Print Page Options
Previous Prev Day Next DayNext

Revised Common Lectionary (Semicontinuous)

Daily Bible readings that follow the church liturgical year, with sequential stories told across multiple weeks.
Duration: 1245 days
Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero (CCL)
Version
Yeremiya 31:31-34

31 “Masiku akubwera,” akutero Yehova,
    “pamene ndidzachita pangano latsopano
ndi Aisraeli
    ndiponso nyumba ya Yuda.
32 Silidzakhala ngati pangano
    limene ndinachita ndi makolo awo
pamene ndinawagwira padzanja
    nʼkuwatulutsa ku Igupto;
chifukwa anaphwanya pangano langa,
    ngakhale ndinali mwamuna wawo,”
            akutero Yehova.
33 “Ili ndi pangano limene ndidzachita ndi Aisraeli
    atapita masiku amenewo,” akutero Yehova.
“Ndidzayika lamulo langa mʼmitima mwawo
    ndi kulilemba mʼmaganizo mwawo.
Ine ndidzakhala Mulungu wawo
    ndipo iwo adzakhala anthu anga.
34 Sipadzafunikanso kuti wina aphunzitse mnzake,
    kapena munthu wina kuphunzitsa mʼbale wake, kunena kuti, ‘Mudziwe Yehova,’
chifukwa onse adzandidziwa Ine,
    kuyambira wamngʼono mpaka wamkulu,”
            akutero Yehova.
“Ndidzawakhululukira zoyipa zawo
    ndipo sindidzakumbukiranso machimo awo.”

Masalimo 51:1-12

Kwa mtsogoleri wa mayimbidwe. Salimo la Davide. Pamene Mneneri Natani anabwera kwa iye atachita chigololo ndi Batiseba.

51 Mundichitire chifundo, Inu Mulungu,
    molingana ndi chikondi chanu chosasinthika;
molingana ndi chifundo chanu chachikulu
    mufafanize mphulupulu zanga.
Munditsuke zolakwa zanga zonse
    ndipo mundiyeretse kuchotsa tchimo langa.

Pakuti ndikudziwa mphulupulu zanga,
    ndipo tchimo langa lili pamaso panga nthawi zonse.
Motsutsana ndi Inu, Inu nokha, ndachimwa
    ndipo ndachita zoyipa pamaso panu,
Kotero kuti inu mwapezeka kuti ndinu wolungama
    pamene muyankhula ndi pamene muweruza.
Zoonadi ine ndinali wochimwa pomwe ndimabadwa,
    wochimwa kuyambira pa nthawi imene amayi anga anakhala woyembekezera ine.
Zoonadi inu mumafuna choonadi mu ziwalo zamʼkati mwanga;
    mumandiphunzitsa nzeru mʼkati mwanga mwenimweni.

Mundiyeretse ndi hisope ndipo ndidzayera,
    munditsuke ndipo ndidzayera kuposa matalala
Mundilole ndimve chimwemwe ndi chisangalalo,
    mulole kuti mafupa amene mwawamphwanya akondwere.
Mufulatire machimo anga
    ndi kufafaniza zolakwa zanga zonse.

10 Mulenge mʼkati mwanga mtima woyera Inu Mulungu
    ndi kukonzanso mzimu wokhazikika mwa ine.
11 Musandichotse pamaso panu
    kapena kuchotsa Mzimu wanu Woyera mwa ine.
12 Bwezeretsani mwa ine chimwemwe cha chipulumutso chanu
    ndipo mundipatse mzimu wofuna kumvera kuti undilimbitse.

Masalimo 119:9-16

Beti

Kodi mnyamata angathe bwanji kuyeretsa mayendedwe ake?
    Akawasamala potsata mawu anu.
10 Ndimakufunafunani ndi mtima wanga wonse;
    musalole kuti ndisochere kuchoka pa malamulo anu.
11 Ndasunga mawu anu mu mtima mwanga
    kuti ndisakuchimwireni.
12 Mutamandike Inu Yehova;
    phunzitseni malamulo anu.
13 Ndi milomo yanga ndimafotokoza malamulo anu onse
    amene amachokera pakamwa panu.
14 Ndimakondwera potsatira malamulo anu
    monga momwe munthu amakondwera akakhala ndi chuma chambiri.
15 Ndimalingalira malangizo anu
    ndipo ndimaganizira njira zanu.
16 Ndimakondwera ndi malamulo anu;
    sindidzayiwala konse mawu anu.

