Print Page Options
Previous Prev Day Next DayNext

Revised Common Lectionary (Semicontinuous)

Daily Bible readings that follow the church liturgical year, with sequential stories told across multiple weeks.
Duration: 1245 days
Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero (CCL)
Version
Masalimo 84

Kwa mtsogoleri wa mayimbidwe. Potsata mayimbidwe a Gititi. Salimo la ana a Kora.

84 Malo anu okhalamo ndi okomadi,
    Inu Yehova Wamphamvuzonse!
Moyo wanga ukulakalaka, mpaka kukomoka,
    kufuna mabwalo a Yehova;
Mtima wanga ndi thupi langa zikufuwulira
    Mulungu wamoyo.

Ngakhale timba wapeza nyumba yokhalamo,
    ndiponso namzeze wadzipezera yekha chisa,
    kumene amagonekako ana ake
pafupi ndi guwa lanu la nsembe,
    Inu Yehova Wamphamvuzonse, Mfumu yanga ndi Mulungu wanga.
Odala amene amakhala mʼNyumba yanu;
    nthawi zonse amakutamandani.
            Sela

Odala amene mphamvu yawo ili mwa Inu,
    mitima yawo ikufunitsitsa kuyenda mʼmisewu yopita ku Ziyoni.
Pamene akudutsa chigwa cha Baka,
    amachisandutsa malo a akasupe;
    mvula ya chizimalupsa imadzazanso mayiwe ake.
Iwo amanka nakulirakulira mphamvu
    mpaka aliyense ataonekera pamaso pa Mulungu mu Ziyoni.

Imvani pemphero langa, Inu Yehova Mulungu Wamphamvuzonse;
    mvereni Inu Mulungu wa Yakobo.
            Sela
Yangʼanani chishango chathu, Inu Mulungu;
    yangʼanani mokoma mtima pa wodzozedwa wanu.

10 Nʼkwabwino kukhala mʼmabwalo anu tsiku limodzi
    kuposa kukhala kwina kwake kwa zaka 1,000;
Ine ndingakonde kukhala mlonda wa pa khomo la Nyumba ya Mulungu wanga
    kuposa kukhala mʼmatenti a anthu oyipa.
11 Pakuti Yehova Mulungu ndi dzuwa ndi chishango;
    Yehova amapereka chisomo ndi ulemu;
Iye sawamana zinthu zabwino
    iwo amene amayenda mwangwiro.

12 Inu Yehova Wamphamvuzonse,
    wodala ndi munthu amene amakhulupirira Inu.

2 Mbiri 29:1-11

Mfumu Hezekiya Ayeretsa Nyumba ya Mulungu

29 Hezekiya anali wa zaka 25 pamene anakhala mfumu ndipo analamulira mu Yerusalemu kwa zaka 29. Dzina la amayi ake linali Abiya mwana wa Zekariya. Iye anachita zolungama pamaso pa Yehova, monga momwe anachitira Davide abambo ake.

Pa chaka choyamba cha ulamuliro wake, iye anatsekula zitseko za Nyumba ya Yehova ndipo anazikonza. Iye analowetsamo ansembe ndi Alevi ndipo anawasonkhanitsa ku bwalo lakummawa ndipo anati: “Mverani, inu Alevi! Dziyeretseni tsopano ndiponso muyeretse Nyumba ya Yehova Mulungu wa makolo anu. Muchotse zodetsa zonse ku malo opatulika. Makolo athu anali osakhulupirika ndipo anachita zoyipa pa maso pa Yehova Mulungu wathu ndi kumusiya Yehovayo. Iwo anatembenuka ndi kusiya malo okhalako Yehova ndi kumufulatira. Iwowo anatsekanso zitseko zapakhonde ndi kuzimitsa nyale. Sanafukize lubani kapena kupereka nsembe zopsereza ku malo opatulika a Mulungu wa Israeli. Kotero, Yehova anakwiyira Yuda ndi Yerusalemu. Iye anawasandutsa chinthu chochititsa mantha, choopsa ndiponso chonyozedwa monga momwe mukuonera ndi maso anuwa lero lino. Ichi nʼchifukwa chake makolo athu anaperekedwa ku lupanga ndipo nʼchifukwa chake ana athu aamuna ndi aakazi ndi akazi athu ali ku ukapolo. 10 Tsono ine ndikuganiza zochita pangano ndi Yehova Mulungu wa Israeli, kuti mkwiyo wake woopsawu utichokere. 11 Ana anga, musanyalanyaze tsopano, pakuti Yehova wakusankhani kuti muziyima pamaso pake ndi kumutumikira Iye, kugwira ntchito pamaso pake ndi kufukiza lubani.”

