Print Page Options
Previous Prev Day Next DayNext

Revised Common Lectionary (Semicontinuous)

Daily Bible readings that follow the church liturgical year, with sequential stories told across multiple weeks.
Duration: 1245 days
Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero (CCL)
Version
Masalimo 147:1-11

147 Tamandani Yehova.

Nʼkwabwino kwambiri kuyimba nyimbo zamatamando kwa Mulungu wathu,
    nʼkokondweretsa ndi koyenera kumutamanda!

Yehova akumanga Yerusalemu;
    Iye akusonkhanitsa amʼndende a Israeli.
Akutsogolera anthu osweka mtima
    ndi kumanga mabala awo.

Amadziwa chiwerengero cha nyenyezi,
    ndipo iliyonse amayitchula dzina.
Yehova ndi wamkulu ndi wamphamvu kwambiri;
    nzeru zake zilibe malire.
Yehova amagwiriziza anthu odzichepetsa,
    koma amagwetsa pansi anthu oyipa.

Imbirani Yehova ndi mayamiko;
    imbani nyimbo kwa Mulungu ndi pangwe.
Iye amaphimba mlengalenga ndi mitambo;
    amapereka mvula ku dziko lapansi
    ndi kumeretsa udzu mʼmapiri.
Iye amapereka chakudya kwa ngʼombe
    ndi kwa ana a makwangwala pamene akulira chakudya.

10 Chikondwerero chake sichili mʼmphamvu za kavalo,
    kapena mʼmiyendo ya anthu amphamvu.
11 Yehova amakondwera ndi amene amamuopa,
    amene chiyembekezo chawo chili mʼchikondi chake chosasinthika.

Masalimo 147:20

20 Sanachitepo zimenezi kwa mtundu wina uliwonse wa anthu;
    anthu enawo sadziwa malamulo ake.

Tamandani Yehova.

Miyambo 12:10-21

10 Munthu wolungama amasamalira moyo wa ziweto zake,
    koma chifundo cha munthu woyipa ndi chakhanza.

11 Wolima mʼmunda mwake mwakhama adzakhala ndi chakudya chochuluka,
    koma wotsata zopanda pake alibe nzeru.

12 Munthu woyipa amalakalaka zofunkha za anthu oyipa,
    koma mizu ya anthu olungama imabereka zipatso.

13 Munthu woyipa amakodwa mu msampha wa mayankhulidwe ake oyipa;
    koma munthu wolungama amatuluka mʼmavuto.

14 Munthu amakhala ndi zabwino zambiri chifukwa cha mawu ake
    ndipo ntchito zimene munthu agwira ndi manja ake zimamupindulira.

15 Zochita za chitsiru mwini wakeyo amaziona ngati zabwino,
    koma munthu wanzeru amamvera malangizo.

16 Mkwiyo wa chitsiru umadziwika nthawi yomweyo,
    koma munthu wanzeru sasamala kunyozedwa.

17 Woyankhula zoona amapereka umboni woona,
    koma mboni yabodza imafotokoza zonama.

18 Munthu woyankhula mosasamala mawu ake amalasa ngati lupanga,
    koma mawu a munthu wanzeru amachiritsa.

19 Mawu woona amakhala mpaka muyaya
    koma mawu abodza sakhalitsa.

20 Mʼmitima ya anthu amene amakonza zoyipa muli chinyengo;
    koma anthu olimbikitsa za mtendere amakhala ndi chimwemwe.

21 Palibe choyipa chimene chimagwera munthu wolungama,
    koma munthu woyipa mavuto samuthera.

Agalatiya 5:2-15

Chonde mvetsetsani! Ine Paulo, ndikukuwuzani kuti mukalola kuchita mdulidwe, Khristu simupindula nayenso konse. Ndikubwerezanso kuwuza munthu aliyense wovomereza kuchita mdulidwe kuti ayeneranso kutsata Malamulo onse. Inu amene mukufuna kulungamitsidwa ndi lamulo mwachotsedwa mwa Khristu; munagwa kusiyana nacho chisomo. Koma mwachikhulupiriro, ife tikudikira mwachidwi kudzera mwa Mzimu, chilungamo chimene tikuyembekeza. Pakuti mwa Khristu Yesu mdulidwe kapena kusachita mdulidwe zilibe phindu. Chinthu chokhacho chimene chimafunika ndi chikhulupiriro chogwira ntchito mwachikondi.

Inu munkathamanga mpikisano wanu wabwino. Anakuletsani ndani kuti musamverenso choonadi? Kukopeka kwanu kumeneku sikuchokera kwa Iye amene anakuyitanani. “Yisiti wapangʼono amagwira ntchito mu buledi yense.” 10 Ine ndikutsimikiza mwa Ambuye kuti inu simudzasiyana nane maganizo. Iye amene akukusokonezani adzalangidwa, kaya iyeyo ndiye ndani. 11 Abale, ngati ine ndikulalikirabe za mdulidwe, nʼchifukwa chiyani ndikusautsidwabe? Ngati ndikanakhala kuti sindikulalikira chipulumutso cha mtanda, palibe amene akanakhumudwa. 12 Kunena za amene akukuvutani, ndikanakonda akanangodzithena okha!

Moyo mwa Mzimu Woyera

13 Inu abale, Mulungu anakuyitanani kuti mukhale mfulu. Koma musagwiritse ntchito ufulu wanuwo kuchita zoyipa zachikhalidwe cha uchimo cha thupi lanu, koma mutumikirane wina ndi mnzake mwachikondi. 14 Pakuti malamulo onse akuphatikizidwa mu lamulo ili, “Konda mnansi wako monga iwe mwini.” 15 Ngati mupitiriza kulumana ndi kukhadzulana, samalani kuti mungawonongane.

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero (CCL)

The Word of God in Contemporary Chichewa Copyright © 2002, 2016 by Biblica, Inc.® Used by permission of Biblica, Inc.® All rights reserved worldwide. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Mwini © 2002, 2016 ndi Biblica, Inc.® Kugwiritsa ntchito mwachilolezo. Umwini ndi otetezedwa pa dziko lonse.