Revised Common Lectionary (Semicontinuous)
Nyimbo. Salimo la ana a Kora.
48 Wamkulu ndi Yehova, ndi woyenera kwambiri matamando
mu mzinda wa Mulungu wathu, phiri lake loyera.
2 Lokongola mu utali mwake,
chimwemwe cha dziko lonse lapansi.
Malo aatali kwambiri a Zafoni ndiye Phiri la Ziyoni,
mzinda wa Mfumu yayikulu.
3 Mulungu ali mu malinga ake;
Iye wadzionetsa yekha kuti ndiye malinga akewo.
4 Pamene mafumu anasonkhana pamodzi,
pamene anayendera pamodzi kudzalimbana nafe,
5 iwo anaona mzindawo ndipo anadabwa kwambiri;
anathawa ndi mantha aakulu.
6 Pomwepo anagwidwa nako kunjenjemera,
ululu wonga wa mkazi woyembekezera pa nthawi yochira.
7 Inu munawawononga monga sitima zapamadzi za ku Tarisisi
zitawonongeka ndi mphepo ya kummawa.
8 Monga momwe tinamvera,
kotero ife tinaona
mu mzinda wa Yehova Wamphamvuzonse,
mu mzinda wa Mulungu wathu.
Mulungu adzawuteteza kwamuyaya.
9 Mʼkati mwa Nyumba yanu Mulungu,
ife timalingaliramo zachikondi chanu chosasinthika.
10 Monga dzina lanu, Inu Mulungu,
matamando anu amafika ku malekezero a dziko lapansi
dzanja lanu lamanja ladzaza ndi chilungamo.
11 Phiri la Ziyoni likukondwera,
midzi ya Yuda ndi yosangalala
chifukwa cha maweruzo anu.
12 Yendayendani mu Ziyoni, uzungulireni mzindawo,
werengani nsanja zake.
13 Yangʼanitsitsani bwino mipanda yake,
penyetsetsani malinga ake,
kuti mudzafotokoze za izo ku mʼbado wotsatira.
14 Pakuti Mulungu uyu ndi Mulungu wathu ku nthawi zosatha;
Iye adzakhala mtsogoleri wathu mpaka ku mapeto.
3 Nkhondo ya pakati pa banja la Sauli ndi banja la Davide inachitika nthawi yayitali. Mphamvu za Davide zinkakulirakulirabe, pamene banja la Sauli mphamvu zake zimapita zicheperachepera.
2 Ana aamuna a Davide amene anabadwira ku Hebroni anali awa: Woyamba anali Amnoni, amayi ake anali Ahinoamu wa ku Yezireeli.
3 Mwana wachiwiri anali Kileabu, amayi ake anali Abigayeli mkazi wamasiye wa Nabala wa ku Karimeli.
Wachitatu anali Abisalomu, amayi ake anali Maaka mwana wa Talimai mfumu ya Gesuri;
4 wachinayi anali Adoniya, amayi ake anali Hagiti;
wachisanu, Sefatiya amayi ake anali Abitali;
5 ndipo wachisanu ndi chimodzi anali Itireamu, amayi ake anali Egila, mkazi wa Davide.
Ana awa a Davide anabadwira ku Hebroni.
Abineri Agwirizana ndi Davide
6 Pamene kunali nkhondo pakati pa banja la Sauli ndi banja la Davide, Abineri anayamba kudzipatsa yekha mphamvu pakati pa banja la Sauli. 7 Sauli anali ndi mzikazi dzina lake Rizipa mwana wa Ayiwa. Ndipo Isiboseti anati kwa Abineri, “Nʼchifukwa chiyani unagona ndi mzikazi wa abambo anga?”
8 Abineri anakwiya kwambiri chifukwa cha zimene Isi-Boseti ananena ndipo anamuyankha kuti “Kodi ukuyesa ndine mutu wagalu umene ali mbali ya Ayuda? Lero lino ndine wokhulupirika ku nyumba ya abambo ako, Sauli ndi banja lake ndi anzake. Ine sindinakupereke kwa Davide, koma tsopano ukundinena pa cholakwa chimene ndachita pa mkazi uyu! 9 Mulungu andilange ine Abineri, andilange kwambiri, ngati sindichitira Davide zimene Yehova anamulonjeza iye mwa lumbiro. 10 Ndidzachotsa ufumu ku nyumba ya Sauli ndi kukhazikitsa ufumu wa Davide pa Aisraeli onse ndi Yuda kuchokera ku Dani mpaka ku Beeriseba.” 11 Isiboseti sanayerekezenso kunena mawu ena kwa Abineri, chifukwa ankamuopa.
12 Kenaka Abineri anatuma amithenga kwa Davide kukanena kuti, “Kodi dzikoli ndi la yani? Uchite mgwirizano ndi ine ndipo ndidzakuthandiza kuti Aisraeli onse azikutsatira.”
7 Inu mukuweruza potengera zimene maso anu akuona. Ngati wina akutsimikiza kuti ndi wake wa Khristu, iye aganizenso kuti ifenso ndife a Khristu monga iye. 8 Tsono ngakhale nditadzitama momasuka za ulamuliro umene Ambuye anatipatsa woti tikukuzeni osati kukuwonongani, ndithu sindidzachita manyazi. 9 Ine sindikufuna kuoneka ngati ndikukuopsezani ndi makalata anga. 10 Pakuti ena amati, “Makalata ake ndi awukali ndi amphamvu koma maonekedwe a thupi lake ndi wosagwira mtima ndipo mayankhulidwe ake ndi achabechabe.” 11 Anthu oterewa ayenera kuzindikira kuti zomwe timalemba mʼmakalata tili kutali ndi zomwe tidzakhale tili komweko.
The Word of God in Contemporary Chichewa Copyright © 2002, 2016 by Biblica, Inc.® Used by permission of Biblica, Inc.® All rights reserved worldwide. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Mwini © 2002, 2016 ndi Biblica, Inc.® Kugwiritsa ntchito mwachilolezo. Umwini ndi otetezedwa pa dziko lonse.