Revised Common Lectionary (Semicontinuous)
Davide Adzozedwa Kukhala Mfumu ya Israeli
5 Mafuko onse a Israeli anabwera kwa Davide ku Hebroni ndipo anati, “Ife ndife mafupa ndi mnofu wanu. 2 Kale lija, pamene Sauli anali mfumu yathu, inu ndinu amene munkatsogolera Aisraeli pa nkhondo zawo. Ndipo Yehova anakuwuzani kuti, ‘Udzaweta anthu anga Aisraeli, ndipo udzakhala mfumu yawo.’ ”
3 Akuluakulu onse a Israeli atafika kwa Mfumu Davide ku Hebroni, mfumu inachita nawo pangano ku Hebroni pamaso pa Yehova, ndipo anamudzoza Davide kukhala mfumu ya Israeli.
4 Davide anali ndi zaka makumi atatu pamene anakhala mfumu, ndipo analamulira zaka makumi anayi. 5 Analamulira Yuda ali ku Hebroni kwa zaka zisanu ndi ziwiri ndi miyezi isanu ndi umodzi, ndipo ali ku Yerusalemu analamulira Israeli yense ndi Yuda kwa zaka 33.
9 Tsono Davide anakhazikika mu lingamo ndipo mzindawu anawutcha, Mzinda wa Davide. Iye anamanga malo onse ozungulira kuyambira ku matsitso ozungulira khoma. 10 Ndipo mphamvu za Davide zinkakulirakulira chifukwa anali ndi Yehova Mulungu Wamphamvuzonse.
Nyimbo. Salimo la ana a Kora.
48 Wamkulu ndi Yehova, ndi woyenera kwambiri matamando
mu mzinda wa Mulungu wathu, phiri lake loyera.
2 Lokongola mu utali mwake,
chimwemwe cha dziko lonse lapansi.
Malo aatali kwambiri a Zafoni ndiye Phiri la Ziyoni,
mzinda wa Mfumu yayikulu.
3 Mulungu ali mu malinga ake;
Iye wadzionetsa yekha kuti ndiye malinga akewo.
4 Pamene mafumu anasonkhana pamodzi,
pamene anayendera pamodzi kudzalimbana nafe,
5 iwo anaona mzindawo ndipo anadabwa kwambiri;
anathawa ndi mantha aakulu.
6 Pomwepo anagwidwa nako kunjenjemera,
ululu wonga wa mkazi woyembekezera pa nthawi yochira.
7 Inu munawawononga monga sitima zapamadzi za ku Tarisisi
zitawonongeka ndi mphepo ya kummawa.
8 Monga momwe tinamvera,
kotero ife tinaona
mu mzinda wa Yehova Wamphamvuzonse,
mu mzinda wa Mulungu wathu.
Mulungu adzawuteteza kwamuyaya.
9 Mʼkati mwa Nyumba yanu Mulungu,
ife timalingaliramo zachikondi chanu chosasinthika.
10 Monga dzina lanu, Inu Mulungu,
matamando anu amafika ku malekezero a dziko lapansi
dzanja lanu lamanja ladzaza ndi chilungamo.
11 Phiri la Ziyoni likukondwera,
midzi ya Yuda ndi yosangalala
chifukwa cha maweruzo anu.
12 Yendayendani mu Ziyoni, uzungulireni mzindawo,
werengani nsanja zake.
13 Yangʼanitsitsani bwino mipanda yake,
penyetsetsani malinga ake,
kuti mudzafotokoze za izo ku mʼbado wotsatira.
14 Pakuti Mulungu uyu ndi Mulungu wathu ku nthawi zosatha;
Iye adzakhala mtsogoleri wathu mpaka ku mapeto.
