Revised Common Lectionary (Semicontinuous)
Kwa mtsogoleri wa mayimbidwe. Potsata mayimbidwe a “Kakombo wa Pangano.” Salimo la Asafu.
80 Tcherani khutu Inu mʼbusa wa Israeli,
Inu amene mumatsogolera Yosefe monga nkhosa;
Inu amene mumakhala pa mpando waufumu pakati pa akerubi, walani
2 kwa Efereimu, Benjamini ndi Manase.
Utsani mphamvu yanu;
bwerani ndi kutipulumutsa.
3 Tibwezereni mwakale Inu Mulungu;
nkhope yanu itiwalire
kuti tipulumutsidwe.
4 Inu Mulungu Wamphamvuzonse,
mpaka liti mkwiyo wanu udzanyeka
kutsutsana ndi mapemphero a anthu anu?
5 Mwawadyetsa buledi wa misozi;
mwachitisa iwo kumwa misozi yodzaza mbale.
6 Mwachititsa kuti tikhale gwero la mikangano pakati pa anansi athu,
ndipo adani athu akutinyoza.
7 Tibwezereni mwakale Inu Mulungu Wamphamvuzonse,
nkhope yanu itiwalire
kuti tipulumutsidwe.
8 Munatulutsa mpesa kuchoka ku Igupto;
munathamangitsa anthu a mitundu ina ndi kuwudzala mpesawo.
9 Munawulimira munda wamphesawo,
ndipo unamera ndi kudzaza dziko.
10 Mapiri anaphimbidwa ndi mthunzi wake,
mikungudza yamphamvu ndi nthambi zake.
11 Unatambalitsa nthambi zake mpaka ku nyanja,
mphukira zake mpaka ku mtsinje.
12 Chifukwa chiyani mwagwetsa makoma ake
kuti onse amene akudutsa athyole mphesa zake?
13 Nguluwe zochokera mʼnkhalango zikuwononga
ndipo zirombo za mthengo zimawudya.
14 Bweraninso kwa ife Inu Mulungu Wamphamvuzonse!
Yangʼanani pansi muli kumwambako ndipo muone!
Uyangʼanireni mpesa umenewu,
15 muzu umene dzanja lanu lamanja ladzala,
mwana amene inu munamukuza nokha.
16 Mpesa wanu wadulidwa ndi kutenthedwa ndi moto;
pakudzudzula kwanu anthu anu awonongeka.
17 Dzanja lanu likhale pa munthu amene ali ku dzanja lanu lamanja,
mwana wa munthu amene mwalera nokha.
18 Ndipo ife sitidzatembenukira kumbali kuchoka kwa Inu;
titsitsimutseni ndipo tidzayitana pa dzina lanu.
19 Tibwezereni mwakale Inu Yehova Mulungu Wamphamvuzonse
nkhope yanu itiwalire
kuti tipulumutsidwe.
Nyimbo ya Munda Wamphesa
5 Ndidzamuyimbira bwenzi langa
nyimbo yokamba za munda wake wa mpesa:
Wokondedwa wanga anali ndi munda wamphesa
pa phiri la nthaka yachonde.
2 Anatipula nachotsa miyala yonse
ndipo anawokamo mipesa yabwino kwambiri.
Anamanga nsanja yolondera pakati pa mundawo
ndipo anasemanso mopsinyira mphesa mʼmundamo.
Ndipo iye anayembekezera kuti mundawo udzabala mphesa zabwino,
koma ayi, unabala mphesa zosadya.
3 “Tsopano, inu amene mumakhala mu Yerusalemu ndi inu anthu a ku Yuda,
weruzani pakati pa ine ndi munda wanga wa mpesawu.
4 Kodi nʼchiyaninso china chimene ndikanachitira munda wanga wa mpesa
kupambana chomwe ndawuchitira kale?
Pamene ndinkayembekezera kuti udzabala mphesa zabwino,
bwanji unabala mphesa zosadya?
5 Tsopano ndikuwuzani
chimene ndidzawuchitire munda wanga wa mpesa:
ndidzachotsa mpanda wake,
ndipo mundawo udzawonongeka;
ndidzagwetsa khoma lake,
ndipo nyama zidzapondapondamo.
6 Ndidzawusandutsa tsala,
udzakhala wosatengulira ndi wosalimira
ndipo mudzamera mkandankhuku ndi minga ina.
Ndidzalamula mitambo
kuti isagwetse mvula pa mundapo.”
7 Munda wamphesa wa Yehova Wamphamvuzonse
ndi Aisraeli,
ndipo anthu a ku Yuda ndiwo
minda yake yomukondweretsa.
Ndipo Iye ankayembekezera chiweruzo cholungama, mʼmalo mwake anaona kuphana;
mʼmalo mwa chilungamo Iye anamva kulira kwa anthu ozunzika.
16 Choncho ine ndikuti, mulole kuti Mzimu akutsogolereni ndipo simudzachita zofuna za thupi lanu la uchimo. 17 Pakuti thupi lanu la uchimo limalakalaka zimene ndi zotsutsana ndi Mzimu, ndi Mzimu zimene ndi zotsutsana ndi thupi lanu la uchimo. Ziwirizi zimadana, kotero kuti simungachite zimene mukufuna. 18 Koma ngati Mzimu akutsogolerani, ndiye kuti simuli pansi pa lamulo.
19 Ntchito za thupi lanu la uchimo zimaonekera poyera ndi izi: dama, zodetsa ndi kuchita zonyansa; 20 kupembedza mafano ndi ufiti; kudana, kukangana, kupsa mtima, kudzikonda, kugawikana, mipatuko 21 ndi nsanje, kuledzera, mchezo ndi zina zotere. Ine ndikukuchenjezani monga ndinachita poyamba paja kuti amene amachita zimenezi sadzalandira ufumu wa Mulungu.
22 Koma chipatso cha Mzimu Woyera ndi chikondi, chimwemwe, mtendere, kuleza mtima, chifundo, kukoma mtima, kukhulupirika, 23 kufatsa ndi kudziretsa. Palibe lamulo loletsa zimenezi. 24 Amene ali ake a Khristu Yesu anapachika pa mtanda thupi lawo la uchimo pamodzi ndi zokhumba zawo ndi zolakalaka zawo. 25 Popeza timakhala ndi moyo mwa Mzimu Woyera, tiyeni tiyende pamodzi ndi Mzimu Woyera. 26 Tisakhale odzitukumula, oputana ndi ochitirana nsanje.
The Word of God in Contemporary Chichewa Copyright © 2002, 2016 by Biblica, Inc.® Used by permission of Biblica, Inc.® All rights reserved worldwide. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Mwini © 2002, 2016 ndi Biblica, Inc.® Kugwiritsa ntchito mwachilolezo. Umwini ndi otetezedwa pa dziko lonse.