Print Page Options
Previous Prev Day Next DayNext

Revised Common Lectionary (Semicontinuous)

Daily Bible readings that follow the church liturgical year, with sequential stories told across multiple weeks.
Duration: 1245 days
Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero (CCL)
Version
Masalimo 45:1-2

Kwa mtsogoleri wamayimbidwe. Monga mwa mayimbidwe a “Maluwa a Kakombo.” Salimo la ana a Kora. Nyimbo ya pa ukwati.

45 Mtima wanga watakasika ndi nkhani yokoma
    pamene ndikulakatula mawu anga kwa mfumu;
    lilime langa ndi cholembera cha wolemba waluso.

Inu ndinu abwino kwambiri kuposa anthu onse
    ndipo milomo yanu inadzozedwa ndi chikondi cha Mulungu chosasinthika,
    popeza Mulungu wakudalitsani kwamuyaya.

Masalimo 45:6-9

Mpando wanu waufumu, Inu Mulungu, udzakhala ku nthawi za nthawi;
    ndodo yaufumu yachilungamo idzakhala ndodo yaufumu ya ufumu wanu.
Inu mumakonda chilungamo ndi kudana ndi zoyipa;
    choncho Mulungu, Mulungu wanu, wakukhazikani pamwamba pa anzanu
    pokudzozani ndi mafuta a chimwemwe.
Mikanjo yanu yonse ndi yonunkhira ndi mure ndi aloe ndi kasiya;
    kuchokera ku nyumba zaufumu zokongoletsedwa ndi mnyanga wanjovu
    nyimbo za zoyimbira zazingwe zimakusangalatsani.
Ana aakazi a mafumu ali pakati pa akazi anu olemekezeka;
    ku dzanja lanu lamanja kuli mkwatibwi waufumu ali mu golide wa ku Ofiri.

Nyimbo ya Solomoni 2:1-7

Mkazi

Ine ndine duwa la ku Saroni,
    duwa lokongola la ku zigwa.

Mwamuna

Monga duwa lokongola pakati pa minga
    ndi momwe alili wokondedwa wanga pakati pa atsikana.

Mkazi

Monga mtengo wa apulosi pakati pa mitengo ya mʼnkhalango
    ndi momwe alili bwenzi langa pakati pa anyamata.
Ndimakondwera kukhala pansi pa mthunzi wako,
    ndipo chipatso chake ndi chokoma mʼkamwa mwanga.
Iye wanditengera ku nyumba yaphwando,
    ndipo mbendera yake yozika pa ine ndi chikondi.
Undidyetse keke ya mphesa zowuma,
    unditsitsimutse ndi ma apulosi,
    pakuti chikondi chandifowoketsa.
Mutu wanga watsamira dzanja lake lamanzere,
    ndipo dzanja lake lamanja landikumbatira.
Inu akazi a ku Yerusalemu, ndithu ndikukupemphani
    pali gwape ndi mbawala yayikazi zakuthengo:
Musachigwedeze chikondi kapena kuchiutsa
    mpaka pamene chifunire ichocho.

Yakobo 1:9-16

Abale omwe ndi anthu wamba anyadire pamene akwezedwa. 10 Koma olemera anyadire pamene atsitsidwa, chifukwa adzatha ngati duwa lakuthengo. 11 Pakuti dzuwa limatuluka nʼkutentha kwake, ndipo limafotetsa zomera. Duwa lake limathothoka ndipo kukongola kwake kumatheratu. Momwemonso munthu wachuma adzazimirira ngakhale atamachitabe malonda ake.

12 Wodala ndi munthu amene amapirira mʼmayesero, chifukwa akapambana adzalandira chipewa cha ulemerero chimene Mulungu analonjeza anthu amene amamukonda.

13 Munthu akayesedwa asanene kuti, “Mulungu akundiyesa.” Pakuti Mulungu sangayesedwe ndi choyipa kapena Iyeyo kuyesa munthu aliyense. 14 Koma munthu aliyense amayesedwa akakokedwa ndi zilakolako zake zoyipa ndi kukopedwa nazo. 15 Pamenepo, chilakolako chikakula chimabala tchimo; ndipo tchimo likakhwima limabereka imfa.

16 Musanyengedwe abale anga okondedwa.

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero (CCL)

The Word of God in Contemporary Chichewa Copyright © 2002, 2016 by Biblica, Inc.® Used by permission of Biblica, Inc.® All rights reserved worldwide. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Mwini © 2002, 2016 ndi Biblica, Inc.® Kugwiritsa ntchito mwachilolezo. Umwini ndi otetezedwa pa dziko lonse.