Print Page Options
Previous Prev Day Next DayNext

Revised Common Lectionary (Semicontinuous)

Daily Bible readings that follow the church liturgical year, with sequential stories told across multiple weeks.
Duration: 1245 days
Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero (CCL)
Version
Masalimo 89:20-37

20 Ndamupeza mtumiki wanga Davide;
    ndamudzoza ndi mafuta opatulika.
21 Dzanja langa lidzamuchirikiza;
    zoonadi, mkono wanga udzamupatsa mphamvu.
22 Adani sadzamulamula kuti apereke msonkho;
    anthu oyipa sadzamusautsa.
23 Ndidzaphwanya adani ake pamaso pake
    ndi kukantha otsutsana naye.
24 Chikondi changa chokhulupirika chidzakhala naye,
    ndipo kudzera mʼdzina langa nyanga yake idzakwezedwa.
25 Ndidzayika dzanja lake pa nyanja,
    dzanja lake lamanja pa mitsinje.
26 Iyeyo adzafuwula kwa Ine kuti, ‘Ndinu Atate anga,
    Mulungu wanga, Thanthwe ndi Chipulumutso changa.’
27 Ndidzamuyika kuti akhale mwana wanga woyamba kubadwa;
    wokwezedwa kwambiri pakati pa mafumu a dziko lapansi.
28 Ndidzamusungira chifundo changa kwamuyaya,
    ndipo pangano langa ndi iye silidzatha.
29 Ine ndidzakhazikitsa zidzukulu zake mpaka muyaya,
    mpando wake waufumu ngati masiku a miyamba.

30 “Ngati ana ake adzataya lamulo langa
    ndi kusatsatira malangizo anga,
31 ngati adzaswa malamulo anga
    ndi kulephera kusunga ziphunzitso zanga,
32 Ine ndidzalanga tchimo lawo ndi ndodo,
    mphulupulu zawo powakwapula.
33 Koma sindidzachotsa chikondi changa pa iye,
    kapena kukhala wosakhulupirika kwa iyeyo.
34 Sindidzaswa pangano langa
    kapena kusintha zimene milomo yanga yayankhula.
35 Ndinalumbira kamodzi mwa kuyera kwanga
    ndipo sindidzanama kwa Davide,
36 kuti zidzukulu zake zidzakhale kwamuyaya
    ndipo mpando wake waufumu udzakhazikika pamaso panga ngati dzuwa;
37 udzakhazikika kwamuyaya monga mwezi,
    mboni yokhulupirika mʼmitambo.
            Sela

1 Mbiri 11:15-19

15 Atatu mwa atsogoleri makumi atatu aja anabwera kwa Davide ku thanthwe ku phanga la Adulamu pamene gulu la Afilisti linali litamanga misasa mʼchigwa cha Refaimu. 16 Nthawi imeneyo Davide anali mu linga, ndipo boma la Afilisti linali ku Betelehemu. 17 Davide analakalaka madzi ndipo anati, “Haa, pakanapezeka munthu wokanditungira madzi a mʼchitsime chomwe chili pafupi ndi chipata cha ku Betelehemu!” 18 Choncho anthu atatuwa anadutsa mizere ya Afilisti, natunga madzi amene anali mʼchitsime chomwe chinali pafupi ndi chipata cha ku Betelehemu nabwera nawo kwa Davide. Koma iye anakana kumwa. Mʼmalo mwake anathira pansi pamaso pa Yehova. 19 Iye anati, “Inu Mulungu, musalole kuti ine ndichite chinthu ichi! Kodi ndimwe magazi a anthu amene anayika miyoyo yawo pachiswe?” Chifukwa iwo anayika miyoyo yawo pachiswe kuti abweretse madziwo, Davide sanamwe.

Zimenezi ndi zimene anachita anthu amphamvu atatuwo.

Akolose 1:15-23

Kupambana Koposa kwa Khristu

15 Mwanayu ndiye chithunzi cha Mulungu wosaonekayo. Iye ndiye Mwana wake woyamba kubadwa ndi wolamulira zolengedwa zonse. 16 Pakuti zinthu zonse zinalengedwa kudzera mwa Iye. Zinthu zakumwamba ndi za pa dziko lapansi, zooneka ndi zosaoneka, maufumu, akuluakulu, aulamuliro ndi amphamvu. Zinthu zonse zinalengedwa kudzera mwa Iye ndipo anazilengera Iyeyo. 17 Iyeyo analipo zinthu zonse zisanalengedwe ndipo zinthu zonse zimamangika pamodzi mwa Iye. 18 Iye ndiyenso mutu wa thupi, limene ndi mpingo. Iye ndiye chiyambi chake, woyamba kuuka kwa akufa, kuti Iyeyo akhale wopambana zonse. 19 Pakuti kunamukomera Mulungu kuti umulungu wake wonse ukhalemo mwa Khristu. 20 Ndipo kudzera mwa Iye Mulungu ayanjanitsenso zinthu zonse ndi Iye mwini, zinthu za pa dziko lapansi, kapena zinthu za kumwamba. Iye anachita mtendere kudzera mʼmagazi ake, wokhetsedwa pa mtanda.

21 Kale inu munali kutali ndi Mulungu ndipo munali adani a Mulungu mʼmaganizo mwanu chifukwa cha khalidwe lanu loyipa. 22 Koma tsopano Iye anakuyanjanitsani mʼthupi la Khristu kudzera mu imfa kuti akuperekeni pamaso pake oyera, opanda banga ndi opanda chotsutsidwa nacho 23 ngati mupitirirabe kukhala mʼchikhulupiriro chanu, okhazikika ndi olimba, osasunthidwa kuchoka pa chiyembekezo chimene munachigwira mu Uthenga Wabwino. Uwu ndi Uthenga Wabwino umene munawumva, umene wakhala ukulalikidwa kwa olengedwa onse a pansi pa thambo, ndi umenenso, ine Paulo ndinakhala mtumiki wake.

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero (CCL)

The Word of God in Contemporary Chichewa Copyright © 2002, 2016 by Biblica, Inc.® Used by permission of Biblica, Inc.® All rights reserved worldwide. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Mwini © 2002, 2016 ndi Biblica, Inc.® Kugwiritsa ntchito mwachilolezo. Umwini ndi otetezedwa pa dziko lonse.