Revised Common Lectionary (Semicontinuous)
150 Tamandani Yehova.
Tamandani Mulungu mʼmalo ake opatulika;
mutamandeni ku thambo lake lamphamvu.
2 Mutamandeni chifukwa cha machitidwe ake amphamvu;
mutamandeni chifukwa cha ukulu wake wopambana.
3 Mutamandeni poyimba malipenga,
mutamandeni ndi pangwe ndi zeze.
4 Mutamandeni ndi matambolini ndi kuvina,
mutamandeni ndi zingwe ndi zitoliro.
5 Mutamandeni ndi ziwaya zolira za malipenga,
mutamandeni ndi ziwaya zolira kwambiri.
6 Chamoyo chilichonse chopuma chitamande Yehova.
Tamandani Yehova.
Kubwezeretsedwa kwa Israeli
30 Yehova anawuza Yeremiya kuti, 2 “Ine Yehova, Mulungu wa Israeli ndikuti, ‘Lemba mʼbuku mawu onse amene ndakuwuza. 3 Nthawi ikubwera pamene ndidzachotse anthu anga, Israeli ndi Yuda kuchokera ku ukapolo ndi kuwabwezera dziko limene ndinapatsa makolo awo,’ akutero Yehova.”
4 Nawa mawu amene Yehova anayankhula ndi anthu a ku Israeli ndi Yuda: 5 “Yehova akuti:
“Ndamva kulira chifukwa cha nkhawa,
ndamva kulira kwa mantha popeza palibe mtendere.
6 Tsono khalani pansi ndi kudzifunsa kuti:
Kodi munthu wamwamuna angathe kubereka mwana?
Nanga nʼchifukwa chiyani ndikuona munthu aliyense wamwamuna
atagwira manja ake pa mimba pake ngati mayi pa nthawi yake yochira?
Chifukwa chiyani nkhope iliyonse ili yakugwa?
7 Mayo ine! Tsiku limeneli ndi lalikulu kwambiri!
Sipadzakhala lina lofanana nalo.
Idzakhala nthawi ya masautso kwa Yakobo,
koma adzapulumuka ku masautsowo.”
8 Yehova Wamphamvuzonse akuti, “Pa tsiku limenelo,
ndidzathyola goli la ukapolo mʼkhosi mwawo
ndipo ndidzadula zingwe zowamanga;
Aisraeli sadzakhalanso akapolo a alendo.
9 Mʼmalo mwake, adzatumikira Yehova Mulungu wawo
ndiponso Davide mfumu yawo,
amene ndidzawasankhira.
10 “ ‘Tsono usachite mantha, iwe mtumiki wanga Yakobo;
usade nkhawa, iwe Israeli,’
akutero Yehova.
‘Ndithu ndidzakupulumutsa kuchokera ku dziko lakutali,
zidzukulu zako kuchokera ku dziko la ukapolo wawo.
Yakobo adzabwerera ndipo adzakhala modekha pa mtendere,
ndipo palibe amene adzamuchititsa mantha.
11 Ine ndili nanu ndipo ndidzakupulumutsani,’
akutero Yehova.
‘Ngakhale ndidzawononga kotheratu mitundu yonse ya anthu
kumene ndinakubalalitsirani,
koma inu sindidzakuwonongani kotheratu.
Sindidzakulekani kuti mukhale osalangidwa.
Koma ndidzakulangani mwachilungamo.’ ”
10 Mmenemu ndi mmene timadziwira ana a Mulungu ndi amene ali ana a mdierekezi. Aliyense amene sachita chilungamo si mwana wa Mulungu; ngakhalenso amene sakonda mʼbale wake.
Kukondana Wina ndi Mnzake
11 Uthenga umene munawumva kuyambira pachiyambi ndi uwu: Tizikondana wina ndi mnzake. 12 Musakhale ngati Kaini, amene anali wa woyipayo ndipo anapha mʼbale wake. Nanga anamupha chifukwa chiyani? Chifukwa zochita zake zinali zoyipa ndipo zochita za mʼbale wake zinali zolungama. 13 Abale anga, musadabwe ngati dziko lapansi lidana nanu. 14 Ife tikudziwa kuti tinatuluka mu imfa ndi kulowa mʼmoyo, chifukwa timakonda abale athu. Aliyense amene sakonda mʼbale wake akanali mu imfa. 15 Aliyense amene amadana ndi mʼbale wake ndi wakupha, ndipo inu mukudziwa kuti wopha anthu mwa iye mulibe moyo wosatha.
16 Mmene timadziwira chikondi chenicheni ndi umu: Yesu anapereka moyo wake chifukwa cha ife. Ndipo nafenso tiyenera kupereka miyoyo yathu chifukwa cha abale athu.
The Word of God in Contemporary Chichewa Copyright © 2002, 2016 by Biblica, Inc.® Used by permission of Biblica, Inc.® All rights reserved worldwide. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Mwini © 2002, 2016 ndi Biblica, Inc.® Kugwiritsa ntchito mwachilolezo. Umwini ndi otetezedwa pa dziko lonse.