Revised Common Lectionary (Semicontinuous)
135 Tamandani Yehova.
Tamandani dzina la Yehova;
mutamandeni, inu atumiki a Yehova,
2 amene mumatumikira mʼnyumba ya Yehova,
mʼmabwalo a nyumba ya Mulungu wathu.
3 Tamandani Yehova, pakuti Yehova ndi wabwino;
imbani nyimbo zotamanda dzina lake, pakuti nʼkokoma kutero,
4 Pakuti Yehova wasankha Yakobo kuti akhale wake,
Israeli kuti akhale chuma chake chapamtima.
5 Ndikudziwa kuti Yehova ndi wamkulu,
kuti Ambuye athu ndi wamkulu kuposa milungu yonse.
6 Yehova amachita chilichonse chimene chimamukomera,
kumwamba ndi dziko lapansi,
ku nyanja zazikulu ndi ku malo ake onse akuya.
7 Iye amatulutsa mitambo kuchokera ku malekezero a dziko lapansi,
amatumiza zingʼaningʼani pamodzi ndi mvula
ndipo amatulutsa mphepo ku malo ake osungiramo.
8 Anakantha ana oyamba kubadwa a Igupto,
ana oyamba kubadwa a anthu ndi nyama.
9 Iye anatumiza zizindikiro zozizwitsa ndi zodabwitsa pakati pako, iwe Igupto,
kutsutsana ndi Farao pamodzi ndi atumiki ake onse.
10 Iye anakantha mitundu yambiri ya anthu
ndi kupha mafumu amphamvu:
11 Sihoni mfumu ya Aamori,
Ogi mfumu ya Basani,
ndi maufumu onse a ku Kanaani;
12 ndipo anapereka dziko lawo ngati cholowa,
cholowa cha anthu ake Aisraeli.
13 Dzina lanu, Inu Yehova, ndi losatha mpaka muyaya,
mbiri yanu, Inu Yehova, idziwika mibado yonse.
14 Pakuti Yehova adzaonetsa kuti anthu ake ngosalakwa,
ndipo adzachitira chifundo atumiki ake.
15 Mafano a mitundu ya anthu ndi siliva ndi golide,
opangidwa ndi manja a anthu.
16 Pakamwa ali napo koma sayankhula
maso ali nawo, koma sapenya;
17 makutu ali nawo, koma sakumva
ndipo mʼkamwa mwawo mulibe mpweya uliwonse.
18 Iwo amene amapanga mafanowo adzakhala ngati mafanowo,
chimodzimodzinso iwo amene amadalira mafanowo.
19 Inu nyumba ya Israeli, tamandani Yehova;
inu nyumba ya Aaroni, tamandani Yehova;
20 Inu nyumba ya Levi, tamandani Yehova;
Inu amene mumaopa Iye, tamandani Yehova.
21 Wodalitsika ndi Yehova kuchokera mʼZiyoni,
amene amakhala mu Yerusalemu.
Tamandani Yehova.
Fano la Golide ndi Ngʼanjo ya Moto
3 Mfumu Nebukadinezara anapangitsa fano la golide lotalika mamita 27 ndi mulifupi mwake mamita atatu, ndipo analiyimika mʼchigwa cha Dura mʼchigawo cha Babuloni. 2 Kenaka iye anayitanitsa akalonga, abwanamkubwa, nduna, aphungu, asungichuma, oweruza milandu, anyakwawa ndi akulu ena onse a madera a dzikolo, kuti abwere ku mwambo wotsekula fano limene analiyimika lija. 3 Choncho akalonga, abwanamkubwa, nduna, aphungu, asungichuma, oweruza milandu, anyakwawa, ndi akulu ena onse a madera a dzikolo, anasonkhana kudzachita mwambo wotsekulira fano limene mfumu Nebukadinezara analiyimika, ndipo mlaliki anayimirira pamaso pa fanolo nati:
4 “Inu anthu a mitundu yonse ndi a ziyankhulo zonse, mukulamulidwa kuti muchite izi: mitundu ya anthu ndi a chiyankhulo chilichonse 5 mukadzamva kulira kwa lipenga, chitoliro, zeze, sansi, chisakasa, mngoli ndi nyimbo za mtundu uliwonse, muyenera kulambira ndi kupembedza fano la golide limene mfumu Nebukadinezara analiyimika. 6 Aliyense amene sadzalambira ndi kupembedza adzaponyedwa nthawi yomweyo mʼngʼanjo ya moto.”
