Revised Common Lectionary (Semicontinuous)
Kwa mtsogoleri wamayimbidwe. Monga mwa mayimbidwe a “Maluwa a Kakombo.” Salimo la ana a Kora. Nyimbo ya pa ukwati.
45 Mtima wanga watakasika ndi nkhani yokoma
pamene ndikulakatula mawu anga kwa mfumu;
lilime langa ndi cholembera cha wolemba waluso.
2 Inu ndinu abwino kwambiri kuposa anthu onse
ndipo milomo yanu inadzozedwa ndi chikondi cha Mulungu chosasinthika,
popeza Mulungu wakudalitsani kwamuyaya.
6 Mpando wanu waufumu, Inu Mulungu, udzakhala ku nthawi za nthawi;
ndodo yaufumu yachilungamo idzakhala ndodo yaufumu ya ufumu wanu.
7 Inu mumakonda chilungamo ndi kudana ndi zoyipa;
choncho Mulungu, Mulungu wanu, wakukhazikani pamwamba pa anzanu
pokudzozani ndi mafuta a chimwemwe.
8 Mikanjo yanu yonse ndi yonunkhira ndi mure ndi aloe ndi kasiya;
kuchokera ku nyumba zaufumu zokongoletsedwa ndi mnyanga wanjovu
nyimbo za zoyimbira zazingwe zimakusangalatsani.
9 Ana aakazi a mafumu ali pakati pa akazi anu olemekezeka;
ku dzanja lanu lamanja kuli mkwatibwi waufumu ali mu golide wa ku Ofiri.
1 Nyimbo ya Solomoni, nyimbo yoposa nyimbo zonse.
Mkazi
2 Undipsompsone ndi milomo yako
chifukwa chikondi chako nʼchokoma kuposa vinyo.
3 Mafuta ako odzola ndi onunkhira bwino;
dzina lako lili ngati mafuta onunkhira otsanulidwa.
Nʼchifukwa chake atsikana amakukonda!
4 Nditenge ndipo ndizikutsata, tiye tifulumire!
Mfumu indilowetse mʼchipinda chake.
Abwenzi
Ife timasangalala ndi kukondwera nawe,
tidzatamanda chikondi chako kupambana vinyo.
Mkazi
Amachita bwinotu potamanda iwe!
5 Ndine wakuda, komatu ndine wokongola,
inu akazi a ku Yerusalemu,
ine ndine wakuda ngati tenti ya ku Kedara,
ngati makatani a tenti ya Solomoni.
6 Musandiyangʼane monyoza chifukwa ndine wakuda,
ndine wakuda chifukwa cha dzuwa.
Alongo anga anandikwiyira
ndipo anandigwiritsa ntchito mʼminda ya mpesa;
munda wangawanga sindinawusamalire.
7 Ndiwuze iwe, amene ndimakukonda, kumene umadyetsa ziweto zako
ndi kumene umagoneka nkhosa zako nthawi yamasana.
Ndikhalirenji ngati mkazi wachiwerewere
pambali pa ziweto za abwenzi ako?
Abwenzi
8 Ngati sukudziwa iwe wokongola kwambiri kuposa akazi ena,
ngati sukudziwa, tsatira makwalala a nkhosa
ndipo udyetse ana ambuzi
pambali pa matenti a abusa.
Mwamuna
9 Iwe bwenzi langa,
uli ngati kavalo wamkazi ku magaleta a Farao.
10 Masaya ako ndi okongola ndi ndolo zamʼmakutuzo,
khosi lako likukongola ndi mikanda yamiyala yamtengowapatali.
11 Tidzakupangira ndolo zagolide
zokongoletsedwa ndi mikanda yasiliva.
Mkazi
12 Pamene mfumu inali pa malo ake odyera,
mafuta anga onunkhira anamveka fungo lake.
13 Wokondedwa wanga ali ngati kathumba ka mure kwa ine,
kamene kamakhala pakati pa mawere angawa.
14 Wokondedwa wanga ali ngati mpukutu wa maluwa ofiira,
ochokera ku minda ya mpesa ya ku Eni-Gedi.
Mwamuna
15 Iwe wokondedwa wanga, ndiwe wokongoladi!
Ndithu, ndiwe chiphadzuwa,
maso ako ali ngati nkhunda.
Mkazi
16 Iwe bwenzi langa, ndiwe wokongoladi!
Ndithu, ndiwe wokongoladi kwambiri!
Ndipo malo athu ogonapo ndi msipu wobiriwira.
Mwamuna
17 Mitanda ya nyumba yathu ndi ya mkungudza,
phaso lake ndi la mtengo wa payini.
1 Yakobo, mtumiki wa Mulungu ndi wa Ambuye Yesu Khristu,
kulembera mafuko khumi ndi awiri obalalikana ku mayiko osiyanasiyana.
Landirani moni.
Masautso ndi Mayesero
2 Abale, muchiyese ngati chimwemwe chenicheni nthawi zonse pamene mukukumana ndi mayesero amitundumitundu. 3 Inu mukudziwa kuti kuyesedwa kwa chikhulupiriro chanu kumabweretsa chipiriro. 4 Chipiriro chiyenera kugwira ntchito yake kuti mukhale okhwima ndi angwiro, osasowa kanthu kalikonse. 5 Ngati wina pakati panu akusowa nzeru, apemphe kwa Mulungu amene amapereka kwa onse mwaulere ndi mosatonzera, ndipo adzapatsidwa. 6 Koma pamene mupempha, muyenera kukhulupirira osakayika, chifukwa amene amakayika ali ngati mafunde pa nyanja amene amawinduka nakankhika ndi mphepo. 7 Munthu wotere asayembekezere kulandira kalikonse kuchokera kwa Ambuye. 8 Iyeyu ndi munthu wa mitima iwiri, wosakhazikika pa zimene akuchita.
The Word of God in Contemporary Chichewa Copyright © 2002, 2016 by Biblica, Inc.® Used by permission of Biblica, Inc.® All rights reserved worldwide. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Mwini © 2002, 2016 ndi Biblica, Inc.® Kugwiritsa ntchito mwachilolezo. Umwini ndi otetezedwa pa dziko lonse.