Prev Day Next DayNext

Revised Common Lectionary (Semicontinuous)

Daily Bible readings that follow the church liturgical year, with sequential stories told across multiple weeks.
Duration: 1245 days
Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero (CCL)
Version
Masalimo 15

Salimo la Davide.

15 Yehova, ndani angathe kukhala mʼmalo anu opatulika?
    Kodi ndani angathe kukhala mʼphiri lanu loyera?

Munthu wa makhalidwe abwino,
    amene amachita zolungama,
woyankhula choonadi chochokera mu mtima mwake,
    ndipo mʼkamwa mwake simutuluka mawu osinjirira,
amene sachitira choyipa mnansi wake
    kapena kufalitsa mbiri yoyipa ya munthu mnzake,
amene sapereka ulemu kwa munthu woyipa.
    Koma amalemekeza amene amaopa Yehova,
amene amakwaniritsa zomwe walonjeza
    ngakhale pamene zikumupweteka,
amene amakongoletsa ndalama zake popanda chiwongoladzanja
    ndipo salandira chiphuphu pofuna kutsutsa anthu osalakwa.

Iye amene amachita zinthu zimenezi
    sadzagwedezeka konse.

Deuteronomo 24:17-25:4

17 Musachitire mlendo kapena mwana wamasiye zoyipa, kapena kulanda mkazi wamasiye chovala ngati chikole cha ngongole. 18 Kumbukirani kuti munali akapolo mʼdziko la Igupto ndipo Yehova Mulungu wanu anakuwombolani kumeneko. Nʼchifukwa chake ndikukulamulani kuti muzichita zimenezi.

19 Mukamakolola mʼmunda mwanu ndipo zokolola zina zikasiyidwa, musamabwerere kukazitola. Muzilekere alendo, ana ndi akazi amasiye, kuti Yehova Mulungu wanu akudalitseni pa zochita zanu zonse. 20 Mukathyola zipatso mu mtengo wa olivi, musamabwererenso kachiwiri ku mtengo womwewo. Zotsalazo zilekereni alendo, ana ndi akazi amasiye. 21 Mukakolola mphesa mʼmunda mwanu musamabwereremonso kachiwiri. Zotsalazo muzilekere alendo, ana ndi akazi amasiye. 22 Kumbukirani kuti munali akapolo mʼdziko la Igupto. Nʼchifukwa chake ndikukulamulani kuti muzichita zimenezi.

25 Anthu akasemphana mawu, ayenera kupita ku bwalo la milandu ndipo woweruza adzaweruza mlanduwo. Adzamasula wosalakwa nalanga wolakwa. Munthu akapezeka wolakwa ayenera kukwapulidwa, woweruza amugoneke pansi wolakwayo ndipo akwapulidwe pamaso pake zikoti zochuluka molingana ndi mlandu wake, koma asamukwapule zikoti zopitirira makumi anayi. Akakwapulidwa kupitirira apo ndiye kuti mʼbale wanuyo anyozeka pamaso panu.

Musamange ngʼombe pakamwa pamene ikupuntha tirigu.

1 Timoteyo 5:17-24

17 Akulu ampingo amene amayangʼanira bwino zochitika za mu mpingo, ndi oyenera ulemu wowirikiza, makamaka amene ntchito yawo ndi kulalikira ndi kuphunzitsa. 18 Pakuti Mawu a Mulungu amati, “Musamange ngʼombe pakamwa pamene ikupuntha tirigu,” ndi “Wantchito ngoyenera kulandira malipiro ake.” 19 Usamamvere mawu oneneza akulu ampingo pokhapokha patakhala mboni ziwiri kapena zitatu. 20 Akulu ampingo amene akuchimwa, uwadzudzule poyera kuti ena aphunzirepo.

21 Ndikukulamulira pamaso pa Mulungu, pamaso pa Yesu Khristu ndi pamaso pa angelo osankhika, kuti usunge malangizowa mosachotsera ndipo usachite kalikonse mokondera.

22 Usafulumire kusanjika manja munthu, ndipo usavomerezane ndi anthu ena pa machimo. Usunge bwino kuyera mtima kwako.

23 Uleke kumangomwa madzi okha, koma uzimwako vinyo pangʼono chifukwa cha vuto lako la mʼmimba ndi kudwala kwako kwa pafupipafupi.

24 Anthu ena machimo awo amaonekeratu poyera, amakafika pa mpando wachiweruzo eni akewo asanakafike. Machimo a anthu ena amabwera mʼmbuyo mwawo.

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero (CCL)

The Word of God in Contemporary Chichewa Copyright © 2002, 2016 by Biblica, Inc.® Used by permission of Biblica, Inc.® All rights reserved worldwide. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Mwini © 2002, 2016 ndi Biblica, Inc.® Kugwiritsa ntchito mwachilolezo. Umwini ndi otetezedwa pa dziko lonse.