Print Page Options
Previous Prev Day Next DayNext

Revised Common Lectionary (Semicontinuous)

Daily Bible readings that follow the church liturgical year, with sequential stories told across multiple weeks.
Duration: 1245 days
Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero (CCL)
Version
Masalimo 40:1-11

Kwa mtsogoleri wa mayimbidwe. Salimo la Davide.

40 Mofatsa ndinadikira Yehova
    Iye anatembenukira kwa ine ndipo anamva kulira kwanga.
Ananditulutsa mʼdzenje lachitayiko,
    mʼthope ndi mʼchithaphwi;
Iye anakhazikitsa mapazi anga pa thanthwe
    ndipo anandipatsa malo oyimapo olimba.
Iye anayika nyimbo yatsopano mʼkamwa mwanga,
    nyimbo yamatamando kwa Mulungu wanga.
Ambiri adzaona,
    nadzaopa ndipo adzakhulupirira Yehova.

Ndi wodala munthu
    amakhulupirira Yehova;
amene sayembekezera kwa odzikuza,
    kapena kwa amene amatembenukira kwa milungu yabodza.
Zambiri, Yehova Mulungu wanga,
    ndi zodabwitsa zimene Inu mwachita.
Zinthu zimene munazikonzera ife
    palibe amene angathe kukuwerengerani.
Nditati ndiyankhule ndi kufotokozera,
    zidzakhala zambiri kuzifotokoza.

Nsembe ndi zopereka Inu simuzifuna,
    koma makutu anga mwawatsekula;
zopereka zopsereza ndi zopereka chifukwa cha tchimo
    Inu simunazipemphe.
Kotero ndinati, “Ndili pano, ndabwera.
    Mʼbuku mwalembedwa za ine.
Ndikufuna kuchita chifuniro chanu, Inu Mulungu wanga;
    lamulo lanu lili mu mtima mwanga.”

Ndikulalikira uthenga wa chilungamo chanu mu msonkhano waukulu;
    sinditseka milomo yanga
    monga mukudziwa Inu Yehova.
10 Sindibisa chilungamo chanu mu mtima mwanga;
    ndinayankhula za kukhulupirika kwanu ndi chipulumutso chanu.
Ine sindiphimba chikondi chanu ndi choonadi chanu
    pa msonkhano waukulu.

11 Musandichotsere chifundo chanu Yehova;
    chikondi chanu ndi choonadi chanu zinditeteze nthawi zonse.

Yesaya 22:15-25

15 Chimene Ambuye, Yehova Wamphamvuzonse akuti,

“Pita, ukanene kwa Sabina kapitawo,
    amene amayangʼanira nyumba yaufumu:
16 Kodi ukuchita chiyani kuno, nanga ndani anakupatsa chilolezo
    kuti udzikumbire manda kuno,
kudzikumbira manda pa phiri
    ndi kudzisemera malo opumulira mʼthanthwe?

17 “Samalira, Yehova watsala pangʼono kukugwira zolimba
    ndi kukuponya mwamphamvu, iwe munthu wamphamvu.
18 Iye adzakukulunga kwambiri ngati mpira
    ndipo adzakuponyera mʼdziko lalikulu.
Kumeneko ndiko ukafere
    ndipo kumeneko ndiko kudzatsalire magaleta ako.
    Ndipo udzasanduka wochititsa manyazi nyumba ya mbuye wako.
19 Ine ndidzakuchotsa pa ukapitawo wako
    ndipo ndidzakutsitsa pa udindo wako.

20 “Tsiku limenelo ndidzayitanitsa mtumiki wanga, Eliyakimu mwana wa Hilikiya. 21 Ndidzamuveka mkanjo wako ndi kumangira lamba wako mʼchiwuno mwake ndi kumupatsa ulamuliro wako. Iye adzakhala kholo la amene amakhala mu Yerusalemu ndiponso a fuko la Yuda. 22 Ndidzamupatsa ulamuliro wa banja la Davide. Adzatsekula ndipo palibe adzatseke, adzatseka popanda wina kutsekula. 23 Ufumu wake udzakhala wokhazikika ngati chikhomo chokhomedwa pa malo olimba. Anthu adzalemekeza nyumba ya abale ake chifukwa cha iye. 24 Ana ndi abale a nyumba ya abambo ake adzakhala ngati katundu pa iye ngati ziwiya zopanda ntchito zimene zapachikidwa pa chikhomo.

25 “Yehova Wamphamvuzonse akunena kuti, ‘Tsiku limeneli chikhomo chokhomedwa kwambiri chija sichidzalimbanso; chidzazuka ndipo chidzagwa ndipo zonse zopachikidwa zidzawonongedwa.’ ” Yehova wayankhula chomwechi.

Agalatiya 1:6-12

Uthenga Wabwino ndi Umodzi Wokha

Ine ndikudabwa kuti mukusiya mwamsangamsanga chotere Mulungu amene anakuyitanani mwachisomo cha Khristu ndipo mwatembenuka ndi kutsatira uthenga wina wosiyana, umene si Uthenga Wabwino konse. Pali anthu ena amene akukusokonezani komanso akufuna kupotoza Uthenga Wabwino wa Khristu. Ngakhale ife kapena mngelo wochokera kumwamba, akalalikira Uthenga Wabwino wosiyana ndi umene tinakulalikirani uja, iyeyo akhale wotembereredwa! Monga tanena kale, tsopano ndikubwereza kunenanso kuti, “Ngati wina aliyense akulalikirani Uthenga Wabwino wosiyana ndi umene munawulandira, iyeyo akhale wotembereredwa.”

10 Kodi tsopano ndikufuna kukopa anthu kuti andivomereze, kapena Mulungu? Kapena ndikufuna kukondweretsa anthu? Ngati ine ndikanakhala kuti ndikufunabe kukondweretsa anthu, sindikanakhala mtumiki wa Khristu.

Paulo Woyitanidwa ndi Mulungu

11 Abale, ine ndikufuna kuti mudziwe, kuti Uthenga Wabwino umene ndinalalikira si ochokera kwa munthu ayi. 12 Ine sindinawulandire kuchokera kwa munthu aliyense, kapena kuphunzitsidwa; koma ndinawulandira mwa vumbulutso lochokera kwa Khristu.

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero (CCL)

The Word of God in Contemporary Chichewa Copyright © 2002, 2016 by Biblica, Inc.® Used by permission of Biblica, Inc.® All rights reserved worldwide. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Mwini © 2002, 2016 ndi Biblica, Inc.® Kugwiritsa ntchito mwachilolezo. Umwini ndi otetezedwa pa dziko lonse.