Print Page Options
Previous Prev Day Next DayNext

Revised Common Lectionary (Semicontinuous)

Daily Bible readings that follow the church liturgical year, with sequential stories told across multiple weeks.
Duration: 1245 days
Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero (CCL)
Version
Masalimo 101

Salimo la Davide.

101 Ndidzayimba za chikondi ndi chiweruzo chanu cholungama;
    kwa Inu Yehova ndidzayimba matamando.
Ndidzatsata njira yolungama;
    nanga mudzabwera liti kwa ine?

Ndidzayenda mʼnyumba mwanga
    ndi mtima wosalakwa.
Sindidzayika chinthu chilichonse choyipa
    pamaso panga.

Ine ndimadana ndi zochita za anthu opanda chikhulupiriro;
    iwo sadzadziphatika kwa ine.
Anthu a mtima wokhota adzakhala kutali ndi ine;
    ine sindidzalola choyipa chilichonse kulowa mwa ine.

Aliyense wosinjirira mnansi wake mseri
    ameneyo ndidzamuletsa;
aliyense amene ali ndi maso amwano ndi mtima wodzikuza,
    ameneyo sindidzamulekerera.

Maso anga adzakhala pa okhulupirika mʼdziko,
    kuti akhale pamodzi ndi ine;
iye amene mayendedwe ake ndi wosalakwa
    adzanditumikira.

Aliyense wochita chinyengo
    sadzakhala mʼnyumba mwanga.
Aliyense woyankhula mwachinyengo
    sadzayima pamaso panga.

Mmawa uliwonse ndidzatontholetsa anthu
    onse oyipa mʼdziko;
ndidzachotsa aliyense wochita zoyipa
    mu mzinda wa Yehova.

1 Mafumu 8:1-21

Abwera ndi Bokosi la Chipangano ku Nyumba ya Yehova

Pamenepo Mfumu Solomoni inasonkhanitsa akuluakulu a Israeli, atsogoleri onse a mafuko ndi akuluakulu a mabanja a Aisraeli mu Yerusalemu, kuti akatenge Bokosi la Chipangano la Yehova ku Ziyoni, Mzinda wa Davide. Aisraeli onse anasonkhana pamaso pa Mfumu Solomoni nthawi ya chikondwerero cha mwezi wa Etanimu, mwezi wachisanu ndi chiwiri.

Akuluakulu onse a Israeli atafika, ansembe ananyamula Bokosi la Chipangano, ndipo anabwera nalo Bokosi la Yehova pamodzi ndi tenti ya msonkhano ndi ziwiya zonse zopatulika zimene zinali mʼmenemo. Ansembe ndi Alevi ndiye anazinyamula, ndipo Mfumu Solomoni ndi gulu lonse la Aisraeli amene anasonkhana naye anali patsogolo pa Bokosi la Chipangano, akupereka nsembe nkhosa zambiri ndi ngʼombe zambiri zosawerengeka.

Ansembe anafika nalo Bokosi la Chipangano la Yehova mʼchipinda chamʼkati mwenimweni, Malo Opatulika Kwambiri, ndipo analiyika pansi pa mapiko a akerubi. Akerubiwo anatambalitsa mapiko awo pamwamba pa Bokosi la Chipangano ndipo anaphimba bokosilo pamodzi ndi mitengo yonyamulira. Mitengoyi inali yayitali kwambiri ndipo inkaonekera kunja kwa chipinda chamʼkati cha Malo Opatulika koma osati kunja kwa Malo Opatulikawo; ndipo mitengoyi ilipo mpaka lero lino. Mʼbokosimo munalibe kanthu kena kalikonse kupatula miyala iwiri imene Mose anayikamo ku Horebu, kumene Yehova anachita pangano ndi Aisraeli atatuluka mʼdziko la Igupto.

