Revised Common Lectionary (Semicontinuous)
8 Mulungu anawuza Nowa ndi ana ake kuti, 9 “Tsopano Ine ndapangana ndi iwe ndi zidzukulu zako zamʼtsogolomo, 10 pamodzi ndi zamoyo zonse, mbalame, ziweto ndi nyama zonse za kuthengo, ndi zonse zimene zinatuluka mʼchombo pamodzi ndi iwe. 11 Pangano langa ndi ili: Ine ndilonjeza kuti sindidzawononganso zamoyo ndi madzi a chigumula. Chigumula sichidzawononganso dziko lapansi.”
12 Ndipo Mulungu anati, “Ine ndikupereka chizindikiro ichi cha pangano langa la pakati pa Ine ndi iwe, ana ako, zamoyo zonse, pamodzi ndi mibado ya mʼtsogolo. 13 Ndayika utawaleza wanga mʼmitambo, ndipo chidzakhala chizindikiro cha pangano langa ndi dziko lapansi. 14 Nthawi zonse pakakhala mitambo mu mlengalenga ndipo utawaleza uwoneka, 15 ndizikumbukira pangano langa pakati pa Ine ndi inu ndi zolengedwa zonse. Madzi sadzakhalanso chigumula chowononga dziko lapansi. 16 Utawaleza ukamadzaoneka mʼmitambo, ndidzawuona ndi kukumbukira pangano losatha pakati pa Mulungu ndi zamoyo zonse pa dziko lapansi.”
17 Choncho Mulungu anati kwa Nowa, “Ichi ndiye chizindikiro cha pangano limene ndalichita pakati pa Ine ndi zamoyo zonse pa dziko lapansi.”
Salimo la Davide.
25 Kwa Inu Yehova, ndipereka moyo wanga.
2 Ndimadalira Inu Mulungu wanga.
Musalole kuti ndichite manyazi
kapena kuti adani anga andipambane.
3 Aliyense amene amayembekezera kwa Ambuye
sadzachititsidwa manyazi
koma achinyengo ndiwo adzachititsidwe manyazi
ndipo sadzakhala ndi chodzitetezera.
4 Ndidziwitseni njira zanu Inu Yehova,
phunzitseni mayendedwe anu;
5 tsogolereni mʼchoonadi chanu ndi kundiphunzitsa,
pakuti Inu ndinu Mulungu mpulumutsi wanga,
ndipo chiyembekezo changa chili mwa Inu tsiku lonse.
6 Kumbukirani Inu Yehova chifundo ndi chikondi chanu chachikulu,
pakuti ndi zakalekale.
7 Musakumbukire machimo a ubwana wanga
ndi makhalidwe anga owukira;
molingana ndi chikondi chanu ndikumbukireni ine,
pakuti Inu Yehova ndinu wabwino.
8 Yehova ndi wabwino ndi wolungama;
choncho Iye akulangiza ochimwa mʼnjira yake.
9 Amatsogolera odzichepetsa kuti achite zolungama
ndipo amawaphunzitsa njira zake.
10 Njira zonse za Yehova ndi zachikondi ndi zokhulupirika
kwa iwo amene amasunga zofuna za pangano lake.
18 Pakuti Khristu anafa chifukwa cha machimo kamodzi kokha kufera onse, wolungama kufera osalungama, kuti akufikitseni kwa Mulungu. Anaphedwa ku thupi koma anapatsidwa moyo mu mzimu. 19 Ndipo ali ngati mzimu chomwecho anapita ndi kukalalikira mizimu imene inali mʼndende, 20 ya anthu amene sanamvere Mulungu atadikira moleza mtima pa nthawi imene Nowa ankapanga chombo. Mʼchombo chija anthu owerengeka okha, asanu ndi atatu, ndiwo anapulumutsidwa ku madzi. 21 Madziwo akufanizira ubatizo umene lero ukukupulumutsaninso, osati chifukwa chochotsa litsiro la mʼthupi koma chifukwa cha chikumbumtima choona pamaso pa Mulungu. Umakupulumutsani chifukwa cha kuuka kwa Yesu Khristu, 22 amene anapita kumwamba ndipo ali kudzanja lamanja la Mulungu komwe angelo ndi maulamuliro ndi amphamvu amamvera Iye.
Kubatizidwa ndi Kuyesedwa kwa Yesu
9 Pa nthawi imeneyo Yesu anabwera kuchokera ku Nazareti wa ku Galileya ndipo anabatizidwa ndi Yohane mu mtsinje wa Yorodani. 10 Pamene Yesu ankatuluka mʼmadzi, anaona kumwamba kukutsekuka ndipo Mzimu Woyera akutsikira pa Iye ngati nkhunda. 11 Ndipo Mawu anamveka kuchokera kumwamba: “Iwe ndiwe Mwana wanga wokondedwa; ndipo ndikondwera nawe.”
12 Nthawi yomweyo Mzimu Woyera anamutumiza Iye ku chipululu, 13 ndipo anali mʼchipululumo masiku makumi anayi, akuyesedwa ndi Satana. Anali pakati pa nyama zakuthengo; ndipo angelo anamutumikira.
Yesu Alengeza za Uthenga Wabwino
14 Yohane atamutsekera mʼndende, Yesu anapita ku Galileya nalalikira Uthenga Wabwino wa Mulungu nati, 15 “Nthawi yafika, ufumu wa Mulungu wayandikira. Tembenukani mtima ndi kukhulupirira Uthenga Wabwino!”
The Word of God in Contemporary Chichewa Copyright © 2002, 2016 by Biblica, Inc.® Used by permission of Biblica, Inc.® All rights reserved worldwide. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Mwini © 2002, 2016 ndi Biblica, Inc.® Kugwiritsa ntchito mwachilolezo. Umwini ndi otetezedwa pa dziko lonse.