Print Page Options
Previous Prev Day Next DayNext

Revised Common Lectionary (Semicontinuous)

Daily Bible readings that follow the church liturgical year, with sequential stories told across multiple weeks.
Duration: 1245 days
Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero (CCL)
Version
Yesaya 49:1-7

Mtumiki wa Yehova

49 Mverani Ine, inu anthu a pa zilumba
    tcherani khutu, inu anthu a mayiko akutali:
Yehova anandiyitana ine ndisanabadwe,
    ananditchula dzina ndili mʼmimba ya amayi anga.
Iye anasandutsa pakamwa panga kukhala ngati lupanga lakuthwa,
    anandibisa mu mthunzi wa dzanja lake;
Iye anandisandutsa ngati muvi wakuthwa
    ndipo anandibisa mʼchimake.
Iye anati kwa ine, “Ndiwe mtumiki wanga, Israeli.
    Anthu adzanditamanda chifukwa cha iwe.”
Koma Ine ndinati, “Ine ndinkaganiza kuti ndinagwira ntchito
    ndi kuwononga mphamvu zanga pachabe,
koma ayi, zondiyenera zili mʼmanja a Yehova,
    ndipo mphotho yanga ili mʼmanja mwa Mulungu wanga.”

Yehova anandiwumba ine
    mʼmimba mwa amayi anga kuti ndikhale mtumiki wake
kuti ndibweze fuko la Yakobo kwa Iye
    ndi kusonkhanitsa Israeli kwa Iye,
choncho ndimalemekezeka mʼmaso mwa Yehova,
    ndipo ndimapeza mphamvu mwa Mulungu wanga.
Yehovayo tsono akuti,
“Nʼchinthu chochepa kwambiri kwa iwe kuti ukhale mtumiki wanga,
    kuti udzutse mafuko a Yakobo
    ndi kuwabweretsa kwawo Aisraeli amene anapulumuka.
Choncho iwe udzakhala ngati chowunikira,
    udzafikitsa uthenga wa chipulumutso changa ku mathero a dziko lapansi.”

Yehova Mpulumutsi ndi Woyerayo wa Israeli akuyankhula,
    Woyerayo wa Israeli akunena,
amene mitundu ya anthu inamuda,
    amenenso anali kapolo wa mafumu ankhanza uja kuti,
“Mafumu adzaona ntchito ya chipulumutso changa ndipo adzayimirira.
    Akalonga nawonso adzagwada pansi.
Zimenezi zidzachitika chifukwa cha Yehova amene ndi wokhulupirika
    ndi Woyerayo wa Israeli amene wakusankha iwe.”

Masalimo 40:1-11

Kwa mtsogoleri wa mayimbidwe. Salimo la Davide.

40 Mofatsa ndinadikira Yehova
    Iye anatembenukira kwa ine ndipo anamva kulira kwanga.
Ananditulutsa mʼdzenje lachitayiko,
    mʼthope ndi mʼchithaphwi;
Iye anakhazikitsa mapazi anga pa thanthwe
    ndipo anandipatsa malo oyimapo olimba.
Iye anayika nyimbo yatsopano mʼkamwa mwanga,
    nyimbo yamatamando kwa Mulungu wanga.
Ambiri adzaona,
    nadzaopa ndipo adzakhulupirira Yehova.

Ndi wodala munthu
    amakhulupirira Yehova;
amene sayembekezera kwa odzikuza,
    kapena kwa amene amatembenukira kwa milungu yabodza.
Zambiri, Yehova Mulungu wanga,
    ndi zodabwitsa zimene Inu mwachita.
Zinthu zimene munazikonzera ife
    palibe amene angathe kukuwerengerani.
Nditati ndiyankhule ndi kufotokozera,
    zidzakhala zambiri kuzifotokoza.

Nsembe ndi zopereka Inu simuzifuna,
    koma makutu anga mwawatsekula;
zopereka zopsereza ndi zopereka chifukwa cha tchimo
    Inu simunazipemphe.
Kotero ndinati, “Ndili pano, ndabwera.
    Mʼbuku mwalembedwa za ine.
Ndikufuna kuchita chifuniro chanu, Inu Mulungu wanga;
    lamulo lanu lili mu mtima mwanga.”

Ndikulalikira uthenga wa chilungamo chanu mu msonkhano waukulu;
    sinditseka milomo yanga
    monga mukudziwa Inu Yehova.
10 Sindibisa chilungamo chanu mu mtima mwanga;
    ndinayankhula za kukhulupirika kwanu ndi chipulumutso chanu.
Ine sindiphimba chikondi chanu ndi choonadi chanu
    pa msonkhano waukulu.

