Revised Common Lectionary (Semicontinuous)
Beti
9 Kodi mnyamata angathe bwanji kuyeretsa mayendedwe ake?
Akawasamala potsata mawu anu.
10 Ndimakufunafunani ndi mtima wanga wonse;
musalole kuti ndisochere kuchoka pa malamulo anu.
11 Ndasunga mawu anu mu mtima mwanga
kuti ndisakuchimwireni.
12 Mutamandike Inu Yehova;
phunzitseni malamulo anu.
13 Ndi milomo yanga ndimafotokoza malamulo anu onse
amene amachokera pakamwa panu.
14 Ndimakondwera potsatira malamulo anu
monga momwe munthu amakondwera akakhala ndi chuma chambiri.
15 Ndimalingalira malangizo anu
ndipo ndimaganizira njira zanu.
16 Ndimakondwera ndi malamulo anu;
sindidzayiwala konse mawu anu.
Israeli Wosankhidwa wa Yehova
44 Yehova akuti, “Mvera tsopano, iwe Yakobo, mtumiki wanga,
Israeli, amene ndinakusankha.
2 Yehova
amene anakupanga iwe, anakuwumba iwe mʼmimba ya amayi ako,
ndi amene adzakuthandiza iwe. Iye akuti,
Usachite mantha, iwe Yakobo, mtumiki wanga,
Yesuruni, amene ndinakusankha.
3 Pakuti ndidzathira madzi pa nthaka yowuma,
ndi kuyendetsa mitsinje mʼdziko lowuma;
ndidzatumiza Mzimu wanga pa ana anu,
ndi kutsitsa madalitso anga pa zidzukulu zanu.
4 Iwo adzakula ngati udzu wothirira bwino
ndi ngati bango lomera mʼmbali mwa mitsinje ya madzi oyenda.
5 Wina adzanena kuti, ‘Ine ndine wa Yehova;’
wina adzadzitcha yekha wa banja la Yakobo;
winanso adzalemba pa dzanja lake, ‘Wa Yehova’
ndipo adzadzitcha wa banja la Israeli.
Yehova, Osati Mafano
6 “Yehova Mfumu
ndi Mpulumutsi wa Israeli, Yehova Wamphamvuzonse akuti:
Ine ndine woyamba ndi wotsiriza;
palibenso Mulungu wina koma Ine ndekha.
7 Ndani nanga angafanane ndi Ine? Muloleni kuti ayankhule.
Muloleni andifotokozere ndi kundiyalira bwino lomwe
zimene zinachitika kuyambira pamene ndinkakhazikitsa anthu anga akalekale,
ndi ziti zimene zidzachitike;
inde, muloleni alosere zimene zikubwera.
8 Musanjenjemere, musachite mantha.
Kodi sindinakuwuzeni zimenezi ndi kuzilosera kalekale lomwe?
Inu ndinu mboni zanga. Kodi aliponso Mulungu wina kupatula Ine?
Ayi, palibe Thanthwe linanso limene sindikulidziwa.”
Uthenga wa Petro
14 Koma Petro anayimirira pamodzi ndi atumwi khumi ndi mmodziwo ndipo anakweza mawu ake nayankhula kwa gulu la anthu nati: “Ayuda anzanga, ndi nonse amene muli mu Yerusalemu, mvetsetsani izi ndipo tcherani khutu ku zimene ndikunena. 15 Kunena zoona, anthu awa sanaledzere ayi, monga momwe mukuganizira, pakuti ino ndi 9 koloko mmawa! 16 Koma izi ndi zimene ananena Mneneri Yoweli kuti:
17 “ ‘Mulungu akuti, mʼmasiku otsiriza
ndidzakhuthulira Mzimu wanga pa anthu onse.
Ana anu aamuna ndi aakazi adzanenera,
anyamata anu adzaona masomphenya,
nkhalamba zanu zidzalota maloto.
18 Ngakhalenso pa antchito anga aamuna ndi aakazi,
ndidzakhuthulira Mzimu wanga masiku amenewo,
ndipo iwo adzanenera.
19 Ndipo ndidzaonetsa zodabwitsa mlengalenga
ndi zizindikiro pa dziko lapansi pano,
ndizo magazi, moto ndi utsi watolotolo.
20 Dzuwa lidzadetsedwa
ndipo mwezi udzaoneka ngati magazi
lisanafike tsiku lalikulu ndi laulemerero la Ambuye.
21 Ndipo aliyense amene adzayitana
pa dzina la Ambuye adzapulumuka.’
22 “Inu Aisraeli mverani mawu awa; Yesu wa ku Nazareti anali munthu amene anaperekedwa kwa inu ndi Mulungu. Ndipo Mulungu anakutsimikizirani zimenezi ndi zamphamvu, zodabwitsa ndi zizindikiro zimene anachita mwa Iye pakati panu, monga inu mukudziwa. 23 Yesu ameneyu anaperekedwa kwa inu mwa kufuna ndi kudziwiratu kwa Mulungu; ndipo inu mothandizidwa ndi anthu oyipa, munamupha Iye pomupachika pa mtanda. 24 Koma Mulungu anamuukitsa kwa akufa, kumumasula Iye ku zowawa za imfa, chifukwa kunali kosatheka kuti agwiridwe ndi imfa.
The Word of God in Contemporary Chichewa Copyright © 2002, 2016 by Biblica, Inc.® Used by permission of Biblica, Inc.® All rights reserved worldwide. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Mwini © 2002, 2016 ndi Biblica, Inc.® Kugwiritsa ntchito mwachilolezo. Umwini ndi otetezedwa pa dziko lonse.