Revised Common Lectionary (Semicontinuous)
Salimo la Davide.
110 Yehova akuwuza Mbuye wanga kuti,
“Khala ku dzanja langa lamanja
mpaka nditasandutsa adani ako
kukhala chopondapo mapazi ako.”
2 Yehova adzakuza ndodo yamphamvu ya ufumu wako kuchokera mʼZiyoni;
udzalamulira pakati pa adani ako.
3 Ankhondo ako adzakhala odzipereka
pa tsiku lako la nkhondo.
Atavala chiyero chaulemerero,
kuchokera mʼmimba ya mʼbandakucha,
udzalandira mame a unyamata wako.
4 Yehova walumbira
ndipo sadzasintha maganizo ake:
“Ndiwe wansembe mpaka muyaya
monga mwa unsembe wa Melikizedeki.”
23 “Aa, achikhala mawu anga analembedwa,
achikhala analembedwa mʼbuku,
24 akanalembedwa pa mwala ndi chitsulo,
akanalembedwa pa thanthwe kuti sangathe kufufutidwa!
25 Koma ndikudziwa kuti mpulumutsi wanga ali ndi moyo,
ndipo pa nthawi yomaliza adzabwera kudzanditeteza.
26 Ndipo khungu langa litatha nʼkuwonongeka,
mʼthupi langa lomweli ndidzamuona Mulungu.
27 Ine ndemwe ndidzamuona Iye
ndi maso angawa, ineyo, osati wina ayi.
Ndithu mtima wanga ukufunitsitsadi!
Cholinga cha Malangizo a Paulo
14 Ngakhale ndili ndi chiyembekezo choti ndifika komweko posachedwapa, ndikukulemberani malangizo awa. 15 Ine zina zikandichedwetsa kubwera, mudziwe za mmene anthu ayenera kukhalira mʼNyumba ya Mulungu, imene ndi mpingo wa Mulungu wamoyo, mzati ndi maziko achoonadi. 16 Mosakayikira, chinsinsi cha chikhulupiriro chathu chachikulu:
Khristu anaonekera ali ndi thupi la munthu,
Mzimu anamuchitira umboni,
angelo anamuona,
analalikidwa pakati pa mitundu yonse,
dziko lapansi linamukhulupirira,
anatengedwa kupita kumwamba mwa ulemerero.
The Word of God in Contemporary Chichewa Copyright © 2002, 2016 by Biblica, Inc.® Used by permission of Biblica, Inc.® All rights reserved worldwide. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Mwini © 2002, 2016 ndi Biblica, Inc.® Kugwiritsa ntchito mwachilolezo. Umwini ndi otetezedwa pa dziko lonse.