Revised Common Lectionary (Semicontinuous)
Kukhazikitsidwa kwa Paska
12 Yehova anayankhula kwa Mose ndi Aaroni mʼdziko la Igupto kuti, 2 “Mwezi uno uzikhala mwezi wanu woyamba wa chaka. 3 Muliwuze khamu lonse la Israeli kuti pa tsiku la khumi la mwezi uno, munthu aliyense asankhire banja lake mwana wankhosa mmodzi. Banja lililonse litenge mwana wankhosa mmodzi. 4 Ngati banja lili lochepa moti silingathe kudya nyama yonse ya nkhosa, ligawane ndi banja lomwe layandikana nalo nyumba. Mabanja adziwiretu chiwerengero cha anthu amene alipo pokonzekera zimenezi. Muwerengere kuchuluka kwa nyama imene anthu adzadye potengera mmene munthu mmodzi angadyere.
5 Ziweto zimene musankhe ziyenera kukhala zazimuna za chaka chimodzi, zopanda chilema, ndipo zikhale nkhosa kapena mbuzi. 6 Muzisunge mpaka tsiku la khumi ndi chinayi la mwezi, pamene gulu lonse la Aisraeli lidzaphe nyamazo madzulo. 7 Ndipo adzatengeko magazi anyamazo ndi kuwaza pa mphuthu ziwiri za chitseko ndiponso pamwamba pa chitseko cha nyumba mmene adzadyeremo ana ankhosawo. 8 Adzawotche nyamayo ndi kudya usiku womwewo, ndipo adzayidye ndi buledi wophikidwa popanda yisiti pamodzi ndi masamba wowawa. 9 Musadzadye yayiwisi kapena yophika, koma mudzawotche yonse, mutu, miyendo ndi zamʼmimba. 10 Musadzasiye nyama ina mpaka mmawa, ngati ina idzatsala mpaka mmawa, mudzayitenthe.
11 Muzidzadya nyamayo mutavala chotere, pokonzekera ulendo: mudzazimangirire lamba mʼchiwuno, nsapato zanu kuphazi ndi ndodo yanu kumanja. Mudzadye mofulumira. Imeneyi ndi Paska ya Yehova.
12 “Usiku umenewo Ine ndidzadutsa mʼdziko la Igupto ndipo ndidzapha chilichonse choyamba kubadwa kuyambira mwana wa munthu aliyense mpaka ana aziweto. Ndidzalanganso milungu yonse ya Igupto. Ine ndine Yehova. 13 Magazi amene mudzawaze pa mphuthu za zitseko ndi pamwamba pa zitseko aja adzakhala ngati chizindikiro. Ine ndikadzaona magaziwo ndidzakudutsani, ndipo ndikadzamakantha anthu a Igupto, mliri wosakazawu sudzakukhudzani.
14 “Ili ndi tsiku la chikumbutso. Tsiku limeneli muzidzachita chikondwerero, kupembedza Yehova. Mibado yonse imene ikubwera izidzakumbukira tsiku limeneli ngati lamulo lamuyaya ndi kuti pa tsikuli azidzachita chikondwerero cholemekeza Yehova.
116 Ndimakonda Yehova pakuti Iyeyo amamva mawu anga;
Iye amamva kulira kwanga kopempha chifundo.
2 Pakuti ananditchera khutu,
ndidzayitana Iye masiku onse a moyo wanga.
12 Ndingamubwezere chiyani Yehova,
chifukwa cha zokoma zake zonse zimene wandichitira?
13 Ndidzakweza chikho cha chipulumutso
ndipo ndidzayitana dzina la Yehova.
14 Ndidzakwaniritsa malonjezo anga kwa Yehova
pamaso pa anthu ake onse.
15 Imfa ya anthu oyera mtima
ndi yamtengowapatali pamaso pa Yehova.
16 Inu Yehova, zoonadi ndine mtumiki wanu:
ndine mtumiki wanu, mwana wa mdzakazi wanu;
Inu mwamasula maunyolo anga.
17 Ndidzapereka nsembe yachiyamiko kwa Inu
ndipo ndidzayitanira pa dzina la Yehova.
18 Ndidzakwaniritsa malonjezo anga kwa Yehova
pamaso pa anthu ake onse,
19 mʼmabwalo a nyumba ya Yehova,
mʼkati mwako iwe Yerusalemu.
Tamandani Yehova.
23 Pakuti zimene ndinalandira kwa Ambuye ndi zomwe ndinakupatsani. Ambuye Yesu, usiku umene anaperekedwa uja, anatenga buledi. 24 Atayamika ndi kumunyema ananena kuti, “Ili ndi thupi langa lomwe laperekedwa kwa inu; muzichita zimenezi pokumbukira Ine.” 25 Chimodzimodzi, atatha kudya, anatenga chikho, nati, “Chikho ichi ndi pangano latsopano la magazi anga; imwani nthawi zonse pokumbukira Ine.” 26 Pakuti nthawi zonse pamene mudya bulediyu ndikumwa chikhochi, mukulalikira imfa ya Ambuye mpaka Iye adzabweranso.
