Revised Common Lectionary (Semicontinuous)
Kwa mtsogoleri wa mayimbidwe. Salimo la Davide mtumiki wa Yehova. Iye anayimbira Yehova nyimbo iyi pamene Yehovayo anamupulumutsa mʼdzanja la adani ake onse ndiponso mʼdzanja la Sauli.
18 Davide anati: Ine ndimakukondani Inu Yehova, mphamvu zanga.
2 Yehova ndiye thanthwe langa, chitetezo changa ndi mpulumutsi wanga;
Mulungu wanga ndi thanthwe langa mʼmene ndimathawiramo.
Chishango changa ndi ndodo yachipulumutso changa, ndi linga langa.
3 Ndimayitana Yehova amene ndi woyenera matamando,
ndipo ndapulumutsidwa kwa adani anga.
4 Zingwe za imfa zinandizinga;
mitsinje yothamanga yachiwonongeko inandiopsa kwambiri.
5 Anandimanga ndi zingwe za ku manda;
misampha ya imfa inalimbana nane.
6 Mʼmasautso anga ndinapemphera kwa Yehova;
ndinalirira kwa Mulungu wanga kuti andithandize.
Ali mʼNyumba yake, anamva mawu anga;
kulira kwanga kunafika pamaso pake ndi mʼmakutu mwake.
43 Inu mwandipulumutsa mʼmanja mwa anthu;
mwandisandutsa kukhala mtsogoleri wa anthu a mitundu ina.
Anthu amene sindikuwadziwa ali pansi pa ulamuliro wanga.
44 Alendo amadzipereka okha pamaso panga;
akangomva za ine amandigonjera.
45 Iwo onse anataya mtima;
anatuluka mʼmalinga awo akunjenjemera.
46 Yehova ndi wamoyo! Litamandidwe Thanthwe langa!
Akuzike Mulungu Mpulumutsi wanga!
47 Iye ndi Mulungu amene amabwezera chilango,
amene amagonjetsa anthu a mitundu yonse amene ali pansi pa ulamuliro wanga,
48 amene amandipulumutsa mʼmanja mwa adani anga.
Inu munandikuza kuposa adani anga;
munandilanditsa mʼmanja mwa anthu ankhanza.
49 Choncho ine ndidzakutamandani pakati pa anthu a mitundu ina, Inu Yehova;
ndidzayimba nyimbo zotamanda dzina lanu.
50 Iye amapereka chipambano chachikulu kwa mfumu yake;
amaonetsa chikondi chosasinthika kwa wodzozedwa wake,
kwa Davide ndi zidzukulu zake kwamuyaya.
Imfa ya Sauli ndi Ana Ake
31 Tsono Afilisti anachitanso nkhondo ndi Aisraeli ndipo Aisraeli anathawa Afilistiwo, kotero kuti ambiri anaphedwa pa phiri la Gilibowa. 2 Afilisti anapanikiza kwambiri Sauli ndi ana ake, ndipo anapha Yonatani, Abinadabu ndi Maliki-Suwa. 3 Nkhondo inakula kwambiri mozungulira Sauli ndipo pamene anthu amauta anamupeza, anamuvulaza kwambiri.
4 Tsono Sauli anawuza mnyamata wake wonyamula zida zake kuti, “Solola lupanga lako undiphe kuopa kuti anthu osachita mdulidwewa angabwere kudzandizunza ine.”
Koma mnyamata wonyamula zida uja anachita mantha kwambiri ndipo sanathe kutero. Choncho Sauli anatenga lupanga lake lomwe nagwerapo. 5 Mnyamata wonyamula zida zake uja ataona kuti Sauli wafa, nayenso anadzigwetsera pa lupanga lake nafa naye limodzi. 6 Motero Sauli ndi ana ake atatu, wonyamula zida zake pamodzi ndi anthu ake onse anafera limodzi pa tsikulo.
7 Pamene Aisraeli amene anali tsidya lina la chigwa ndi amene anali tsidya la chigwa cha Yorodani anaona kuti gulu la ankhondo la Aisraeli lathawa komanso kuti Sauli ndi ana ake aphedwa, nawonso anathawa kusiya mizinda yawo. Ndipo Afilisti anabwera kudzakhalamo.
8 Mmawa mwake, Afilisti atabwera kudzatenga zinthu za anthu ophedwa anapeza Sauli ndi ana ake atatu atafa pa phiri la Gilibowa. 9 Iwo anadula mutu wake ndi kumuvula zida zake zankhondo. Ndipo anatumiza amithenga mʼdziko lonse la Afilisti kukafalitsa nkhani yabwinoyi kwa mafano awo ndi kwa anthu awo. 10 Iwo anayika zida zake zankhondo mʼnyumba yopembedzera Asitoreti, ndipo thupi lake analikhomera pa khoma la mzinda wa Beti-Sani.
11 Pamene anthu a ku Yabesi Giliyadi anamva zimene Afilisti anachitira Sauli, 12 anthu awo onse olimba mtima anayenda usiku wonse kupita ku Beti-Sani. Anakachotsa mtembo wa Sauli ndi mitembo ya ana ake pa khoma la mzinda wa Beti-Sani, ndipo anabwera nayo ku Yabesi kumene anayitentha ndi moto. 13 Pambuyo pake anatenga mafupa awo ndi kuwakwirira pansi pa mtengo wabwemba ku Yabesi, ndipo anasala kudya masiku asanu ndi awiri.
9 Nʼkosafunika kuti ndikulembereni za utumiki othandiza anthu a Mulungu. 2 Popeza ndikudziwa mtima wanu wofuna kuthandiza, ndipo ndakhala ndikuwawuza monyadira a ku Makedoniya za chimenechi. Ndimawawuza kuti inu a ku Akaya munakonzeka kale chaka chatha kuti mupereke. Ndipo changu chanu chapatsa chidwi ambiri mwa iwo kuti nawonso achitepo kanthu. 3 Koma ndikutumiza abalewo kuti kukunyadirani kwathu pa zimenezi kutsimikizike kuti si kwachabe ndi kuti mukhale okonzeka monga ndinanenera. 4 Pakuti nditabwera kumeneko ndi abale ena a ku Makedoniya, ndikukupezani kuti simunakonzeke, tingadzachite manyazi chifukwa chokudalirani. Koma amene angadzachite manyazi kwambiri ndi inuyo. 5 Choncho ndinaganiza kuti nʼkofunika kupempha abale kuti adzakuchezereni ineyo ndisanafike, ndikuti adzatsirize kukonzekera mphatso zomwe munalonjeza kupereka mowolowamanja. Motero mphatsoyo idzakhala yokonzeratu, ndipo idzakhala mphatso yoperekedwa mowolowamanja, osati mokakamizidwa.
The Word of God in Contemporary Chichewa Copyright © 2002, 2016 by Biblica, Inc.® Used by permission of Biblica, Inc.® All rights reserved worldwide. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Mwini © 2002, 2016 ndi Biblica, Inc.® Kugwiritsa ntchito mwachilolezo. Umwini ndi otetezedwa pa dziko lonse.