Revised Common Lectionary (Semicontinuous)
Ufumu wa Mesiya
9 Anthu amene anali ndi nkhawa, sadzakhalanso otaya mtima. Masiku amakedzana Mulungu ananyozetsa dziko la Zebuloni ndi dziko la Nafutali, koma kutsogolo kuno dera lonse la Galileya, limene lili dziko la anthu a mitundu ina, kuyambira ku nyanja yayikulu, mʼmbali mwa Yorodani, adzalisandutsa laulemu.
2 Anthu oyenda mu mdima
awona kuwala kwakukulu;
kwa iwo okhala mʼdziko la mdima wandiweyani
kuwunika kwawafikira.
3 Inu mwauchulukitsa mtundu wanu
ndipo mwawonjezera chimwemwe chawo.
Iwo akukondwa pamaso panu,
ngati mmene anthu amakondwera nthawi yokolola,
ngatinso mmene anthu amakondwera
pamene akugawana zolanda ku nkhondo.
4 Monga munachitira pogonjetsa Amidiyani,
inu mwathyola goli
limene limawalemera,
ndodo zimene amamenyera mapewa awo,
ndiponso mikwapulo ya anthu owazunza.
Salimo la Davide.
27 Yehova ndiye kuwunika kwanga ndi chipulumutso changa;
ndidzaopa yani?
Yehova ndi linga la moyo wanga;
ndidzachita mantha ndi yani?
4 Chinthu chimodzi chokha chimene ndipempha kwa Yehova,
ichi ndi chimene ndidzachifunafuna:
kuti ndikhale mʼNyumba ya Yehova
masiku onse a moyo wanga,
ndi kuyangʼana kukongola kwa Yehova,
ndi kumufunafuna Iye mʼNyumba yake.
5 Pakuti pa tsiku la msautso
Iye adzanditeteza mʼmalo ake okhalamo;
adzandibisa mʼkati mwa Nyumba yake
ndi kukhazika ine pamwamba pa thanthwe.
6 Kotero mutu wanga udzakwezedwa
kuposa adani anga amene andizungulira;
pa Nyumba yake ndidzapereka nsembe ndi mfuwu wachimwemwe;
ndidzayimba nyimbo kwa Yehova.
7 Imvani mawu anga pamene ndiyitana Inu Yehova
mundichitire chifundo ndipo mundiyankhe.
8 Mtima wanga ukuti kwa Inu, “Funafuna nkhope yake!”
Nkhope yanu Yehova ndidzayifunafuna.
9 Musandibisire nkhope yanu,
musamubweze mtumiki wanu mwamkwiyo;
mwakhala muli thandizo langa.
Musandikane kapena kunditaya,
Inu Mulungu Mpulumutsi wanga.
Kugawikana mu Mpingo
10 Ndidandaulira inu, abale, mʼdzina la Ambuye athu Yesu Khristu kuti nonsenu muvomerezane wina ndi mnzake kuti pasakhale kugawikana pakati panu ndi kuti mukhale amodzi kwenikweni mu nzeru ndi mʼmaganizo. 11 Abale anga, ena a ku nyumba ya Kloe andidziwitsa kuti pali mkangano pakati panu. 12 Chimene ndikutanthauza ndi ichi: wina amati, “Ndimatsatira Paulo,” wina, “Ndimatsatira Apolo,” wina, “Ndimatsatira Kefa,” winanso, “Ndimatsatira Khristu.”
13 Kodi Khristu wagawikana? Kodi Paulo anapachikidwa pa mtanda chifukwa cha inu? Kodi munabatizidwa mʼdzina la Paulo? 14 Ine ndikuyamika kuti sindinabatizepo mmodzi mwa inu kupatula Krispo ndi Gayo, 15 mwakuti palibe amene anganene kuti anabatizidwa mʼdzina langa. 16 (Inde, ine ndinabatizanso a mʼbanja la Stefano, koma sindikumbukira ngati ndinabatizanso wina aliyense). 17 Pakuti Khristu sananditume ine kudzabatiza, koma kudzalalikira Uthenga Wabwino, osati ndi mawu anzeru za umunthu, kuopa kuti mtanda wa Khristu ungakhale wopanda mphamvu.
Khristu ndiye Nzeru ndi Mphamvu za Mulungu
18 Pakuti uthenga wa mtanda ndi chopusa kwa iwo amene akuwonongeka, koma kwa ife amene tikupulumutsidwa uthengawu ndi mphamvu ya Mulungu.
Yesu Ayamba Kulalikira
12 Yesu atamva kuti Yohane anamutsekera mʼndende, anabwerera ku Galileya. 13 Ndipo atachoka ku Nazareti anapita ku Kaperenawo ndi kukhala mʼmbali mwa nyanja, mʼdera la Zebuloni ndi Nafutali; 14 pokwaniritsa zimene zinanenedwa kudzera mwa mneneri Yesaya kuti,
15 “Dziko la Zebuloni ndi dziko la Nafutali,
njira ya ku nyanja, kutsidya lija la Yorodani,
Galileya wa anthu a mitundu ina,
16 anthu okhala mu mdima
awona kuwala kwakukulu;
ndi kwa iwo okhala mʼdziko la mthunzi wa imfa
kuwunika kwawafikira.”
17 Kuyambira nthawi imeneyo, Yesu anayamba kulalikira nati, “Tembenukani mtima ufumu wakumwamba wayandikira.”
Yesu Ayitana Ophunzira ake Oyamba
18 Pamene Yesu ankayenda mʼmbali mwa nyanja ya Galileya, anaona abale awiri, Simoni wotchedwa Petro ndi mʼbale wake Andreya akuponya khoka mʼnyanja popeza anali asodzi. 19 Yesu anati, “Bwerani, tsateni Ine ndipo ndidzakusandutsani asodzi a anthu.” 20 Nthawi yomweyo anasiya makoka awo namutsata Iye.
21 Atapita patsogolo, anaona abale ena awiri, Yakobo ndi mʼbale wake Yohane ana a Zebedayo. Iwowa anali mʼbwato ndi abambo awo, Zebedayo, akukonza makoka awo ndipo Yesu anawayitana. 22 Nthawi yomweyo anasiya bwato ndi abambo awo namutsata Iye.
Yesu Achiritsa Odwala
23 Yesu anayendayenda mu Galileya kuphunzitsa mʼmasunagoge awo, nalalikira Uthenga Wabwino wa ufumu ndi kuchiritsa matenda onse pakati pa anthu.
The Word of God in Contemporary Chichewa Copyright © 2002, 2016 by Biblica, Inc.® Used by permission of Biblica, Inc.® All rights reserved worldwide. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Mwini © 2002, 2016 ndi Biblica, Inc.® Kugwiritsa ntchito mwachilolezo. Umwini ndi otetezedwa pa dziko lonse.