Print Page Options
Previous Prev Day Next DayNext

Revised Common Lectionary (Semicontinuous)

Daily Bible readings that follow the church liturgical year, with sequential stories told across multiple weeks.
Duration: 1245 days
Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero (CCL)
Version
1 Mafumu 2:10-12

10 Tsono Davide anamwalira ndipo anayikidwa mʼmanda mu Mzinda wa Davide. 11 Iyeyo nʼkuti atalamulira Israeli kwa zaka makumi anayi. Ku Hebroni analamulira zaka zisanu ndi ziwiri ndipo ku Yerusalemu analamulira zaka 33. 12 Choncho Solomoni anakhala pa mpando waufumu wa abambo ake Davide, ndipo ufumu wake unakhazikika kwambiri.

1 Mafumu 3:3-14

Solomoni anaonetsa chikondi chake pa Yehova poyenda motsatira malamulo a abambo ake Davide, kupatula kuti ankapereka nsembe ndi kufukiza lubani ku malo osiyanasiyana achipembedzo.

Mfumu inapita ku Gibiyoni kukapereka nsembe popeza kumeneko ndiye kunali malo oposa malo ofunika kwambiri pachipembedzo. Kumeneko Solomoni anapereka nsembe zopsereza 1,000 pa guwa lansembe. Ku Gibiyoniko Yehova anaonekera kwa Solomoni mʼmaloto usiku, ndipo Mulungu anati, “Pempha chilichonse chimene ukufuna ndipo ndidzakupatsa.”

Solomoni anayankha kuti, “Inu munaonetsa kukoma mtima kwanu kwakukulu kwa kapolo wanu, abambo anga Davide, chifukwa anali wokhulupirika pamaso panu, wolungama mtima ndiponso wa mtima wangwiro. Inu mukupitirizabe kukoma mtima kwanu kwakukulu kwa iye ndipo mwamupatsa mwana kuti akhale pa mpando wake waufumu lero lino.

“Tsopano Inu Yehova Mulungu wanga, mtumiki wanune mwandiyika kukhala mfumu mʼmalo mwa abambo anga Davide. Komatu ndine mwana wamngʼono ndipo sindidziwa kagwiridwe kake ka ntchito yangayi. Mtumiki wanu ali pakati pa anthu amene munawasankha, mtundu waukulu, anthu ochuluka kwambiri osatheka kuwawerenga. Choncho mupatseni mtumiki wanu nzeru zolamulira anthu anu ndi kuti azitha kusiyanitsa pakati pa chabwino ndi choyipa. Pakuti ndani amene angathe kulamulira anthu anu ochulukawa?”

10 Ambuye anakondwera kuti Solomoni anapempha zimenezi. 11 Tsono Mulungu anati kwa Solomoni, “Popeza wapempha zinthu zimenezi osati moyo wautali kapena chuma chako kapena imfa ya adani ako koma nzeru zolamulira anthu mwachilungamo, 12 Ine ndidzakuchitira zimene wapempha. Ndidzakupatsa mtima wanzeru ndi wozindikira zinthu, kotero kuti sipanakhalepo wina wofanana nawe ndipo sipadzapezekanso wina wonga iwe pambuyo pako. 13 Kuwonjeza apo, ndidzakupatsa zimene sunazipemphe: chuma ndi ulemu, kotero kuti pa masiku onse a moyo wako sipadzakhala mfumu yofanana nawe. 14 Ndipo ngati udzayenda mʼnjira zanga ndi kumvera malamulo anga ndiponso malangizo anga monga abambo ako Davide anachitira, ndidzakupatsa moyo wautali.”

Masalimo 111

111 Tamandani Yehova.

Ndidzathokoza Yehova ndi mtima wanga wonse
    mʼbwalo la anthu olungama mtima ndi pa msonkhano.

