Print Page Options
Previous Prev Day Next DayNext

Revised Common Lectionary (Semicontinuous)

Daily Bible readings that follow the church liturgical year, with sequential stories told across multiple weeks.
Duration: 1245 days
Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero (CCL)
Version
Masalimo 75

Kwa mtsogoleri wa mayimbidwe, potsata mayimbidwe a “Musawononge.” Salimo la Asafu. Nyimbo.

75 Tikuthokoza Inu Mulungu,
    tikuthokoza, pakuti dzina lanu lili pafupi nafe,
    anthutu amafotokoza za ntchito zanu zodabwitsa.

Mumati, “Ine ndimayika nthawi yoyenera,
    ndine amene ndimaweruza mwachilungamo.
Pamene dziko lapansi ndi anthu ake onse anjenjemera,
    ndine amene ndimagwiriziza mizati yake molimba.
            Sela
Kwa odzitama ndikuti, ‘Musadzitamenso,’
    ndipo kwa oyipa, ‘Musatukulenso nyanga zanu.
Musatukule nyanga zanu motsutsana ndi kumwamba;
    musayankhule ndi khosi losololoka.’ ”

Kugamula milandu sikuchokera kummawa kapena kumadzulo
    kapena ku chipululu.
Koma ndi Mulungu amene amaweruza:
    Iyeyo amatsitsa wina, nakwezanso wina.
Mʼdzanja la Yehova muli chikho
    chodzaza ndi vinyo wochita thovu, wosakanizidwa ndi zokometsera;
Iye amamutsanulira pansi ndipo onse oyipa a dziko lapansi
    amamwa ndi senga zake zonse.

Kunena za ine, ndidzalengeza izi kwamuyaya;
    ndidzayimba matamando kwa Mulungu wa Yakobo.
10 Ndidzadula nyanga za onse oyipa
    koma nyanga za olungama zidzakwezedwa.

Yobu 41:1-11

41 “Kodi ungathe kukoka ngʼona ndi mbedza ya nsomba
    kapena kukanikiza lilime lake pansi ndi chingwe?
Kodi ungathe kumanga chingwe mʼmphuno mwake,
    kapena kubowola nsagwada zake ndi mbedza?
Kodi ngʼonayo idzakupempha kuti uyichitire chifundo?
    Kodi idzakuyankhula ndi mawu ofatsa?
Kodi idzachita nawe mgwirizano
    kuti uyisandutse kapolo wako mpaka muyaya?
Kodi udzasewera nayo ngati mbalame,
    kapena kuyimangirira kuti atsikana ako asewere nayo?
Kodi anthu adzayitsatsa malonda?
    Nanga amalondawo nʼkugawanagawana nyama yake kuti akagulitse?
Kodi chikopa chake ungathe kuchilasa ndi zisonga,
    kapena kubowola mutu wake ndi nthungo zophera nsomba?
Ukayiputa udziwe kuti pali nkhondo,
    ndipo iweyo sudzabwereranso.
Chiyembekezo choti nʼkuyigonjetsa ndi chabodza;
    kungoyiona kokha, ndithu iwe kumangodzigwera wekha.
10 Palibe wolimba mtima kuti ndi kuyiputa.
    Ndani angalimbe mtima kulimbana ndi Ine?
11 Kodi ndani anandipatsa kanthu kuti ndimubwezere?
    Zonse za pansi pa thambo ndi zanga.

Ahebri 6:13-20

Kukhazikika kwa Malonjezo a Mulungu

13 Pamene Mulungu ankamulonjeza Abrahamu, popeza panalibe wamkulu womuposa, amene akanamutchula ndikulumbira mwa Iye, analumbira mwa Iye yekha kuti, 14 “Ine ndidzakudalitsa ndithu, ndipo ndidzakupatsa zidzukulu zambiri.” 15 Ndipo Abrahamu atayembekezera mofatsa, analandira zimene anamulonjezazo.

16 Anthu amalumbira mʼdzina la wina amene akuwaposa, ndipo lumbiro lotere limatsimikizira zomwe zayankhulidwa ndi kuthetsa mikangano yonse. 17 Momwemonso Mulungu pofuna kutsimikizira anthu amene adzalandire lonjezo, kuti Iye sangasinthe maganizo, anatsimikiza lonjezo lakelo ndi lumbiro. 18 Mulungu anachita zinthu ziwiri, lonjezo ndi lumbiro, zimene sizingathe kusintha ndipo Mulungu sangathe kunama. Choncho Mulungu akutilimbikitsa mtima ife amene tinathawira kwa Iye kuti tichigwiritsitse chiyembekezo chimene tinalandira. 19 Chiyembekezo chimenechi tili nacho ngati nangula wa moyo wathu. Nʼchokhazikika ndi chosagwedezeka ndipo chimalowa mʼkatikati mwa malo opatulika, kuseri kwa chinsalu chotchinga. 20 Yesu anatitsogolera kupita kumeneko, nalowako mʼmalo mwathu. Iye anasanduka Mkulu wa ansembe onse wamuyaya, monga mwa dongosolo la unsembe wa Melikizedeki.

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero (CCL)

The Word of God in Contemporary Chichewa Copyright © 2002, 2016 by Biblica, Inc.® Used by permission of Biblica, Inc.® All rights reserved worldwide. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Mwini © 2002, 2016 ndi Biblica, Inc.® Kugwiritsa ntchito mwachilolezo. Umwini ndi otetezedwa pa dziko lonse.