Revised Common Lectionary (Semicontinuous)
Yehova Ayankhula
38 Apo Yehova anamuyankha Yobu mʼkamvuluvulu. Ndipo anati:
2 “Kodi uyu ndani amene akusokoneza uphungu wanga
poyankhula mawu opanda nzeru?
3 Onetsa chamuna;
ndikufunsa
ndipo undiyankhe.
4 “Kodi unali kuti pamene ndinkayika maziko a dziko lapansi?
Ndiwuze ngati ukudziwa.
5 Ndani amene analemba malire ake? Ndithudi iwe ukudziwa!
Ndani amene anayeza ndi chingwe dzikoli?
6 Kodi maziko ake anawakumba potani,
kapena ndani anayika mwala wake wapangodya,
7 pamene nyenyezi za kummawa zinkayimba pamodzi
ndipo angelo onse a Mulungu ankafuwula mokondwa?
34 “Kodi iwe ungathe kulamula mitambo
kuti igwetse mvula ya chigumula?
35 Kodi ungathe kutumiza zingʼaningʼani kuti zingʼanime?
Kodi zimabwera pamaso pako ndi kuti, ‘Tili pano?’
36 Kodi ndani anayika nzeru mu mtima,
ndani analonga mʼmaganizo nzeru zomvetsa zinthu?
37 Wanzeru ndani amene angathe kuwerenga mitambo?
Ndani angathe kupendeketsa mitsuko ya madzi akuthambo
38 pamene fumbi limasanduka matope,
ndipo matopewo amawumbika?
39 “Kodi ndani amawusakira chakudya mkango waukazi
ndi kukhutitsa misona ya mikango
40 pamene ili khale mʼmapanga mwawo
kapena pamene ikubisala pa tchire?
41 Kodi amamupatsa khwangwala chakudya chake ndani
pamene ana ake akulirira kwa Mulungu
ndi kumayendayenda chifukwa chosowa zakudya?
104 Tamanda Yehova, iwe moyo wanga.
Inu Yehova Mulungu wanga, ndinu wamkulu kwambiri;
mwavala ulemerero ndi ufumu.
2 Iye wadzifunditsa kuwala ngati chovala;
watambasula miyamba ngati tenti
3 ndipo wayika pa madzi mitanda ya chipinda chake.
Iye amasandutsa mitambo kukhala galeta lake,
ndi kuwuluka pa mapiko a mphepo.
4 Amapanga mphepo kukhala amithenga ake,
malawi amoto kukhala atumiki ake.
5 Anakhazikitsa dziko lapansi pa maziko ake;
silingasunthike.
6 Munaliphimba ndi nyanja yozama ngati chovala;
madzi anayimirira pamwamba pa mapiri.
7 Koma pakudzudzula kwanu madzi anathawa,
pa mkokomo wa bingu lanu iwo anamwazika;
8 Inu munamiza mapiri,
iwo anatsikira ku zigwa
kumalo kumene munawakonzera.
9 Inu munayika malire ndipo sangathe kudutsa,
iwo sadzamizanso dziko lapansi.
24 Ntchito zanu ndi zochulukadi Inu Yehova!
Munazipanga zonse mwanzeru,
dziko lapansi ladzaza ndi zolengedwa zanu.
35 Koma anthu ochimwa awonongeke pa dziko lapansi
ndipo anthu oyipa asapezekenso.
Tamanda Yehova, Iwe moyo wanga.
Tamandani Yehova.
5 Mkulu wa ansembe aliyense amasankhidwa kuchokera pakati pa anthu ndipo amayikidwa kuti aziwayimirira pamaso pa Mulungu, kuti azipereka mphatso ndi nsembe chifukwa cha machimo. 2 Popeza kuti iye mwini ali ndi zofowoka zake, amatha kuwalezera mtima amene ali osadziwa ndi osochera. 3 Chifukwa cha ichi, iye amadziperekera nsembe chifukwa cha machimo ake omwe ndiponso chifukwa cha machimo a anthu ena.
4 Palibe amene amadzipatsa yekha ulemu wotere, koma amachita kuyitanidwa ndi Mulungu monga momwe anayitanidwira Aaroni. 5 Nʼchifukwa chake Khristu sanadzipatse yekha ulemu wokhala Mkulu wa ansembe. Koma Mulungu anamuwuza kuti,
“Iwe ndiwe Mwana wanga;
Ine lero ndakhala Atate ako.”
6 Ndipo penanso anati,
“Iwe ndiwe wansembe mpaka muyaya,
monga mwa unsembe wa Melikizedeki.”
7 Yesu, pa nthawi imene anali munthu pa dziko lapansi pano, anapereka mapemphero ake ndi zopempha mofuwula ndi misozi kwa Iye amene akanamupulumutsa ku imfa, ndipo anamumvera chifukwa anagonjera modzipereka. 8 Ngakhale Iye anali Mwana wa Mulungu anaphunzira kumvera pomva zowawa. 9 Atasanduka wangwiro kotheratu, anakhala gwero la chipulumutso chosatha kwa onse omvera Iye. 10 Ndipo Mulungu anamuyika kukhala Mkulu wa ansembe, monga mwa dongosolo la unsembe wa Melikizedeki.
Pempho la Yakobo ndi Yohane
35 Ndipo Yakobo ndi Yohane, ana a Zebedayo, anabwera kwa Iye ndipo anati, “Aphunzitsi, tikufuna kuti mutichitire ife chilichonse chimene tipemphe.”
36 Iye anafunsa kuti, “Kodi mukufuna ndikuchitireni chiyani?”
37 Iwo anayankha kuti, “Timafuna kuti mmodzi wa ife adzakhale kumanja ndi wina kumanzere mu ulemerero wanu.”
38 Yesu anati, “Simukudziwa chimene mukupempha. Kodi mungamwere chikho chimene ndidzamwera kapena kubatizidwa ndi ubatizo umene ndibatizidwe nawo?”
39 Iwo anayankha kuti, “Tikhoza.” Yesu anawawuza kuti, “Mudzamweradi chikho chimene Ine ndidzamwera, ndi kubatizidwa ndi ubatizo umene Ine ndidzabatizidwe nawo, 40 koma kukhala kumanja kapena kumanzere si Ine wopereka. Malo awa ndi a amene anasankhidwiratu.”
41 Ophunzira khumiwo otsalawo atamva izi anapsera mtima Yakobo ndi Yohane. 42 Yesu anawayitana pamodzi nati, “Inu mukudziwa kuti iwo amene amadziyesa ngati atsogoleri a anthu amitundu ina amadyera anthu awo masuku pamutu. Akuluakulu awonso amaonetsadi mphamvu zawo pa iwo. 43 Sizili choncho ndi inu. Mʼmalo mwake, amene akufuna kukhala wamkulu pakati panu ayenera kukhala wotumikira, 44 ndipo aliyense amene akufuna kukhala wamkulu akhale kapolo wa onse. 45 Pakuti ngakhale Mwana wa Munthu sanabwere kudzatumikiridwa, koma kudzatumikira, ndi kupereka moyo wake kuti ukhale dipo la anthu ambiri.”
The Word of God in Contemporary Chichewa Copyright © 2002, 2016 by Biblica, Inc.® Used by permission of Biblica, Inc.® All rights reserved worldwide. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Mwini © 2002, 2016 ndi Biblica, Inc.® Kugwiritsa ntchito mwachilolezo. Umwini ndi otetezedwa pa dziko lonse.