Ahebri 5:5-10

Nʼchifukwa chake Khristu sanadzipatse yekha ulemu wokhala Mkulu wa ansembe. Koma Mulungu anamuwuza kuti,

“Iwe ndiwe Mwana wanga;
    Ine lero ndakhala Atate ako.”

Ndipo penanso anati,

“Iwe ndiwe wansembe mpaka muyaya,
    monga mwa unsembe wa Melikizedeki.”

Yesu, pa nthawi imene anali munthu pa dziko lapansi pano, anapereka mapemphero ake ndi zopempha mofuwula ndi misozi kwa Iye amene akanamupulumutsa ku imfa, ndipo anamumvera chifukwa anagonjera modzipereka. Ngakhale Iye anali Mwana wa Mulungu anaphunzira kumvera pomva zowawa. Atasanduka wangwiro kotheratu, anakhala gwero la chipulumutso chosatha kwa onse omvera Iye. 10 Ndipo Mulungu anamuyika kukhala Mkulu wa ansembe, monga mwa dongosolo la unsembe wa Melikizedeki.

Yohane 12:20-33

Agriki Afuna Kuona Yesu

20 Tsopano panali Agriki ena pakati pa amene anapita kukapembedza ku phwando. 21 Iwo anabwera kwa Filipo, wochokera ku Betisaida wa ku Galileya, ndi pempho, nati, “Akulu, ife tikufuna kuona Yesu.” 22 Filipo anapita kukawuza Andreya; Andreya ndi Filipo pamodzi anakawuza Yesu.

23 Yesu anayankha kuti, “Nthawi yafika yakuti Mwana wa Munthu alemekezedwe. 24 Zoonadi, Ine ndikukuwuzani kuti, ‘Mbewu ya tirigu imakhala imodzi yokha ngati sikugwa mʼnthaka ndi kufa. Koma ngati imfa, imabereka mbewu zambiri.’ 25 Munthu amene amakonda moyo wake adzawutaya, pamene munthu amene amadana ndi moyo wake mʼdziko lino lapansi adzawusungira ku moyo wosatha. 26 Aliyense amene atumikira Ine ayenera kunditsata; ndipo kumene Ine ndili, wotumikira wanga adzakhalanso komweko. Atate anga adzalemekeza amene atumikira Ine.

27 “Moyo wanga ukuvutika tsopano, kodi ndidzanena chiyani? Ndinene kuti Atate pulumutseni ku nthawi ino? Ayi. Chifukwa chimene Ine ndinabwera pa nthawi iyi ndi chimenechi. 28 Atate, lemekezani dzina lanu!”

Kenaka mawu anabwera kuchokera kumwamba, “Ine ndalilemekeza, ndipo ndidzalilemekezanso.” 29 Gulu la anthu lomwe linali pamenepo litamva linati, “Kwagunda bingu,” ena anati, “Mngelo wayankhula kwa Iye.”

30 Yesu anati, “Mawu awa abwera chifukwa cha inu osati chifukwa cha Ine. 31 Ino tsopano ndi nthawi yachiweruzo pa dziko lapansi; tsopano olamulira wa dziko lapansi adzathamangitsidwa. 32 Koma Ine, akadzandipachika pa dziko lapansi, ndidzakokera anthu onse kwa Ine.” 33 Iye ananena izi kuti aonetse mmene adzafere.

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero (CCL)

The Word of God in Contemporary Chichewa Copyright © 2002, 2016 by Biblica, Inc.® Used by permission of Biblica, Inc.® All rights reserved worldwide. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Mwini © 2002, 2016 ndi Biblica, Inc.® Kugwiritsa ntchito mwachilolezo. Umwini ndi otetezedwa pa dziko lonse.