11 Musandichotsere chifundo chanu Yehova;
    chikondi chanu ndi choonadi chanu zinditeteze nthawi zonse.

1 Akorinto 1:1-9

Paulo, woyitanidwa mwachifuniro cha Mulungu kuti akhale mtumwi wa Khristu Yesu ndi mʼbale wathu Sositene.

Kupita ku mpingo wa Mulungu ku Korinto, kwa oyeretsedwa mwa Khristu Yesu ndi oyitanidwa kukhala opatulika ndiponso kwa onse amene amapemphera mʼdzina la Ambuye athu Yesu Khristu mʼdziko lonse lapansi, amene ndi Ambuye wawo ndi wathunso.

Landirani chisomo ndi mtendere zochokera kwa Mulungu Atate athu ndi Ambuye athu Yesu Khristu.

Kuthokoza

Nthawi zonse ndimayamika Mulungu chifukwa cha inu chifukwa cha chisomo chake chopatsidwa kwa inu mwa Khristu Yesu. Pakuti mwa Iye mwalemekezedwa mʼnjira iliyonse, mʼkuyankhula kwanu konse ndi mʼkudziwa kwanu konse, chifukwa umboni wathu pa za Khristu unatsimikizidwa mwa inu. Choncho inu simusowa mphatso yauzimu iliyonse pamene mukudikira mofunitsitsa kuti Ambuye athu Yesu Khristu avumbulutsidwe. Adzakulimbikitsani mpaka kumapeto kuti mudzakhale wopanda mlandu pa tsiku lobwera Ambuye athu Yesu Khristu. Mulungu amene wakuyitanani inu mu chiyanjano ndi Mwana wake Yesu Khristu Ambuye athu ngokhulupirika.

Yohane 1:29-42

Yesu Mwana Wankhosa wa Mulungu

29 Pa tsiku lotsatira Yohane anaona Yesu akubwera kwa iye ndipo anati, “Taonani, Mwana Wankhosa wa Mulungu, amene achotsa tchimo la dziko lapansi! 30 Uyu ndi amene ndimatanthauza pamene ndinanena kuti, ‘Munthu amene akubwera pambuyo panga ndi wondiposa ine chifukwa analipo ine ndisanabadwe.’ 31 Ine mwini sindinamudziwe Iye, koma ndinabwera kubatiza ndi madzi kuti Iye adziwike mu Israeli.”

32 Kenaka Yohane anapereka umboni uwu: “Ine ndinaona Mzimu Woyera ngati nkhunda kuchokera kumwamba nakhala pa Iye. 33 Ine sindikanamudziwa Iye, koma kuti amene anandituma ine kudzabatiza ndi madzi anati kwa ine, ‘Munthu amene udzaona Mzimu Woyera akutsika nakhazikika pa Iye ndi amene adzabatize ndi Mzimu Woyera.’ 34 Ine ndaona ndipo ndikuchitira umboni kuti uyu ndi Mwana wa Mulungu.”

Ophunzira Oyamba a Yesu

35 Pa tsiku lotsatira Yohane analinso pamenepo pamodzi ndi awiri a ophunzira ake. 36 Iye ataona Yesu akudutsa anati, “Taonani Mwana Wankhosa wa Mulungu!”

37 Ophunzira ake awiriwo atamva iye akunena izi, iwo anamutsatira Yesu. 38 Atatembenuka, Yesu anaona iwo akumutsatira ndipo anawafunsa kuti, “Kodi mukufuna chiyani?”

Iwo anati, “Rabi (kutanthauza kuti Aphunzitsi), kodi mukukhala kuti?”

39 Iye anayankha kuti, “Bwerani mudzaone.”

Choncho iwo anapita ndi kukaona kumene Iye amakhala, ndipo anakhala naye tsiku limenelo. Linali ngati pafupifupi ora la khumi.

40 Andreya mʼbale wake wa Simoni Petro, anali mmodzi wa awiriwo amene anamva zimene Yohane ananena ndiponso amene anamutsata Yesu. 41 Choncho chimene Andreya anachita ndi kukapeza mʼbale wake Simoni ndipo anamuwuza kuti, “Ife tamupeza Mesiya,” (kutanthauza kuti Khristu).

42 Kenaka iye anabweretsa Simoni kwa Yesu, amene anamuyangʼana ndipo anati, “Iwe ndiwe Simoni, mwana wa Yohane. Udzatchedwa Kefa” (limene litanthauza kuti Petro).

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero (CCL)

The Word of God in Contemporary Chichewa Copyright © 2002, 2016 by Biblica, Inc.® Used by permission of Biblica, Inc.® All rights reserved worldwide. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Mwini © 2002, 2016 ndi Biblica, Inc.® Kugwiritsa ntchito mwachilolezo. Umwini ndi otetezedwa pa dziko lonse.