Yesu Asambitsa Mapazi a Ophunzira Ake
13 Inali pafupifupi nthawi ya phwando la Paska. Yesu anadziwa kuti nthawi yafika yoti achoke mʼdziko lapansi ndi kupita kwa Atate. Atawakonda ake amene anali mʼdziko lapansi, Iye anawaonetsa chikondi chake chonse.
2 Atayamba kudya mgonero, mdierekezi anali atalowa kale mu mtima wa Yudasi Isikarioti mwana wa Simoni, kuti amupereke Yesu. 3 Yesu podziwa kuti Atate anamupatsa Iye zonse mʼmanja mwake, ndi kuti Iye anachokera kwa Mulungu ndipo amabwerera kwa Mulunguyo; 4 anayimirira kuchoka pa chakudya navula zovala zake natenga nsalu yopukutira nadzimanga mʼchiwuno mwake. 5 Atachita izi, anathira madzi mʼbeseni ndi kuyamba kusambitsa mapazi a ophunzira ake, ndi kuwapukuta ndi chopukutira chimene anachimanga mʼchiwuno mwake.
6 Atafika pa Petro, Petroyo anati kwa Iye, “Ambuye, kodi mudzandisambitsa mapazi anga?”
7 Yesu anayankha kuti, “Iwe sukuzindikira tsopano chimene ndikuchita, koma udzazindikira mʼtsogolo.”
8 Petro anati, “Ayi, Inu simudzandisambitsa konse mapazi anga.”
Yesu anayankha kuti, “Ngati Ine sindisambitsa mapazi ako, ulibe gawo mwa Ine.”
9 Simoni Petro anayankha kuti, “Ambuye, osati mapazi okha komanso manja anga ndi mutu wanga womwe!”
10 Yesu anayankha kuti, “Munthu amene wasamba amangofunika kusamba mapazi ake okha chifukwa thupi lake lonse ndi loyera. Ndipo inu ndinu oyera, ngakhale kuti si aliyense mwa inu.” 11 Pakuti Iye anadziwa amene adzamupereka, ndipo nʼchifukwa chake anati saliyense wa inu ali woyera.
12 Iye atamaliza kusambitsa mapazi awo anavala zovala zake ndi kubwerera pamalo pake. Iye anawafunsa kuti, “Kodi mukuzindikira zimene ndakuchitirani inu? 13 Inu mumanditcha Ine, ‘Mphunzitsi’ ndi ‘Mbuye,’ ndipo mumakhoza mukamatero, pakuti ichi ndi chimene Ine ndili. 14 Tsono ngati Ine, Mbuye wanu ndi Mphunzitsi wanu, ndasambitsa mapazi anu, inunso muyenera kusambitsana mapazi anu. 15 Ine ndakupatsani chitsanzo kuti muzichita monga Ine ndachitira. 16 Zoonadi, Ine ndikukuwuzani kuti wantchito saposa mbuye wake, kapena wotumidwa kuposa amene wamutuma. 17 Ngati inu mudziwa zinthu zimenezi, mudzakhala odala mukamazichita.
Yesu Aneneratu kuti Petro Adzamukana
31 Yudasi atatuluka, Yesu anati, “Tsopano Mwana wa Munthu walemekezedwa, ndipo mwa Iyeyu Mulungu walemekezedwanso. 32 Ngati Mulungu walemekezedwa mwa Iye, Mulungu mwini adzalemekezanso Mwana, ndipo amulemekeza nthawi yomweyo.
33 “Ana anga, Ine ndikhala nanu kwa nthawi yochepa chabe. Inu mudzandifunafuna Ine, ndipo monga momwe ndinawawuzira Ayuda, choncho Ine ndikukuwuzani tsopano kuti, kumene Ine ndikupita, inu simungabwereko.
34 “Lamulo latsopano limene ndikukupatsani ndi lakuti: Kondanani wina ndi mnzake, monga momwe Ine ndinakonda inu. Nanunso mukondane wina ndi mnzake. 35 Mukamakondana aliyense adzadziwa kuti ndinu ophunzira anga.”
The Word of God in Contemporary Chichewa Copyright © 2002, 2016 by Biblica, Inc.® Used by permission of Biblica, Inc.® All rights reserved worldwide. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Mwini © 2002, 2016 ndi Biblica, Inc.® Kugwiritsa ntchito mwachilolezo. Umwini ndi otetezedwa pa dziko lonse.