7 Choncho anthu onse aja atangomva kulira kwa lipenga, chitoliro, zeze, sansi, chisakasa, mngoli ndi nyimbo za mtundu uliwonse, analambira ndi kupembedza fano la golide limene mfumu Nebukadinezara analiyimika.
8 Pa nthawi imeneyi alawuli ena anafika ndi kuwanenera zoyipa Ayuda. 9 Iwo anati kwa mfumu Nebukadinezara, “Inu mfumu mukhale ndi moyo wautali! 10 Inu mfumu, mwakhazikitsa lamulo kuti aliyense akamva kulira kwa lipenga, chitoliro, zeze, sansi, chisakasa, mngoli ndi nyimbo za mtundu uliwonse, ayenera kulambira ndi kupembedza fano la golide, 11 ndi kuti aliyense osalambira ndi kupembedza adzaponyedwa mʼngʼanjo ya moto. 12 Koma alipo Ayuda ena Sadirake, Mesaki ndi Abedinego amene munawayika kuti ayangʼanire ntchito ya dera la ku Babuloni. Anthu amenewa sakumvera inu mfumu. Iwo sakutumikira milungu yanu kapena kulambira fano la golide limene munaliyimikalo.”
13 Tsono Nebukadinezara anakwiya ndi kupsa mtima kwambiri, ndipo anayitanitsa Sadirake, Mesaki ndi Abedenego. Choncho amuna awa anabwera pamaso pa mfumu, 14 ndipo Nebukadinezara anawafunsa kuti, “Kodi ndi zoona, Sadirake, Mesaki ndi Abedenego, kuti simukutumikira milungu yanga kapena kupembedza fano la golide ndinaliyikalo? 15 Tsopano ngati muli okonzeka kulambira ndi kupembedza fano ndinalipanga, mukangomva kulira kwa lipenga chitoliro, zeze, sansi, chisakasa, mngoli ndi nyimbo za mtundu uliwonse, muchita bwino. Koma ngati simulipembedza, mudzaponyedwa mʼnganjo ya moto. Nanga ndi mulungu uti amene adzatha kukupulumutsani mʼmanja anga?”
16 Sadirake, Mesaki ndi Abedenego anayankha mfumu Nebukadinezara kuti, “Sikoyenera kuti tikuyankheni pa nkhani imeneyi. 17 Ngati tiponyedwa mʼngʼanjo ya moto, Mulungu amene timamutumikira akhoza kutipulumutsa ku ngʼanjo yamotoyo, ndipo adzatilanditsa mʼdzanja lanu mfumu. 18 Koma ngakhale Mulungu wathu atapanda kutipulumutsa, tikufuna mudziwe inu mfumu, kuti sitidzatumikira milungu yanu kapena kupembedza fano la golide limene munaliyimika.”
19 Pamenepo Nebukadinezara anapsa mtima ndi Sadirake, Mesaki ndi Abedenego, ndipo anayipidwa nawo. Iye analamulira kuti ngʼanjo ayitenthetse kasanu ndi kawiri kuposa nthawi zonse, 20 ndipo analamula ena mwa asilikali amphamvu kwambiri mʼgulu lake lankhondo kuti amange Sadirake, Mesaki ndi Abedenego ndi kuwaponya mʼngʼanjo ya moto. 21 Choncho amuna awa, atavala mikanjo yawo, mabuluku, nduwira ndi zovala zina zonse, anamangidwa ndi kuponyedwa mʼngʼanjo ya moto. 22 Tsono popeza lamulo la mfumu linali lofulumiza, ngʼanjo inatenthetsedwa kowirikiza mwakuti malawi ake anapha asilikali amene ananyamula Sadirake, Mesaki ndi Abedenego, 23 ndipo anyamata atatuwa, ali chimangidwire, anagwera mʼngʼanjo ya moto.
