Revised Common Lectionary (Semicontinuous)
Kwa mtsogoleri wa mayimbidwe, potsata mayimbidwe a “Musawononge.” Salimo la Asafu. Nyimbo.
75 Tikuthokoza Inu Mulungu,
tikuthokoza, pakuti dzina lanu lili pafupi nafe,
anthutu amafotokoza za ntchito zanu zodabwitsa.
2 Mumati, “Ine ndimayika nthawi yoyenera,
ndine amene ndimaweruza mwachilungamo.
3 Pamene dziko lapansi ndi anthu ake onse anjenjemera,
ndine amene ndimagwiriziza mizati yake molimba.
Sela
4 Kwa odzitama ndikuti, ‘Musadzitamenso,’
ndipo kwa oyipa, ‘Musatukulenso nyanga zanu.
5 Musatukule nyanga zanu motsutsana ndi kumwamba;
musayankhule ndi khosi losololoka.’ ”
6 Kugamula milandu sikuchokera kummawa kapena kumadzulo
kapena ku chipululu.
7 Koma ndi Mulungu amene amaweruza:
Iyeyo amatsitsa wina, nakwezanso wina.
8 Mʼdzanja la Yehova muli chikho
chodzaza ndi vinyo wochita thovu, wosakanizidwa ndi zokometsera;
Iye amamutsanulira pansi ndipo onse oyipa a dziko lapansi
amamwa ndi senga zake zonse.
9 Kunena za ine, ndidzalengeza izi kwamuyaya;
ndidzayimba matamando kwa Mulungu wa Yakobo.
10 Ndidzadula nyanga za onse oyipa
koma nyanga za olungama zidzakwezedwa.
40 Yehova anati kwa Yobu:
2 “Kodi iwe ufuna kukangana ndi Wamphamvuzonse?
Iwe amene unatsutsana ndi Mulungu umuyankhe Iyeyo!”
3 Pamenepo Yobu anayankha Yehova:
4 “Ine sindili kanthu konse,
kodi ndingathe kukuyankhani chiyani? Ndagwira pakamwa panga.
5 Ndinayankhula kamodzi, koma pano ndilibe yankho,
ndinayankha kawiri, koma sindiwonjezeranso mawu ena.”
6 Ndipo Yehova anayankha Yobu mʼkamvuluvulu kuti,
7 “Tsopano vala dzilimbe ngati mwamuna;
ndikufunsa mafunso
ndipo iwe undiyankhe.
8 “Kodi iwe unganyoze chiweruzo changa cholungama?
Kodi ungandidzudzule kuti iweyo ukhale wolungama?
9 Kodi uli ndi dzanja monga la Mulungu,
ndipo mawu ako angagunde ngati mphenzi monga a Mulungu?
10 Ngati zili choncho udzikometsere ndi ulemerero ndi kukongola,
ndipo udziveke ulemu ndi ulemerero waufumu.
11 Tsanula ukali wako wosefukirawo,
uyangʼane aliyense wodzikuza ndipo umuchepetse,
12 Uyangʼane aliyense wodzikweza ndipo umutsitse,
uwapondereze oyipa onse pamalo pomwe alilipo.
13 Onsewo uwakwirire pamodzi mfumbi;
ukulunge nkhope zawo mʼmanda.
14 Ukatero Ine ndidzakuvomereza
kuti dzanja lako lamanja lakupulumutsadi.
15 “Taganiza za mvuwu,
imene ndinayipanga monga momwe ndinapangira iwe,
ndipo imadya udzu ngati ngʼombe.
16 Mphamvu zake ndi zazikulu kwambiri,
thupi lake ndi lanyonga kwambiri!
17 Mchira wake umayima tolotolo ngati mtengo wamkungudza;
mitsempha ya ntchafu zake ndi yogwirana bwino.
18 Mafupa ake ali ngati mapayipi amkuwa,
nthiti zake zili ngati mipiringidzo yachitsulo.
19 Mvuwuyo ndi yayikulu mwa zolengedwa za Mulungu,
komatu mlengi wake amatha kuyiopseza ndi lupanga lake.
20 Imapeza chakudya chake ku mtunda
ndipo nyama zakuthengo zonse zimasewera pambali pake.
21 Imagona pa tsinde pa zitsamba za mipeta,
imabisala mʼbango ndiponso pa thawale.
22 Imaphimbika ndi mthunzi wazitsamba za mipeta;
imazunguliridwa ndi misondozi ya mu mtsinje.
23 Madzi a mu mtsinje akakokoma, sichita mantha,
iyo sitekeseka, ngakhale madzi a mu Yorodani afike mʼkhosi mwake.
24 Kodi alipo amene angathe kukola mvuwu ndi mbedza
kapena kuyikola mu msampha?
6 Tsono tiyeni tisangoyima pa maphunziro oyambirira enieni a Khristu koma tipitirire kuti mukule msinkhu. Tisaphunzitsenso zinthu zomwe zili ngati maziko, monga za kutembenuka mtima kusiya ntchito zosapindulitsa pa moyo wosatha, za kukhulupirira Mulungu, 2 za maubatizo, za kusanjika manja, za kuuka kwa akufa ndi za chiweruzo chotsiriza. 3 Ndipo Mulungu akalola, tidzaterodi.
4 Nʼkosatheka kuwabwezanso anthu amene nthawi ina anawunikiridwa. Iwowa analawapo mphatso yochokera kumwamba, nʼkulandira nawo Mzimu Woyera. 5 Analawa kukoma kwa mawu a Mulungu ndi mphamvu za nthawi ikubwera. 6 Popeza anabwerera mʼmbuyo, nʼkosatheka kuti atembenukenso mtima chifukwa akupachikanso Mwana wa Mulungu ndi kumunyozetsa poyera.
7 Nthaka yolandira mvula kawirikawiri nʼkubala mbewu zopindulitsa oyilima, Mulungu amayidalitsa. 8 Koma nthaka yobereka minga ndi nthula ndi yopanda phindu ndipo ili pafupi kutembereredwa. Matsiriziro ake idzatenthedwa mʼmoto.
9 Okondedwa anga, ngakhale tikuyankhula zimenezi, ife tikudziwa kuti muli nazo zinthu zabwino zomwe zimabwera pamodzi ndi chipulumutso. 10 Mulungu ndi wolungama, sangayiwale ntchito zanu ndi chikondi chanu chimene munamuonetsa pothandiza anthu ake monga mmene mukuchitirabe tsopano. 11 Ife tikufuna kuti aliyense wa inu aonetse changu chomwechi mpaka kumapeto, kuti zichitikedi zomwe mukuyembekezera. 12 Ife sitikufuna kuti inu mukhale aulesi, koma mutsatire anthu amene, pokhulupirira ndi kupirira, akulandira zimene zinalonjezedwa.
The Word of God in Contemporary Chichewa Copyright © 2002, 2016 by Biblica, Inc.® Used by permission of Biblica, Inc.® All rights reserved worldwide. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Mwini © 2002, 2016 ndi Biblica, Inc.® Kugwiritsa ntchito mwachilolezo. Umwini ndi otetezedwa pa dziko lonse.