Print Page Options
Previous Prev Day Next DayNext

Revised Common Lectionary (Semicontinuous)

Daily Bible readings that follow the church liturgical year, with sequential stories told across multiple weeks.
Duration: 1245 days
Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero (CCL)
Version
Machitidwe a Atumwi 3:12-19

12 Petro ataona zimenezi anawawuza kuti, “Inu Aisraeli, chifukwa chiyani mukudabwa ndi zimene zachitikazi? Bwanji mukuyangʼana ife ngati kuti tamuyendetsa munthuyu ndi mphamvu yathu kapena chifukwa cha kupembedza kwathu? 13 Mulungu wa Abrahamu, Isake ndi Yakobo, Mulungu wa makolo athu, wamulemekeza mtumiki wake Yesu. Amene inu munamukana pamaso pa Pilato ndi kumupereka Iye kuti aphedwe, ngakhale kuti Pilato anafuna kuti amumasule. 14 Koma inu munamukana Woyera ndi Wolungamayo ndipo munapempha kuti akumasulireni munthu wakupha anthu. 15 Inu munapha mwini moyo, koma Mulungu anamuukitsa kwa akufa. Ife ndife mboni za zimenezi. 16 Mwachikhulupiriro mʼdzina la Yesu, munthu uyu amene mukumuona ndi kumudziwa analimbikitsidwa. Mʼdzina la Yesu ndi chikhulupiriro chimene chili mwa iye chamuchiritsa kwathunthu, monga nonse mukuona.

17 “Tsopano abale ine ndikudziwa kuti inu munachita zimenezi mosadziwa, monga momwenso anachitira atsogoleri anu. 18 Koma umu ndi mmene Mulungu anakwaniritsira zimene zinanenedwa kale ndi aneneri onse, kuti Khristu adzamva zowawa. 19 Chifukwa chake, lapani, bwererani kwa Mulungu, kuti machimo anu afafanizidwe, kuti nthawi ya kutsitsimuka ibwere kuchokera kwa Ambuye,

Masalimo 4

Kwa mtsogoleri wa mayimbidwe wa zida za zingwe. Salimo la Davide.

Ndiyankheni pamene ndiyitana Inu,
    Inu Mulungu wa chilungamo changa.
Pumulitseni ku zowawa zanga;
    chitireni chifundo ndi kumva pemphero langa.

Anthu inu, mpaka liti mudzakhala mukusandutsa ulemerero wanga kukhala manyazi?
    Mpaka liti mudzakonda zachabe ndi kufuna milungu yabodza?
            Sela.
Dziwani kuti Yehova wadziyikira padera anthu okhulupirika;
    Yehova adzamva pamene ndidzamuyitana.

Kwiyani koma musachimwe;
    pamene muli pa mabedi anu,
    santhulani mitima yanu ndi kukhala chete.
            Sela
Perekani nsembe zolungama
    ndipo dalirani Yehova.

Ambiri akufunsa kuti, “Ndani angationetse chabwino chilichonse?”
    Kuwunika kwa nkhope yanu kutiwalire, Inu Yehova.
Inu mwadzaza mtima wanga ndi chimwemwe chachikulu
    kuposa kuchuluka kwa tirigu wawo ndi vinyo watsopano.
Ine ndidzagona ndi kupeza tulo mwamtendere,
    pakuti Inu nokha, Inu Yehova,
    mumandisamalira bwino.

1 Yohane 3:1-7

Taonani kukula kwake kwa chikondi chimene Atate anatikonda nacho, kuti titchedwe ana a Mulungu! Ndipo nʼchimene ife tili! Nʼchifukwa chake dziko lapansi silitidziwa chifukwa silinamudziwe Iye. Abale okondedwa, tsopano ndife ana a Mulungu, ndipo sichinaoneke chimene tidzakhala. Koma tikudziwa kuti Yesu akadzaonekera, tidzafanana naye, pakuti tidzamuona Iyeyo monga momwe alili. Aliyense amene ali ndi chiyembekezo ichi mwa Iye adziyeretse yekha, monga Iye ali woyera.

Aliyense amene amachimwa amaphwanya lamulo; pakuti tchimo ndi kuphwanya lamulo. Koma inu mukudziwa kuti Yesu anabwera kuti adzachotse machimo athu. Ndipo mwa Iye mulibe tchimo. Aliyense wokhala mwa Khristu sachimwa. Aliyense amene amachimwa sanamuone kapena kumudziwa.

Ana okondedwa, musalole kuti aliyense akusocheretseni. Munthu amene amachita chilungamo ndi wolungama, monga Khristu ali wolungama.

Luka 24:36-48

Yesu Aonekera kwa Ophunzira

36 Akufotokoza zimenezi, Yesu mwini wake anayimirira pakati pawo ndipo anati, “Mukhale ndi mtendere.”

37 Koma chifukwa choti anathedwa nzeru ndi kuchita mantha, ankaganiza kuti akuona mzukwa. 38 Iye anawafunsa kuti, “Nʼchifukwa chiyani mukuvutika? Nʼchifukwa chiyani mukukayika mu mtima mwanu? 39 Taonani manja anga ndi mapazi anga. Ine ndine amene! Khudzeni kuti muone. Mzukwa ulibe mnofu ndi mafupa monga mukuonera ndili nazo.”

40 Iye atanena izi anawaonetsa manja ake ndi mapazi ake. 41 Ndipo pamene iwo samakhulupirirabe, chifukwa cha chimwemwe ndi kudabwa, Iye anawafunsa kuti, “Kodi muli ndi chakudya chilichonse pano?” 42 Iwo anamupatsa Iye kachidutswa ka nsomba yophika. 43 Iye anakatenga ndi kukadya iwo akuona.

44 Iye anawawuza kuti, “Izi ndi zimene ndinakuwuzani pamene ndinali nanu: chilichonse chiyenera kukwaniritsidwa chimene chinalembedwa cha Ine mʼbuku la Malamulo a Mose, Aneneri ndi Masalimo.”

45 Kenaka anawatsekula maganizo kuti azindikire Malemba. 46 Iye anawawuza kuti, “Izi ndi zimene zinalembedwa: Khristu adzazunzika ndipo adzauka kwa akufa tsiku lachitatu. 47 Ndipo kutembenuka mtima ndi kukhululukidwa kwa machimo zidzalalikidwa mu dzina lake kwa anthu amitundu yonse kuyambira mu Yerusalemu. 48 Inu ndinu mboni za zimenezi.

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero (CCL)

The Word of God in Contemporary Chichewa Copyright © 2002, 2016 by Biblica, Inc.® Used by permission of Biblica, Inc.® All rights reserved worldwide. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Mwini © 2002, 2016 ndi Biblica, Inc.® Kugwiritsa ntchito mwachilolezo. Umwini ndi otetezedwa pa dziko lonse.