2 Mbiri 29:16-19

16 Ansembe analowa ku malo opatulika a Yehova kukayeretsako. Anatulutsira ku bwalo la Nyumba ya Yehova chilichonse chodetsedwa chimene anachipeza mʼNyumba ya Yehova. Alevi anatenga zimenezo ndi kupita nazo ku chigwa cha Kidroni. 17 Iwo anayamba mwambo woyeretsawu tsiku loyamba la mwezi woyamba ndipo pa tsiku lachisanu ndi chitatu la mweziwo anafika pa khonde la nyumba ya Yehova. Tsono anachita mwambo woyeretsa Nyumba ya Yehova ija masiku asanu ndi atatu, ndipo anamaliza pa tsiku la 16 mwezi woyamba.

18 Ndipo anapita kwa mfumu Hezekiya ndi kukafotokoza kuti, “Ife tayeretsa Nyumba ya Mulungu yonse, guwa lansembe zopsereza ndi ziwiya zake zonse, ndiponso tebulo limene timayikapo buledi wopatulika pamodzi ndi zinthu zake zonse. 19 Takonza ndi kuyeretsa zinthu zonse zimene mfumu Ahazi anazichotsa mwa kusakhulupirika kwake pamene anali mfumu. Taziyika kutsogolo kwa guwa la Yehova.”

Ahebri 9:23-28

23 Tsono panafunika kuti zinthu zingofanizira zenizeni za kumwamba, ziyeretsedwe ndi nsembe zimenezi, koma zinthu za kumwamba zenizenizo kuti ziyeretsedwe panafunika nsembe zina zoposa zimenezo. 24 Pakuti Khristu sanalowe mʼmalo opatulika omangidwa ndi anthu amene anali chifaniziro cha malo enieniwo. Iye analowa kumwamba kwenikweniko kuti azionekera pamaso pa Mulungu chifukwa cha ife. 25 Iye sanalowe kumwamba kuti azikadziperekanso nsembe kachiwiri monga momwe mkulu wa ansembe ankachitira chaka ndi chaka ku Malo Opatulika kwambiri ndi magazi amene sanali ake. 26 Zikanatero bwenzi Khristu atamva zowawa kambirimbiri chilengedwere cha dziko lapansi. Koma tsopano anaoneka kamodzi kokha chifukwa cha onse pa nthawi yotsiriza kuti achotse tchimo podzipereka yekha nsembe. 27 Popeza kunayikika kwa munthu kufa kamodzi ndipo kenaka kuweruzidwa, 28 momwemonso Khristu anadzipereka nsembe kamodzi kokha kuchotsa machimo a anthu ambiri. Ndipo Iye adzaonekanso kachiwiri, osati kudzachotsa tchimo, koma kudzapereka chipulumutso kwa amene akumudikira.

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero (CCL)

The Word of God in Contemporary Chichewa Copyright © 2002, 2016 by Biblica, Inc.® Used by permission of Biblica, Inc.® All rights reserved worldwide. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Mwini © 2002, 2016 ndi Biblica, Inc.® Kugwiritsa ntchito mwachilolezo. Umwini ndi otetezedwa pa dziko lonse.