24 Kenaka mfumu Nebukadinezara anadabwa ndipo anafunsa nduna zake kuti, “Kodi sanali amuna atatu amene anamangidwa ndi kuponyedwa mʼmoto?”
Iwo anayankha kuti, “Ndi zoonadi, mfumu.”
25 Iye anati, “Taonani! Ndikuona amuna anayi akuyendayenda mʼmoto, osamangidwa ndi osapwetekedwa ndipo wachinayi akuoneka ngati mwana wa milungu.”
26 Pamenepo Nebukadinezara anayandikira pa khomo langʼanjo ya moto ndi kufuwula kuti, “Sadirake, Mesaki ndi Abedenego, atumiki a Mulungu Wammwambamwamba, tulukani! Bwerani kuno!”
Ndipo Sadirake, Mesaki ndi Abedenego anatuluka mʼmoto, 27 ndipo akalonga, akazembe, abwanamkubwa ndi nduna zamfumu anasonkhana mowazungulira. Anaona kuti moto sunatenthe matupi awo ngakhale tsitsi kumutu kwawo silinapse; zovala zawo sizinapse, ndipo sankamveka fungo la moto.
28 Kenaka Nebukadinezara anati, “Atamandike Mulungu wa Sadirake, Mesaki ndi Abedenego, amene anatumiza mngelo wake ndi kupulumutsa atumiki ake! Iwo anakhulupirira Iye ndi kunyozera lamulo la mfumu ndipo anali okonzeka kutaya moyo wawo koposa kutumikira kapena kupembedza mulungu wina aliyense wosakhala Mulungu wawo. 29 Tsono ndikulamula kuti anthu a mitundu ina kaya chiyankhulo china chili chonse amene anganyoze Mulungu wa Sadirake, Mesaki ndi Abedenego adulidwe nthulinthuli ndipo nyumba zawo ndidzagwetsa ndi kusandutsa bwinja, popeza palibe Mulungu amene akhoza kupulumutsa mʼnjira yotere.”
30 Ndipo mfumu Nebukadinezara anakweza pa ntchito Sadirake, Mesaki ndi Abedenego mʼchigawo cha Babuloni.
Chikondi ndi Chidani
3 Ife timatsimikiza kuti tikumudziwa ngati tikusunga malamulo ake. 4 Munthu akamanena kuti, “Ine ndimadziwa Mulungu,” koma samvera malamulo a Mulunguyo, ndi wabodza ameneyo ndipo mwa iye mulibe choonadi. 5 Koma munthu aliyense akamvera mawu ake, ndiye kuti chikondi cha Mulungu chafikadi penipeni mwa iyeyo. Pamenepo timatsimikizadi kuti tili mwa Iye. 6 Aliyense amene amati amakhala mwa Mulungu, ayenera kukhala moyo umene Yesu ankakhala.
7 Okondedwa, sindikukulemberani lamulo latsopano koma lakale lomwe lija, limene munali nalo kuyambira pachiyambi. Lamulo la kalelo ndi mawu amene munawamva kale. 8 Komabe ndi lamulo latsopano limene ndikukulemberani. Choonadi chake chikuoneka mwa Yesu ndiponso mwa inu, chifukwa mdima ukutha ndipo kuwunika kwenikweni kwayamba kale kuwala.
9 Aliyense amene amati ali mʼkuwunika, koma nʼkumadana ndi mʼbale wake ali mu mdima. 10 Aliyense amene amakonda mʼbale wake amakhalanso mʼkuwunika, ndipo mwa iye mulibe chokhumudwitsa. 11 Koma aliyense wodana ndi mʼbale wake ali mu mdima ndipo akuyenda mu mdima. Iyeyo sakudziwa kumene akupita, chifukwa mdima wamudetsa mʼmaso mwake.
The Word of God in Contemporary Chichewa Copyright © 2002, 2016 by Biblica, Inc.® Used by permission of Biblica, Inc.® All rights reserved worldwide. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Mwini © 2002, 2016 ndi Biblica, Inc.® Kugwiritsa ntchito mwachilolezo. Umwini ndi otetezedwa pa dziko lonse.