2 Ndikudziwa munthu mwa Khristu amene zaka khumi ndi zinayi zapitazo anatengedwa kupita kumwamba kwachitatu. Sindikudziwa ngati zinachitika ali mʼthupi kapena ayi, zimenezo akudziwa ndi Mulungu. 3 Ndipo ndikumudziwa munthu ameneyu. Sindikudziwa ngati zinachitika mʼthupi kapena ayi, zimenezo akudziwa ndi Mulungu. 4 Munthuyu anatengedwa kupita ku paradizo. Ndipo anamva zinthu zosatheka kuneneka, zinthu zimene munthu saloledwa kunena. 5 Ndidzatamanda za munthu ngati ameneyu, koma sindidzadzitamandira ine mwini kupatula za kufowoka kwanga. 6 Ngakhale nditafuna kudzitamandira, sindingakhale chitsiru, chifukwa ndikunena zoona. Koma ndimapewa kuti pasapezeke munthu wondiganizira moposera chimene ndili chifukwa cha zimene ndimachita kapena kuyankhula, 7 kapena chifukwa cha mavumbulutso aakulu kuposa awa. Choncho, kuti ndisadzitukumule, ndinayikidwa minga mʼthupi langa, wamthenga wa Satana, kuti adzindizunza. 8 Katatu konse ndinapempha Ambuye kuti andichotsere. 9 Koma anandiwuza kuti, “Chisomo changa ndi chokukwanira, pakuti mphamvu zanga zimaoneka kwathunthu mwa munthu wofowoka.” Choncho ndidzadzitamandira mokondwera chifukwa cha zofowoka zanga, kuti mʼkutero mphamvu ya Khristu ikhale pa ine. 10 Tsono, chifukwa cha Khristu, ndimakondwera pamene ndili wofowoka, pamene akundinyoza, pamene ndikumva zowawa, ndi pamene akundizunza ndi kundisautsa. Pakuti pamene ndili wofowoka ndiye kuti ndili wamphamvu.
Amupeputsa Yesu ku Nazareti
6 Yesu anachoka kumeneko napita ku mudzi kwawo, pamodzi ndi ophunzira ake. 2 Tsiku la Sabata litafika, anayamba kuphunzitsa mʼsunagoge, ndipo ambiri amene anamumva anadabwa.
Iwo anafunsa kuti, “Kodi munthu uyu anazitenga kuti zimenezi? Kodi ndi nzeru yotani imene munthu ameneyu wapatsidwa, kuti Iye akuchitanso zodabwitsa! 3 Kodi uyu si mpalamatabwa uja? Kodi uyu si mwana wa Mariya ndi mʼbale wa Yakobo, Yose, Yudasi ndi Simoni? Kodi alongo ake si ali ndi ife?” Ndipo anakhumudwa naye.
4 Yesu anawawuza kuti, “Mneneri amalemekezedwa kulikonse kupatula kwawo, ndi pakati pa abale ake ndi a mʼbanja mwake.” 5 Sanachite zodabwitsa kumeneko, koma anangosanjika manja pa odwala ochepa ndi kuwachiritsa. 6 Ndipo Iye anadabwa chifukwa chakusowa chikhulupiriro kwawo.
Yesu Atuma Ophunzira Khumi ndi Awiri
Pamenepo Yesu anayenda mudzi ndi mudzi kuphunzitsa. 7 Atayitana khumi ndi awiriwo, Iye anawatuma awiriawiri ndipo anawapatsa ulamuliro pa mizimu yoyipa.
8 Zomwe anawalangiza ndi izi: “Musatenge kanthu ka paulendo koma ndodo yokha; osatenga buledi, thumba, kapena ndalama. 9 Muvale nsapato koma osatenga malaya apadera. 10 Pamene mulowa mʼnyumba mukakhale momwemo kufikira mutachoka mʼmudzimo. 11 Ndipo ngati pa malo ena sakakulandirani kapena kukumverani, sasani fumbi la kumapazi anu pamene mukuchoka, kuti ukhale umboni wowatsutsa.”
12 Anatuluka kupita kukalalikira kuti anthu atembenuke mtima. 13 Anatulutsa ziwanda zambiri ndi kudzoza mafuta odwala ambiri ndi kuwachiritsa.
The Word of God in Contemporary Chichewa Copyright © 2002, 2016 by Biblica, Inc.® Used by permission of Biblica, Inc.® All rights reserved worldwide. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Mwini © 2002, 2016 ndi Biblica, Inc.® Kugwiritsa ntchito mwachilolezo. Umwini ndi otetezedwa pa dziko lonse.