10 Ansembe atatuluka mʼMalo Opatulikawo, mtambo unadzaza Nyumba ya Yehova. 11 Ndipo ansembewo sanathe kugwira ntchito yawo chifukwa cha mtambowo, pakuti ulemerero wa Yehova unadzaza mʼNyumba ya Yehova.

12 Pamenepo Solomoni anati, “Yehova anati adzakhala mʼmitambo yakuda; 13 taonani ndithu, ine ndakumangirani Nyumba yokongola kwambiri, malo woti muzikhalamo mpaka muyaya.”

14 Aisraeli onse ali chiyimire pomwepo, mfumu inatembenuka ndi kuwadalitsa. 15 Ndipo inati:

“Atamandike Yehova, Mulungu wa Israeli, amene wachita ndi dzanja lake zimene analonjeza ndi pakamwa pake kwa Davide abambo anga. Pakuti Iye anati, 16 ‘Kuyambira tsiku limene ndinatulutsa anthu anga Aisraeli ku Igupto, sindinasankhe mzinda wina uliwonse pa fuko lina lililonse la Aisraeli kuti kumeneko andimangire Nyumba, koma ndasankha Davide kuti alamulire anthu anga Aisraeli.’

17 “Abambo anga Davide anali ndi maganizo mu mtima mwawo oti amangire nyumba Yehova, Mulungu wa Israeli. 18 Koma Yehova ananena kwa abambo anga, Davide, kuti, ‘Popeza zinali mu mtima mwako kumangira nyumba Dzina langa, unachita bwino kukhala ndi maganizo amenewa mu mtima mwakomo. 19 Komatu, si iwe amene udzamanga Nyumba ya Mulungu, koma mwana wako, mwana amene iwe udzabereke. Iyeyo ndiye adzandimangire Nyumba.’

20 “Yehova wasunga zimene analonjeza: ine ndalowa mʼmalo mwa abambo anga Davide ndipo tsopano ndili pa mpando waufumu wa Israeli, monga momwe Yehova analonjezera, ndipo ndamangira nyumba Dzina la Yehova, Mulungu wa Israeli. 21 Ndalikonzera malo Bokosi la Chipangano mmene muli pangano la Yehova limene anapangana ndi makolo athu pamene anawatulutsa mʼdziko la Igupto.”

Marko 8:14-21

Yisiti wa Afarisi ndi Herode

14 Ophunzira anayiwala kutenga buledi, kupatula buledi mmodzi yekha amene anali naye mʼbwato. 15 Yesu anawachenjeza kuti, “Samalani ndipo onetsetsani yisiti wa Afarisi ndi wa Herode.”

16 Iwo anakambirana wina ndi mnzake ndipo anati, “Ndi chifukwa choti tilibe buledi.”

17 Yesu atadziwa zokambirana zawo anawafunsa kuti, “Nʼchifukwa chiyani mukukambirana kuti mulibe buledi? Kodi inu simukuonabe kapena kuzindikira? Kodi mitima yanu ndi yowumitsidwa? 18 Kodi muli ndi maso ndipo simukuona, ndi makutu ndipo mukulephera kumva? Kodi simukukumbukira? 19 Pamene ndinagawa malofu asanu a buledi kwa anthu 5,000, ndi madengu angati amene munatoleramo buledi ndi nsomba zotsalira?”

Iwo anayankha kuti, “Khumi ndi awiri.”

20 “Ndipo pamene ndinagawa malofu asanu ndi awiri a buledi, kwa anthu 4,000, ndi madengu angati amene munatoleramo buledi ndi nsomba zotsalira?”

Iwo anayankha kuti, “Asanu ndi awiri.”

21 Iye anawafunsa kuti, “Kodi simumvetsetsabe?”

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero (CCL)

The Word of God in Contemporary Chichewa Copyright © 2002, 2016 by Biblica, Inc.® Used by permission of Biblica, Inc.® All rights reserved worldwide. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Mwini © 2002, 2016 ndi Biblica, Inc.® Kugwiritsa ntchito mwachilolezo. Umwini ndi otetezedwa pa dziko lonse.