Revised Common Lectionary (Semicontinuous)
Kwa mtsogoleri wa mayimbidwe wa zida za zingwe. Salimo la Davide.
4 Ndiyankheni pamene ndiyitana Inu,
Inu Mulungu wa chilungamo changa.
Pumulitseni ku zowawa zanga;
chitireni chifundo ndi kumva pemphero langa.
2 Anthu inu, mpaka liti mudzakhala mukusandutsa ulemerero wanga kukhala manyazi?
Mpaka liti mudzakonda zachabe ndi kufuna milungu yabodza?
Sela.
3 Dziwani kuti Yehova wadziyikira padera anthu okhulupirika;
Yehova adzamva pamene ndidzamuyitana.
4 Kwiyani koma musachimwe;
pamene muli pa mabedi anu,
santhulani mitima yanu ndi kukhala chete.
Sela
5 Perekani nsembe zolungama
ndipo dalirani Yehova.
6 Ambiri akufunsa kuti, “Ndani angationetse chabwino chilichonse?”
Kuwunika kwa nkhope yanu kutiwalire, Inu Yehova.
7 Inu mwadzaza mtima wanga ndi chimwemwe chachikulu
kuposa kuchuluka kwa tirigu wawo ndi vinyo watsopano.
8 Ine ndidzagona ndi kupeza tulo mwamtendere,
pakuti Inu nokha, Inu Yehova,
mumandisamalira bwino.
Petro Achiritsa Wolumala Miyendo
3 Tsiku lina Petro ndi Yohane ankapita ku Nyumba ya Mulungu kukapemphera nthawi ya 3 koloko masana. 2 Ndipo munthu wolumala chibadwire ankanyamulidwa tsiku ndi tsiku kukayikidwa pa khomo la Nyumbayo lotchedwa Khomo Lokongola kuti azikapempha amene amalowa ku bwalo la Nyumbayo. 3 Ataona Petro ndi Yohane ali pafupi kulowa anawapempha ndalama. 4 Iwo anamuyangʼanitsitsa iye. Kenaka Petro anati, “Tiyangʼane!” 5 Munthuyo anawayangʼanitsitsa kuyembekezera kuti alandira kanthu kuchokera kwa iwo.
6 Petro anati kwa iye, “Ine ndilibe siliva kapena golide, koma chimene ndili nacho ndikupatsa. Mʼdzina la Yesu Khristu wa ku Nazareti, yenda.” 7 Ndipo anamugwira dzanja lamanja, namuthandiza kuti ayimirire ndipo nthawi yomweyo mapazi ake ndi akakolo ake analimba. 8 Iye analumpha ndi kuyamba kuyenda. Kenaka analowa nawo pamodzi mʼbwalo la Nyumba ya Mulungu, akuyenda ndi kulumpha ndiponso kuyamika Mulungu. 9 Anthu onse atamuona akuyenda ndiponso kuyamika Mulungu, 10 anamuzindikira kuti ndi yemwe uja ankakhala pa khomo la Nyumbayo lotchedwa Khomo Lokongola, ndipo anazizwa ndi kudabwa ndi zimene zinamuchitikira.
Mkangano Pakati pa Ophunzira
24 Komanso mkangano unabuka pakati pawo kuti ndani mwa iwo amene amaganiziridwa kukhala wamkulu. 25 Yesu anawawuza kuti, “Mafumu a anthu a mitundu ina amaonetsa mphamvu za ufumu wawo pa anthuwo; ndipo amene ali ndi ulamuliro, amapatsidwa dzina la kuti ‘Opindula.’ 26 Koma inu simuyenera kukhala choncho. Mʼmalo mwake, wamkulu pakati panu akhale ngati wamngʼono pa onse, ndipo iye amene alamulira akhale ngati wotumikira. 27 Pakuti wamkulu ndani, iye amene ali pa tebulo kapena iye amene akutumikira? Kodi si iye amene ali pa tebulo? Koma ndili pakati panu ngati mmodzi wokutumikirani. 28 Inu ndinu amene mwayima nane mʼmayesero. 29 Ndipo Ine ndikupatsani inu ufumu, monga momwe Atate anga anandipatsiranso Ine, 30 kuti inu muthe kudya ndi kumwa pa tebulo langa mu ufumu wanga ndi kukhala pa mipando yaufumu kuweruza mafuko khumi ndi awiri a Israeli.”
The Word of God in Contemporary Chichewa Copyright © 2002, 2016 by Biblica, Inc.® Used by permission of Biblica, Inc.® All rights reserved worldwide. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Mwini © 2002, 2016 ndi Biblica, Inc.® Kugwiritsa ntchito mwachilolezo. Umwini ndi otetezedwa pa dziko lonse.