Revised Common Lectionary (Semicontinuous)
Mtumiki wa Yehova
42 “Nayu mtumiki wanga, amene ndimamuchirikiza,
amene ndamusankha, amenenso ndimakondwera naye.
Ndayika Mzimu wanga mwa Iyeyo,
ndipo adzaweruza anthu a mitundu yonse mwachilungamo.
2 Iye sadzafuwula, sadzamveka mawu,
kapena mawu ake kumveka mʼmisewu.
3 Bango lophwanyika sadzalithyola,
ndipo moto wozilala sadzawuzimitsa.
Motero adzaonetsa kuti chilungamo ndicho choonadi;
4 sadzafowoka kapena kukhumudwa
mpaka atakhazikitsa chilungamo pa dziko lapansi,
ndi mpaka mayiko a mʼmbali mwa nyanja atafika poyembekezera malangizo ake.”
5 Yehova Mulungu
amene analenga zamlengalenga ndi kuziyalika,
amene analenga dziko lapansi ndi zonse zimene zimabereka,
amenenso amapereka mpweya kwa anthu ake okhala mʼdzikomo,
ndi moyo kwa onse oyendamo, akuti,
6 “Ine Yehova, ndakuyitana chifukwa Ine ndine wolungama;
ndikugwira dzanja ndipo
ndidzakuteteza.
Ndakupereka kukhala pangano langa kwa anthu
ndi kuwunika kwa anthu a mitundu ina.
7 Udzatsekula maso a anthu osaona,
udzamasula anthu a mʼndende
ndi kutulutsa mʼndende anthu okhala mu mdima.
8 “Ine ndine Yehova: dzina langa ndi limenelo!
Sindidzapereka ulemerero wanga kwa wina aliyense
kapena matamando anga kwa mafano.
9 Taonani, zinthu zimene ndinalosera kale zachitikadi,
ndipo ndikuwuzani zinthu zatsopano;
zinthuzo zisanaonekere
Ine ndakudziwitsani.”
5 Chikondi chanu Yehova, chimafika ku mayiko a kumwamba,
kukhulupirika kwanu mpaka ku mitambo.
6 Chilungamo chanu Mulungu chili ngati mapiri aakulu,
chiweruzo chanu chili ngati kuzama kwakukulu.
Yehova mumasunga munthu pamodzi ndi chinyama.
7 Chikondi chanu chosatha ndi chamtengowapatali!
Otchuka pamodzi ndi anthu wamba pakati pa anthu
amapeza pothawirapo mu mthunzi wa mapiko anu.
8 Iwo amadyerera zinthu zambiri za mʼnyumba yanu;
Inu mumawapatsa chakumwa kuchokera mu mtsinje wanu wachikondwerero.
9 Pakuti kwa Inu kuli kasupe wamoyo;
mʼkuwala kwanu ifenso timaona kuwala.
10 Pitirizani chikondi chanu pa iwo amene amakudziwani,
chilungamo chanu kwa olungama mtima.
11 Musalole kuti phazi la wodzikuza libwere kulimbana nane,
kapena dzanja la oyipa kundithamangitsa.
Magazi a Yesu
11 Koma Khristu atafika monga Mkulu wa ansembe wa zinthu zokoma zimene zilipo tsopano, Iye analowa mʼChihema chachikulu ndiponso changwiro chimene sichinamangidwe ndi munthu, ndiye kuti sichili pansi pano. 12 Iye sanalowemo ndi magazi ambuzi yayimuna, ana angʼombe amphongo, koma analowa Malo Opatulika kamodzi kokha ndi magazi ake, atatikonzera chipulumutso chosatha. 13 Ngati magazi ambuzi yayimuna, angʼombe yayimuna ndi phulusa la mwana wangʼombe wamkazi zimati zikawazidwa pa odetsedwa zimawayeretsa kotero kuti amakhala oyeretsedwa ku thupi, 14 nʼkoposa kotani magazi a Khristu, amene mwa Mzimu wamuyaya anadzipereka yekha kwa Mulungu kukhala nsembe yopanda chilema. Iye adzayeretsa chikumbumtima chathu pochotsa ntchito za imfa, kuti ife titumikire Mulungu wamoyo.
15 Pa chifukwa chimenechi Khristu ndi mʼkhalapakati wa pangano latsopano, kuti iwo amene anayitanidwa alandire chuma chamuyaya, pakuti Iye tsopano anafa ngati dipo lomasula iwo ku machimo amene anachita ali pansi pa pangano loyamba lija.
Mariya Adzoza Mapazi a Yesu
12 Masiku asanu ndi limodzi Paska asanafike, Yesu anafika ku Betaniya, kumene kumakhala Lazaro, amene Yesu anamuukitsa kwa akufa. 2 Kumeneko anamukonzera Yesu chakudya cha madzulo. Marita anatumikira pamene Lazaro anali mmodzi wa iwo amene anakhala nawo pa chakudyacho. 3 Kenaka Mariya anatenga botolo la mafuta a nadi, onunkhira bwino kwambiri, amtengowapatali; Iye anadzoza mapazi a Yesu napukuta ndi tsitsi lake. Ndipo nyumba yonse inadzaza ndi fungo lonunkhira bwino la mafutawo.
4 Koma mmodzi wa ophunzira ake, Yudasi Isikarioti, amene pambuyo pake adzamupereka anati, 5 “Nʼchifukwa chiyani mafuta awa sanagulitsidwe ndipo ndalama zake nʼkuzipereka kwa osauka?” Mafutawo anali a mtengo wa malipiro a chaka chimodzi. 6 Iye sananene izi chifukwa cha kuganizira osauka koma chifukwa anali mbava; ngati wosunga thumba la ndalama, amabamo zomwe ankayikamo.
7 Yesu anayankha kuti, “Mulekeni. Mafutawa anayenera kusungidwa mpaka tsiku loyika maliro anga. 8 Inu mudzakhala ndi osauka nthawi zonse, koma simudzakhala nane nthawi zonse.”
9 Pa nthawi imeneyi gulu lalikulu la Ayuda linadziwa kuti Yesu anali kumeneko, ndipo linabwera, sichifukwa cha Iye yekha koma kudzaonanso Lazaro, amene anamuukitsa kwa akufa. 10 Choncho akulu a ansembe anakonza njira yoti aphenso Lazaro, 11 pakuti chifukwa cha iye Ayuda ambiri amapita kwa Yesu ndi kumukhulupirira.
The Word of God in Contemporary Chichewa Copyright © 2002, 2016 by Biblica, Inc.® Used by permission of Biblica, Inc.® All rights reserved worldwide. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Mwini © 2002, 2016 ndi Biblica, Inc.® Kugwiritsa ntchito mwachilolezo. Umwini ndi otetezedwa pa dziko lonse.