Print Page Options
Previous Prev Day Next DayNext

Revised Common Lectionary (Semicontinuous)

Daily Bible readings that follow the church liturgical year, with sequential stories told across multiple weeks.
Duration: 1245 days
Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero (CCL)
Version
Masalimo 72

Salimo la Solomoni.

72 Patsani mwana wa mfumu nzeru zanu zoweruzira mwa chilungamo,
    Inu Mulungu mupatseni mwana wa mfumu chilungamo chanu.
Iye adzaweruza anthu anu mwachilungamo,
    anthu anu ozunzika mosakondera.
Mapiri adzabweretsa chuma kwa anthu anu,
    timapiri tidzabweretsa zipatso zachilungamo.
Iye adzateteza ozunzika pakati pa anthu
    ndi kupulumutsa ana a anthu osowa;
    adzaphwanya ozunza anzawo.

Adzakhala ndi moyo pa mibado yonse,
    nthawi zonse pamene dzuwa ndi mwezi zikuwala.
Iye adzakhala kugwa kwa mvula pa minda yolimidwa
    ngati mivumbi yothirira dziko lapansi.
Mʼmasiku a munthu wolungama adzakhazikika;
    chuma chidzachuluka mpaka mwezi utaleka kuwala.

Iye adzalamulira kuchokera ku nyanja ina mpaka ku nyanja ina
    ndiponso kuchokera ku mtsinje mpaka ku malekezero a dziko lapansi.
Mafuko a mʼchipululu adzawerama pamaso pake
    ndipo adani ake adzanyambita fumbi.
10 Mafumu a ku Tarisisi ndi a ku zilumba zakutali
    adzabweretsa mitulo kwa iye,
mafumu a ku Seba ndi Seba
    adzapereka mphatso kwa iyeyo.
11 Mafumu onse adzamuweramira
    ndipo mitundu yonse idzamutumikira.

12 Pakuti iye adzawombola wosowa amene akulira,
    wozunzika amene alibe wina womuthandiza.
13 Iye adzachitira chifundo anthu ofowoka ndi anthu osowa
    ndi kupulumutsa osowa ku imfa.
14 Iye adzalanditsa iwo ku mazunzo ndi chiwawa
    pakuti magazi awo ndi amtengo wapatali pamaso pake.

15 Iye akhale ndi moyo wautali;
    golide ochokera ku Seba apatsidwe kwa iye.
Anthu amupempherere nthawi zonse
    ndi kumudalitsa tsiku lonse.
16 Mulole kuti tirigu achuluke mʼdziko lonse;
    pamwamba pa mapiri pakhale tirigu.
Zipatso zake zichuluke ngati za ku Lebanoni;
    zichuluke ngati udzu wakuthengo
17 Dzina lake likhazikike kwamuyaya,
    lipitirire kukhala monga momwe limakhalira dzuwa.

Mitundu yonse idzadalitsika kudzera mwa iye
    ndipo iwo adzamutcha iye wodala.

18 Matamando akhale kwa Yehova Mulungu, Mulungu wa Israeli
    amene Iye yekha amachita ntchito zodabwitsa.
19 Matamando akhale ku dzina lake laulemerero kwamuyaya
    dziko lonse lapansi lidzaze ndi ulemerero wake.
            Ameni ndi Ameni.

20 Uku ndiko kumaliza kwa mapemphero a Davide mwana wa Yese.

Eksodo 3:1-5

Kuyitanidwa kwa Mose pa Chitsamba Choyaka Moto

Tsono Mose amaweta ziweto za mpongozi wake Yetero, wansembe uja wa ku Midiyani. Tsiku lina iye anazitsogolera kupita ku chipululu ndipo anafika ku phiri la Mulungu lotchedwa Horebu. Kumeneko mngelo wa Yehova anaonekera kwa iye mʼmalawi amoto mʼchitsamba. Mose anaona kuti ngakhale chitsambacho chimayaka koma sichimanyeka. Tsono Mose anati mu mtima mwake, “Ine ndipita komweko ndikaone zodabwitsazi, chitsamba sichikunyeka chifukwa chiyani?”

Yehova ataona kuti Mose anapatuka kuti adzaonetsetse, Mulungu anamuyitana Mose kuchokera mʼchitsambamo nati, “Mose! Mose!”

Ndipo anayankha, “Wawa.”

Mulungu anati, “Usayandikire kuno. Vula nsapato zako, pakuti malo amene wayimapo ndi opatulika.”

Ahebri 11:23-31

23 Ndi chikhulupiriro Mose atabadwa makolo ake anamubisa miyezi itatu, chifukwa iwo anaona kuti mwanayo anali wokongola ndipo sanaope konse lamulo la mfumu.

24 Ndi chikhulupiriro Mose atakula, anakana kutchedwa mwana wa mwana wamkazi wa Farao. 25 Iye anasankha kuzunzika nawo limodzi anthu a Mulungu kuposa kusangalala ndi zokondweretsa za uchimo kwa nthawi yochepa. 26 Anaona kuti kuzunzika chifukwa cha Khristu kunali kwa mtengowapatali kuposa chuma cha ku Igupto, chifukwa amaona mphotho ya mʼtsogolo. 27 Ndi chikhulupiriro anachoka ku Igupto wosaopa ukali wa mfumu. Iye anapirira chifukwa anamuona Mulungu amene ndi wosaonekayo. 28 Ndi chikhulupiriro anachita Paska ndi kuwaza magazi, kuti mngelo wowononga ana oyamba kubadwa asaphe ana oyamba kubadwa a Aisraeli.

29 Ndi chikhulupiriro Aisraeli anawoloka Nyanja Yofiira ngati pa mtunda powuma, koma Aigupto atayesa kutero anamizidwa.

30 Ndi chikhulupiriro mpanda wa Yeriko unagwa, Aisraeli atawuzungulira kasanu ndi kawiri.

31 Ndi chikhulupiriro Rahabe, mkazi wadama sanaphedwe pamodzi ndi osamvera aja chifukwa analandira bwino ozonda aja ku nyumba kwake.

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero (CCL)

The Word of God in Contemporary Chichewa Copyright © 2002, 2016 by Biblica, Inc.® Used by permission of Biblica, Inc.® All rights reserved worldwide. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Mwini © 2002, 2016 ndi Biblica, Inc.® Kugwiritsa ntchito mwachilolezo. Umwini ndi otetezedwa pa dziko lonse.