Print Page Options
Previous Prev Day Next DayNext

Revised Common Lectionary (Semicontinuous)

Daily Bible readings that follow the church liturgical year, with sequential stories told across multiple weeks.
Duration: 1245 days
Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero (CCL)
Version
Masalimo 89:20-37

20 Ndamupeza mtumiki wanga Davide;
    ndamudzoza ndi mafuta opatulika.
21 Dzanja langa lidzamuchirikiza;
    zoonadi, mkono wanga udzamupatsa mphamvu.
22 Adani sadzamulamula kuti apereke msonkho;
    anthu oyipa sadzamusautsa.
23 Ndidzaphwanya adani ake pamaso pake
    ndi kukantha otsutsana naye.
24 Chikondi changa chokhulupirika chidzakhala naye,
    ndipo kudzera mʼdzina langa nyanga yake idzakwezedwa.
25 Ndidzayika dzanja lake pa nyanja,
    dzanja lake lamanja pa mitsinje.
26 Iyeyo adzafuwula kwa Ine kuti, ‘Ndinu Atate anga,
    Mulungu wanga, Thanthwe ndi Chipulumutso changa.’
27 Ndidzamuyika kuti akhale mwana wanga woyamba kubadwa;
    wokwezedwa kwambiri pakati pa mafumu a dziko lapansi.
28 Ndidzamusungira chifundo changa kwamuyaya,
    ndipo pangano langa ndi iye silidzatha.
29 Ine ndidzakhazikitsa zidzukulu zake mpaka muyaya,
    mpando wake waufumu ngati masiku a miyamba.

30 “Ngati ana ake adzataya lamulo langa
    ndi kusatsatira malangizo anga,
31 ngati adzaswa malamulo anga
    ndi kulephera kusunga ziphunzitso zanga,
32 Ine ndidzalanga tchimo lawo ndi ndodo,
    mphulupulu zawo powakwapula.
33 Koma sindidzachotsa chikondi changa pa iye,
    kapena kukhala wosakhulupirika kwa iyeyo.
34 Sindidzaswa pangano langa
    kapena kusintha zimene milomo yanga yayankhula.
35 Ndinalumbira kamodzi mwa kuyera kwanga
    ndipo sindidzanama kwa Davide,
36 kuti zidzukulu zake zidzakhale kwamuyaya
    ndipo mpando wake waufumu udzakhazikika pamaso panga ngati dzuwa;
37 udzakhazikika kwamuyaya monga mwezi,
    mboni yokhulupirika mʼmitambo.
            Sela

1 Mbiri 15:1-2

Bokosi la Chipangano Alibweretsa ku Yerusalemu

15 Davide atadzimangira nyumba zina mu Mzinda wa Davide, iye anakonza malo a Bokosi la Mulungu ndipo analimangira tenti. Pamenepo Davide anati, “Palibe wina ati anyamule Bokosi la Mulungu koma Alevi chifukwa Yehova anawasankha kuti azinyamula Bokosi la Yehova ndi kumatumikira pamaso pake nthawi zonse.”

1 Mbiri 16:4-13

Iye anasankha Alevi ena kuti azitumikira pamene panali Bokosi la Yehova, kuti azipemphera, azithokoza ndi kulemekeza Yehova Mulungu wa Israeli. Mtsogoleri wawo anali Asafu, wachiwiri anali Zekariya, kenaka Yeiyeli, Semiramoti, Yehieli, Matitiya, Eliabu, Benaya, Obedi-Edomu ndi Yeiyeli. Iwo amayimba azeze ndi apangwe, Asafu amayimba ziwaya za malipenga, ndipo ansembe Benaya ndi Yahazieli amawomba malipenga nthawi zonse pamaso pa Bokosi la Chipangano la Mulungu.

Nyimbo Yotamanda ya Davide

Tsiku limeneli Davide anayamba nʼkusankha Asafu ndi anzake kuti ndiwo apereke nyimbo iyi ya matamando kwa Yehova:

Yamikani Yehova, itanani dzina lake;
    lalikani za ntchito zake pakati pa mitundu ya anthu.
Imbirani Iye, muyimbireni nyimbo zamatamando;
    nenani za ntchito zake zonse zodabwitsa.
10 Nyadirani dzina lake loyera;
    ikondwere mitima ya iwo akufunafuna Yehova.
11 Dalirani Yehova ndi mphamvu zake;
    funafunani nkhope yake nthawi zonse.
12 Kumbukirani ntchito zodabwitsa wazichita,
    zozizwitsa zake, ndi kuweruza kwa mʼkamwa mwake,
13 inu zidzukulu za Israeli mtumiki wake,
    inu ana a Yakobo, osankhidwa ake.

Luka 18:35-43

Yesu Achiritsa Wosaona

35 Yesu atayandikira ku Yeriko, munthu wina wosaona amene amakhala pambali pa msewu namapempha, 36 anamva gulu la anthu likudutsa. Iye anafunsa chomwe chimachitika. 37 Iwo anamuwuza kuti “Yesu wa ku Nazareti akudutsa.”

38 Iye anayitana mofuwula, “Yesu Mwana wa Davide, mundichitire chifundo!”

39 Iwo amene amamutsogolera njira anamudzudzula ndi kumuwuza kuti akhale chete, koma iye anafuwulabe, “Mwana wa Davide, chitireni chifundo!”

40 Yesu anayima nalamula kuti abwere naye kwa Iye. Atabwera pafupi, Yesu anamufunsa kuti, 41 “Kodi ukufuna kuti ndikuchitire chiyani?”

Iye anayankha kuti, “Ambuye, ine ndifuna ndionenso.”

42 Yesu anati kwa iye, “Onanso; chikhulupiriro chako chakupulumutsa.” 43 Nthawi yomweyo anaonanso ndipo anayamba kumutsatira Yesu, akulemekeza Mulungu. Anthu onse ataona izi, iwonso analemekeza Mulungu.

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero (CCL)

The Word of God in Contemporary Chichewa Copyright © 2002, 2016 by Biblica, Inc.® Used by permission of Biblica, Inc.® All rights reserved worldwide. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Mwini © 2002, 2016 ndi Biblica, Inc.® Kugwiritsa ntchito mwachilolezo. Umwini ndi otetezedwa pa dziko lonse.