Ntchito za Yehova nʼzazikulu;
    onse amene amakondwera nazo amazilingalira.
Zochita zake ndi za ulemerero ndi zaufumu,
    ndipo chilungamo chake ndi chosatha.
Iye wachititsa kuti zodabwitsa zake zikumbukirike;
    Yehova ndi wokoma mtima ndi wachifundo.
Amapereka chakudya kwa amene amamuopa Iye;
    amakumbukira pangano lake kwamuyaya.
Waonetsa anthu ake mphamvu ya ntchito zake,
    kuwapatsa mayiko a anthu a mitundu ina.
Ntchito za manja ake ndi zokhulupirika ndi zolungama;
    malangizo ake onse ndi odalirika.
Malamulo ndi okhazikika ku nthawi za nthawi,
    ochitidwa mokhulupirika ndi molungama.
Iyeyo amawombola anthu ake;
    anakhazikitsa pangano lake kwamuyaya
    dzina lake ndi loyera ndi loopsa.

10 Kuopa Yehova ndicho chiyambi cha nzeru;
    onse amene amatsatira malangizo ake amamvetsa bwino zinthu.
    Iye ndi wotamandika mpaka muyaya.

Aefeso 5:15-20

15 Samalani makhalidwe anu, musakhale ngati opanda nzeru koma ngati anzeru. 16 Gwiritsani ntchito mpata uliwonse, chifukwa masiku ano ndi oyipa. 17 Choncho musakhale opusa, koma mudziwe zimene Ambuye akufuna kuti muchite. 18 Musaledzere ndi vinyo, chifukwa adzawononga moyo wanu. Mʼmalo mwake, mudzazidwe ndi Mzimu Woyera. 19 Muziyankhulana wina ndi mnzake mawu a Masalimo, nyimbo za Mulungu ndi nyimbo za uzimu. Muziyimbira Ambuye movomerezana ndi mitima yanu. 20 Muziyamika Mulungu Atate nthawi zonse chifukwa cha zonse, mʼdzina la Ambuye athu Yesu Khristu.

Yohane 6:51-58

51 Ine ndine chakudya chamoyo chochokera kumwamba. Ngati munthu adya chakudya ichi, adzakhala ndi moyo nthawi zonse. Chakudya chimenechi ndi thupi langa, limene Ine ndidzalipereka kuti anthu pa dziko lapansi akhale ndi moyo.”

52 Kenaka Ayuda anayamba kutsutsana kwambiri pakati pawo kuti, “Kodi munthu uyu angathe kutipatsa bwanji thupi lake kuti tidye?”

53 Yesu anawawuza kuti, “Zoonadi, Ine ndikukuwuzani kuti ngati simungadye thupi la Mwana wa Munthu ndi kumwa magazi ake, simungakhale ndi moyo mwa inu. 54 Aliyense amene adya thupi langa ndi kumwa magazi anga ali ndi moyo wosatha ndipo Ine ndidzamuukitsa kwa akufa pa tsiku lomaliza. 55 Pakuti thupi langa ndi chakudya chenicheni ndipo magazi anga ndi chakumwa chenicheni. 56 Aliyense amene adya thupi langa ndi kumwa magazi anga amakhala mwa Ine, ndi Ine mwa iye. 57 Monga Atate amoyo anandituma Ine, ndipo ndili ndi moyo chifukwa cha Atatewo, chomwechonso amene adya thupi langa adzakhala ndi moyo chifukwa cha Ine. 58 Ichi ndiye chakudya chimene chinatsika kuchokera kumwamba. Makolo athu akale anadya mana ndi kufa, koma iye amene adya chakudya ichi, adzakhala ndi moyo nthawi yonse.”

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero (CCL)

The Word of God in Contemporary Chichewa Copyright © 2002, 2016 by Biblica, Inc.® Used by permission of Biblica, Inc.® All rights reserved worldwide. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Mwini © 2002, 2016 ndi Biblica, Inc.® Kugwiritsa ntchito mwachilolezo. Umwini ndi otetezedwa pa dziko lonse.