Print Page Options
Previous Prev Day Next DayNext

Revised Common Lectionary (Semicontinuous)

Daily Bible readings that follow the church liturgical year, with sequential stories told across multiple weeks.
Duration: 1245 days
Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero (CCL)
Version
Masalimo 107:1-3

BUKU LACHISANU

Masalimo 107–150

107 Yamikani Yehova chifukwa ndi wabwino;
    pakuti chikondi chake ndi chosatha.
Owomboledwa a Yehova anene zimenezi
    amene Iyeyo anawawombola mʼdzanja la mdani,
iwo amene anawasonkhanitsa kuchokera ku mayiko,
    kuchokera kumadzulo ndi kummawa, kuchokera kumpoto ndi kummwera.

Masalimo 107:17-22

17 Ena anakhala zitsiru chifukwa cha njira zawo zowukira,
    ndipo anamva zowawa chifukwa cha mphulupulu zawo.
18 Iwo ananyansidwa ndi chakudya chilichonse
    ndipo anafika pafupi ndi zipata za imfa.
19 Pamenepo analirira Yehova mʼmasautso awo
    ndipo Iye anawapulumutsa ku masautso awowo.
20 Iye anatumiza mawu ake ndi kuwachiritsa;
    anawalanditsa ku manda.
21 Ayamike Yehova chifukwa cha chikondi chake chosatha
    ndi machitidwe ake odabwitsa kwa anthu.
22 Apereke nsembe yachiyamiko
    ndi kufotokoza za ntchito zake ndi nyimbo zachimwemwe.

Genesis 9:8-17

Mulungu anawuza Nowa ndi ana ake kuti, “Tsopano Ine ndapangana ndi iwe ndi zidzukulu zako zamʼtsogolomo, 10 pamodzi ndi zamoyo zonse, mbalame, ziweto ndi nyama zonse za kuthengo, ndi zonse zimene zinatuluka mʼchombo pamodzi ndi iwe. 11 Pangano langa ndi ili: Ine ndilonjeza kuti sindidzawononganso zamoyo ndi madzi a chigumula. Chigumula sichidzawononganso dziko lapansi.”

12 Ndipo Mulungu anati, “Ine ndikupereka chizindikiro ichi cha pangano langa la pakati pa Ine ndi iwe, ana ako, zamoyo zonse, pamodzi ndi mibado ya mʼtsogolo. 13 Ndayika utawaleza wanga mʼmitambo, ndipo chidzakhala chizindikiro cha pangano langa ndi dziko lapansi. 14 Nthawi zonse pakakhala mitambo mu mlengalenga ndipo utawaleza uwoneka, 15 ndizikumbukira pangano langa pakati pa Ine ndi inu ndi zolengedwa zonse. Madzi sadzakhalanso chigumula chowononga dziko lapansi. 16 Utawaleza ukamadzaoneka mʼmitambo, ndidzawuona ndi kukumbukira pangano losatha pakati pa Mulungu ndi zamoyo zonse pa dziko lapansi.”

17 Choncho Mulungu anati kwa Nowa, “Ichi ndiye chizindikiro cha pangano limene ndalichita pakati pa Ine ndi zamoyo zonse pa dziko lapansi.”

Aefeso 1:3-6

Madalitso Auzimu mwa Khristu

Tiyamike Mulungu, Atate a Ambuye athu Yesu Khristu, amene anatipatsa madalitso onse a uzimu kumwamba mwa Khristu. Dziko lapansi lisanalengedwe, Mulungu anatisankhiratu mwa Khristu kuti tikhale oyera mtima ndi wopanda cholakwa pamaso pake. Mwa chikondi chake, Iye anakonzeratu kuti ife titengedwe ngati ana mwa Yesu Khristu, molingana ndi kukonda kwake ndi chifuniro chake. Anachita zimenezi kuti tiziyamika ulemerero wa chisomo chake, umene watipatsa kwaulere mwa Khristu amene amamukonda.

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero (CCL)

The Word of God in Contemporary Chichewa Copyright © 2002, 2016 by Biblica, Inc.® Used by permission of Biblica, Inc.® All rights reserved worldwide. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Mwini © 2002, 2016 ndi Biblica, Inc.® Kugwiritsa ntchito mwachilolezo. Umwini ndi otetezedwa pa dziko lonse.